Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinaona Kuti Padzikoli Palibe Chilungamo

Ndinaona Kuti Padzikoli Palibe Chilungamo

NDINABADWA m’chaka cha 1965, ku Northern Ireland ndipo banja lathu linali losauka. Ndinakulira m’chigawo cha Derry, pa nthawi imene m’dzikoli munkachitika nkhondo pakati pa Akatolika ndi Apulotesitanti. Nkhondo imeneyi inachitika kwa zaka zoposa 30. Akatolika ankaona kuti Apulotesitanti, omwe anali ndi mphamvu zambiri m’boma komanso anali ochuluka, ankawapondereza pa nkhani ya zisankho, zachitetezo, kulemba ntchito komanso nkhani za nyumba.

Ndinkaona kuti padzikoli palibe chilungamo. Sindikukumbukira kuti ndi maulendo angati pomwe ndinamenyedwa, kutulutsidwa m’galimoto atandiloza ndi mfuti pamutu, kufunsidwa komanso kufufuzidwa ndi apolisi kapena ndi asilikali. Zimenezi ndinatopa nazo kwambiri moti ndinkaganiza kuti, ‘Kodi ndingowasiya kapena ndiwabwezere?’

Ndinapanga nawo zionetsero zokumbukira anthu 14 amene anaphedwa ndi asilikali a ku Britain mu 1972 komanso zionetsero zokumbukira akaidi amene anafa chifukwa chonyanyala kudya mu 1981. Ndinkanyamula mbendera zoletsedwa ku Northern Ireland komanso ndinkalemba mawu  onyoza boma la Britain paliponse pamene ndafuna. Nthawi zambiri Akatolika ankazunzidwa kapena kuphedwa chifukwa chopanga zionetsero. Kawirikawiri zionetsero zinkayamba ngati zabwinobwino koma zinkathera m’ziwawa.

Ndili ku yunivesite, ine ndi ana asukulu ena tinachita zionetsero zokwiya ndi kuwonongeka kwa zachilengedwe. Kenako ndinasamukira ku London ndipo ndili kumeneko ndinachita nawonso zionetsero zokwiya ndi malamulo a boma omwe ankakondera anthu olemera n’kumapondereza anthu osauka. Komanso ndinachita nawo sitalaka yokwiya ndi kudulidwa kwa malipiro a ogwira ntchito. Kenako mu 1990, ndinachita nawonso zionetsero zokwiya ndi msonkho umene boma linaika kuti aliyense azilipira. Zionetserozo zinachititsa kuti malo otchedwa Trafalgar Square aphwanyidwe kwambiri.

N’kupita kwa nthawi, ndinasokonezeka maganizo chifukwa choona kuti kuchita zionetsero sikunkathandiza chilichonse. M’malo mwake zinkangochititsa kuti ndizidana kwambiri ndi anthu komanso boma.

Ngakhale anthu atakhala ndi zolinga zabwino, sangakwanitse kuchita zinthu mwachilungamo

Imeneyi ndi nthawi imene mnzanga wina anandithandiza kudziwana ndi Mboni za Yehova. Iwo anandiphunzitsa kuchokera m’Baibulo kuti Mulungu adzathetsa mavuto onse ndiponso adzakonza zinthu zonse zimene anthu awononga. (Yesaya 65:17; Chivumbulutso 21:3, 4) Ngakhale anthu atakhala ndi zolinga zabwino, sangakwanitse kuchita zinthu mwachilungamo. Anthufe timafunika malangizo a Mulungu komanso mphamvu zake kuti tilimbane ndi mizimu yoipa imene imachititsa mavuto amene ali padzikoli.—Yeremiya 10:23; Aefeso 6:12.

Ndinazindikira kuti zionetsero zonse zomwe ndinkapanga nawo zinali zopanda phindu lililonse. Ndinasangalala kwambiri kudziwa kuti nthawi ina padzikoli, anthu onse azidzachitirana zinthu mwachilungamo chifukwa palibe munthu amene adzapose mnzake.

Baibulo limanena kuti Yehova ndi Mulungu amene “amakonda chilungamo.” (Salimo 37:28) Chimenechi ndi chifukwa chimodzi chimene chimatitsimikizira kuti ufumu wake udzakhala wachilungamo, zimene maboma onse a anthu sangakwanitse. (Danieli 2:44) Ngati mukufuna kudziwa zambiri, funsani wa Mboni za Yehova aliyense m’dera lanu kapena pitani pa webusaiti yathu ya www.pr418.com.