Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Switzerland

Kafukufuku wina amene anachitika ku Switzerland anasonyeza kuti anthu ambiri a zaka zoposa 60 akhoza kufa patsiku lawo limene anabadwa poyerekeza ndi masiku ena. Kafukufukuyu anasonyeza kuti anthu ambiri amadwala matenda a mtima patsiku limene anabadwa. Akazi amadwala matenda ofa ziwalo ndipo amuna ambiri amadzipha. Asayansi akukhulupirira kuti nkhawa komanso kuledzera ndi zimene zimachititsa kwambiri ngozi komanso kuti anthu azidzipha. Koma akatswiri ena amatsutsa zimenezi ponena kuti madokotala ambiri amatha kulakwitsa polemba deti limene munthuyo anabadwa komanso limene anamwalira.

Israel

Akatswiri ena ofufuza a ku Israel apeza kuti amuna ooneka bwino ndi omwe akumaitanidwa ku intavyu, akaika chithunzi chawo pakalata yofunsira ntchito, kuposa akazi okongola. N’chifukwa chiyani zili choncho? Iwo akukhulupirira kuti zimenezi zikuchitika chifukwa m’makampani ambiri akazi ndi amene amachititsa intavyu anthu ofunsira ntchito. Magazini ya The Economist inanena kuti: “N’zomvetsa chisoni kuti akazi ena ali ndi moyo wachikale womachitira nsanje akazi anzawo omwe akufuna ntchito.”

United States

Anthu atatu olimbikitsa ufulu, sisitere wa zaka 82 ndi azibambo awiri, wina wa zaka 63 ndipo winayo wa zaka 57, analowa pamalo oletsedwa osungirako zinthu zopangira zida za nkhondo zoopsa kwambiri. Malowa ali ku Oak Ridge, ku Tennessee ndipo amasungirako matani 100 a zinthu zopangira zida zoopsa. Anthuwa atalowa anapenta khoma lamalowo mawu osonyeza kuti amadana ndi nkhondo. Mkulu wa dipatimenti yoona za mphamvu zamagetsi a m’mafakitale, dzina lake Steven Chu, ananena kuti: “Zimene anthuwa anachita n’zosayenera komanso zomvetsa chisoni chifukwa malowa ndi amodzi mwa malo otetezedwa kwambiri padziko lonse.” Iye akukhulupirira kuti zimene zinachititsa kuti anthuwa afike pamalowa ndi kuchepa kwa chitetezo.

Australia

Khoti lalikulu m’dziko la Australia likufuna kuti makampani opanga fodya asamaike fodya m’mapaketi okongola komanso okopa anthu. Khotili likufuna kuti makampaniwa aziika ndudu m’mapaketi osalemba chilichonse koma pazikhala zithunzi zosonyeza kuipa kosuta fodya.