Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mphaka Wam’tchire Wakuchipululu

Mphaka Wam’tchire Wakuchipululu

Pakadutsa miyezi iwiri ali ndi bere, mphakayu amatha kuswa ana atatu

TAYEREKEZANI kuti ndi usiku ndipo muli kudera lachipululu. Kenako mukuona mphaka wa m’tchire akutuluka kuphanga n’kuima. Mphakayo akuyang’ana uku ndi uku ataimika makutu. Ndiyeno akuyamba kuyenda monyang’ama mu mchenga.

Mwadzidzidzi mphaka uja akudumpha n’kumbwandira mbewa. Zimenezi ndi zimene mphaka wa m’tchire wa kuchipululu amakonda kuchita. Mphakayu amasaka mbewa usiku wonse. Akakhuta amatenga mbewa zotsala n’kuzikwirira mu mchenga. Akatero amabwerera kuphanga kwake mam’mawa kwambiri ndipo saoneka masana onse. Onani zina zokhudza mphaka ameneyu.

  • Chifukwa chakuti mphakayu amamva kwambiri, amatha kudziwa kumene kuli nyama imene akufuna kuigwira ngakhale itakhala kuuna pansi pa nthaka

  • Mphaka wamphongo akafuna mphaka wamkazi, amalira mwabesi. Mphaka wamkazi amatha kumva kulira kumeneku ngakhale atakhala kutali kwambiri

  • Ubweya umene umakhala kuphazi kwa mphakayu umathandiza kuti mwendo wake usamalowe kwambiri mumchenga komanso umathandiza kuti asapse ndi kutentha kwa mchenga

  •  Mkati mwa makutu ake muli ubweya woyera womwe umateteza kuti musalowe mchenga womwe ukuwuluka

  • Nthawi zambiri zimavuta kudziwa pamene mphakayu wadutsa chifukwa ubweya umene uli kuphazi kwa mphakayu umafufuta zidindo za mapazi ake

  • Mphakayu safuna madzi ambiri, moti amatha kukhala nthawi yaitali asanamwe madzi. Amangodalira madzi a m’nyama imene wadya

  • Mchenga wa m’chipululu cha Kara-Kum umatentha kufika madigiri 80. Koma nthawi zina kumazizira kwambiri kufika madigiri -25