Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 30

“Pitirizani Kusonyeza Chikondi”

“Pitirizani Kusonyeza Chikondi”

1-3. Kodi chimachitika n’chiyani tikamatsanzira Yehova pa nkhani yosonyeza ena chikondi?

 “KUPATSA kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Mawu a Yesuwa, amatiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri iyi: Tikamasonyeza chikondi chenicheni, zotsatira zake zimakhala zabwino. Ngakhale kuti timasangalala ena akamatikonda, koma timasangalala kwambiri ifeyo tikamasonyeza ena chikondi.

2 Palibe amene amadziwa bwino mfundo imeneyi kuposa Atate wathu wakumwamba. Monga taonera m’mitu yapitayi ya gawo lino, chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi, ndi Yehova. Palibe amene wasonyezapo chikondi kwambiri kapenanso kwa nthawi yaitali kuposa iyeyo. Choncho n’zosadabwitsa kuti Yehova akutchulidwa kuti “Mulungu wachimwemwe”​—1 Timoteyo 1:11.

3 Mulungu wathu wachikondi amafuna tiziyesetsa kumutsanzira, makamaka pa nkhani yosonyeza chikondi. Lemba la Aefeso 5:1, 2 limati: “Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa, ndipo pitirizani kusonyeza chikondi.” Tikamatsanzira Yehova pa nkhani yosonyeza chikondi, timasangalala kwambiri chifukwa kumeneku n’kupatsa. Timasangalalanso podziwa kuti tikusangalatsa Yehova, chifukwa Mawu ake amatiuza kuti tiyenera “kukondana.” (Aroma 13:8) Komabe palinso zifukwa zina zotichititsa kuti ‘tipitirize kusonyeza chikondi.’

Chikondi N’chofunika Kwambiri

Chikondi chimatichititsa kuti tizikhulupirira abale athu

4, 5. N’chifukwa chiyani n’zofunika kwambiri kuti tizisonyeza Akhristu anzathu chikondi chololera kuvutikira ena?

4 N’zofunika kwambiri kuti tizikonda Akhristu anzathu. N’chifukwa chiyani tikutero? Mwachidule, chifukwa chakuti chikondi ndi khalidwe lofunika kwambiri kwa Akhristu oona. Popanda chikondi sitingagwirizane kwambiri ndi Akhristu anzathu komanso Yehova sangatigwiritse ntchito. Tiyeni tione zimene Mawu a Mulungu amanena pa nkhaniyi.

5 Pa usiku womaliza wa moyo wake padzikoli, Yesu anauza otsatira ake kuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mofanana ndi mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana choncho. Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga ngati mukukondana.” (Yohane 13:34, 35) Ponena kuti “mofanana ndi mmene ine ndakukonderani,” Yesu akutilamula kuti tizisonyeza chikondi chofanana ndi chimene iye anasonyeza. M’Mutu 29 tinaona kuti Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. Nafenso tiyenera kukhala ndi chikondi chimenechi ndipo tiyenera kuchisonyeza m’njira yoti anthu amene satumikira Yehova azitha kuona kuti timakondanadi. Ndithudi, chikondi chololera kuvutikira ena ndi chizindikiro chathu monga otsatira enieni a Khristu.

6, 7. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Baibulo limatsindika kufunika kokhala ndi chikondi? (b) Kodi mawu a Paulo a pa 1 Akorinto 13:4-8 akunena za chikondi chiti?

6 Nanga bwanji ngati tilibe chikondi? Mtumwi Paulo ananena kuti: “Ngati . . . ndilibe chikondi, ndili ngati belu longolira kapena chinganga chosokosera.” (1 Akorinto 13:1) Ziwiri zonsezi, chinganga komanso belu longolira, zimasokosa kwambiri. Chimenechi ndi chitsanzo choyenera. Munthu wopanda chikondi amafanana ndi chida choimbira chimene chimasokosera ndipo sichisangalatsa. Munthu wotereyu sangakhale ndi anzake apamtima. Paulo ananenanso kuti: “Ngati . . . ndili ndi chikhulupiriro cholimba moti ndingathe kusuntha mapiri, koma ndilibe chikondi, zomwe ndimachita zilibe ntchito.” (1 Akorinto 13:2) Tangoganizani, zinthu zonse zimene munthu wopanda chikondi amachita n’zopanda ntchito. Ndiyetu m’pake kuti Baibulo limati tizikhala anthu achikondi.

7 Komabe, kodi tingasonyeze bwanji chikondi tikamachita zinthu ndi anthu? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tikambirane zimene Paulo ananena pa 1 Akorinto 13:4-8. Mavesiwa sakunena za chikondi chimene Mulungu amatisonyeza kapenanso chikondi chimene timamusonyeza. Koma akunena za chikondi chimene timasonyeza anthu ena. Paulo anafotokoza zimene chikondi chimachita ndiponso zimene sichichita.

Zimene Chikondi Chimachita

8. Kodi kuleza mtima kungatithandize bwanji tikamachita zinthu ndi ena?

8 “Chikondi nʼcholeza mtima.” Munthu wachikondi amakhala wololera ndipo amachita zimenezo moleza mtima. (Akolose 3:13) Mwina mungavomereze kuti timafunikadi kukhala oleza mtima. Popeza ifeyo komanso Akhristu anzathu si ife angwiro ndipo timatumikira limodzi, timadziwa kuti nthawi zina tikhoza kulakwirana kapena kukhumudwitsana. Koma ngati ndife oleza mtima ndiponso ololera, tingathe kupirira zokhumudwitsa zing’onozing’ono zimene zingakhalepo tikamachita zinthu ndi ena, ndipo sitingasokoneze mtendere mumpingo.

9. Kodi tingasonyeze kukoma mtima m’njira ziti?

9 “Chikondi . . . nʼchokoma mtima.” Timasonyeza kuti ndife okoma mtima pochita zinthu zothandiza ena komanso polankhula mawu osonyeza kuti timawaganizira. Chikondi chimachititsa kuti tizifufuza njira zoti tisonyeze ena kukoma mtima, makamaka amene akufunika kuwathandiza. Mwachitsanzo, Mkhristu wachikulire angamasowe wocheza naye ndipo angafunike kumulimbikitsa. Mayi yemwe akulera yekha ana kapena mlongo amene mwamuna wake si Mboni angafunike kumuthandiza zinthu zina. Munthu amene akudwala kapena amene akukumana ndi mavuto enaake angafune kumva mawu abwino ochokera kwa mnzake wokhulupirika. (Miyambo 12:25; 17:17) Tikamayamba ndife kusonyeza kukoma mtima m’njira ngati zimenezi, timasonyeza kuti ndifedi achikondi.​—2 Akorinto 8:8.

10. Kodi chikondi chimatithandiza bwanji kukhala kumbali ya choonadi komanso kulankhula zoona ngakhale pamene kuchita zimenezo kuli kovuta?

10 “Chikondi . . . chimasangalala ndi choonadi.” Baibulo lina limati: “Chikondi . . . chimasangalala kukhala kumbali ya choonadi.” Chikondi chimatichititsa kuti tizikhala kumbali ya choonadi ‘n’kumauzana zoona.’ (Zekariya 8:16) Mwachitsanzo, ngati munthu yemwe timamukonda wachita tchimo lalikulu, kukonda Yehova ndiponso wolakwayo kudzatithandiza kutsatira mfundo za Yehova m’malo moyesa kubisa tchimolo, kulichepetsa kapena kunena zabodza. N’zoona kuti zingakhale zovuta kuvomereza zomwe zachitikazo. Koma ngati timafunira zabwino munthuyo, tidzafuna kuti alandire chilango chochokera kwa Mulungu, womwe ndi umboni woti amamukonda. (Miyambo 3:11, 12) Komanso popeza ndife Akhristu, timafuna “kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—Aheberi 13:18.

11. Popeza chikondi ‘chimakwirira zinthu zonse,’ kodi tiyenera kutani ndi zimene Akhristu anzathu amalakwitsa?

11 “Chikondi . . . chimakwirira zinthu zonse.” Baibulo lina limati chikondi “chimaphimba zinthu zonse.” (Kingdom Interlinear) Lemba la 1 Petulo 4:8 limati: “Chikondi chimakwirira machimo ochuluka.” Kunena zoona, Mkhristu wachikondi sakonda kulankhula zimene Akhristu anzake amalakwitsa n’cholinga choti ena azidziwe. Nthawi zambiri, zolakwa za Akhristu anzathu zimakhala zazing’ono moti tikhoza kungozikwirira kapena kuziphimba ndi chikondi.​—Miyambo 10:12; 17:9.

12. Kodi mtumwi Paulo anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira kuti Filimoni achita zabwino, nanga tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Paulo?

12 “Chikondi . . . chimakhulupirira zinthu zonse.” Baibulo limene anamasulira Moffatt limati chikondi “nthawi zonse chimafunitsitsa kukhulupirira zabwino kwambiri.” Timayesetsa kukhulupirira Akhristu anzathu ndipo timapewa kukayikira zolinga zawo popanda zifukwa zomveka. Chikondi chimatithandiza kuti tisamakayikire abale athu ndipo timakhulupirira kuti amachita “zabwino kwambiri.” a Timaona chitsanzo cha zimenezi m’kalata imene Paulo analembera Filimoni. Paulo analemba kalatayi pofuna kulimbikitsa Filimoni kuti amulandire bwino kapolo wake Onesimo amene anathawa, yemwe pa nthawiyi anali Mkhristu. Iye sanakakamize Filimoni kuti achite zimenezi, koma anamupempha mwachikondi. Ankakhulupirira kuti Filimoni achita zoyenera. Ananena kuti: “Ndikukulembera zimenezi chifukwa ndikukhulupirira kuti uzichitadi. Ndikudziwanso kuti uchita ngakhale zoposa zimene ndanenazi.” (Vesi 21) Tikamakhulupirira abale athu chifukwa chowakonda, zimawathandiza kuti azichita zinthu zabwino.

13. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayembekezera zabwino kwa abale athu?

13 “Chikondi . . . chimayembekezera zinthu zonse.” Monga mmene zilili kuti munthu wachikondi amakhulupirira kuti ena achita zabwino, iye amayembekezeranso zabwino. Chikondi chimatichititsa kuti tiziyembekezera kuti abale athu achita zabwino. Mwachitsanzo, ngati m’bale “wapatuka nʼkuyamba kulowera njira yolakwika mosazindikira,” timakhulupirira kuti atsatira malangizo achikondi omwe angapatsidwe. (Agalatiya 6:1) Timakhulupiriranso kuti anthu amene afooka ayambiranso kutumikira Yehova mwakhama. Timawalezera mtima ndipo timachita zonse zomwe tingathe powathandiza kuti akhalenso ndi chikhulupiriro cholimba. (Aroma 15:1; 1 Atesalonika 5:14) Munthu amene timamukonda akasiya choonadi, sititaya mtima ndipo timakhulupirira kuti tsiku lina nzeru zidzamubwerera ndipo adzabwerera kwa Yehova ngati mwana wolowerera wa m’fanizo la Yesu uja.​—Luka 15:17, 18.

14. Kodi nthawi zina tingafunike kupirira mayesero ati mumpingo, nanga chikondi chingatithandize bwanji?

14 “Chikondi . . . chimapirira zinthu zonse.” Kupirira kumatithandiza kukhalabe olimba tikakumana ndi zokhumudwitsa kapena mavuto. Sikuti mayesero amachokera kwa anthu osalambira Yehova okha. Nthawi zina amachokera kwa abale ndi alongo athu. Popeza anthufe si angwiro, nthawi zina abale athu angatikhumudwitse. Mwina angalankhule mawu olasa ngati lupanga. (Miyambo 12:18) Mwinanso tingaone kuti nkhani ina mumpingo sinasamaliridwe ngati mmene ifeyo timaganizira. Kapena zochita za m’bale wina amene anthu amamulemekeza zingatikhumudwitse ndipo tingamadzifunse kuti, ‘Mkhristu angachitirenji zimenezi?’ Tikakumana ndi zinthu ngati zimenezi, kodi tidzachoka mumpingo n’kusiya kutumikira Yehova? Ngati tili ndi chikondi sitingachite zimenezo. Chikondi chimatithandiza kuti tisamangoona zimene Mkhristu wina amalakwitsa n’kulephera kuona zabwino zomwe iyeyo kapena abale ndi alongo athu amachita. Chifukwa cha chikondi, timakhalabe okhulupirika kwa Mulungu n’kumathandiza mpingo, kaya m’bale kapena mlongo wina wachita kapena kulankhula zotani.​—Salimo 119:165.

Zimene Chikondi Sichichita

15. Kodi munthu wansanje amatani, nanga chikondi chimatithandiza bwanji kupewa khalidwe loipali?

15 “Chikondi sichichita nsanje.” Sitiyenera kuchitira ena nsanje chifukwa choti ali ndi katundu, luso linalake kapena chifukwa cha madalitso amene alandira. Munthu wansanje amakhala wodzikonda ndipo nsanje imabweretsa mavuto kwa iyeyo ndiponso anthu ena. Ngati munthu wotereyu sangasinthe, akhoza kusokoneza mtendere mumpingo. Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kupewa mtima wansanje? (Yakobo 4:5) Chikondi. Khalidwe lofunika kwambiri limeneli lingatithandize kuti tizisangalala ndi amene akuoneka kuti ali ndi zinthu zina zabwino zomwe ife tilibe. (Aroma 12:15) Chikondi chimatithandizanso kuti tisakhumudwe ngati wina watamandidwa chifukwa cha luso lake lapadera kapena chifukwa cha zimene wakwanitsa kuchita.

16. Ngati timakondadi abale athu, n’chifukwa chiyani timapewa kudzitama chifukwa cha zimene tikuchita m’gulu la Yehova?

16 “Chikondi . . . sichidzitama, sichidzikuza.” Chikondi chimatichititsa kuti tisamadzitame chifukwa cha maluso athu kapena zinthu zimene takwanitsa kuchita. Ngati timakondadi abale athu, kodi pali chifukwa choti tizidzitama chifukwa cha udindo wathu mumpingo kapena zinthu zikatiyendera bwino mu utumiki? Zimenezo zingafooketse ena ndipo angamadzione kuti ndi opanda pake poyerekezera ndi ifeyo. Ngati tili ndi chikondi sitingamadzitame chifukwa cha zimene Mulungu watilola kuchita m’gulu lake. (1 Akorinto 3:5-9) Ndipotu chikondi “sichidzikuza,” kapena mogwirizana ndi Baibulo lina, “sichisangalala ndi maganizo odzimva chifukwa choona kuti ndiwe wofunika.” (The New Testament in Modern English) Choncho chikondi chimatichititsa kuti tisamadzione kuti ndife apamwamba kuposa ena.​—Aroma 12:3.

17. Ngati tili ndi chikondi, kodi timachita chiyani, nanga timapewa zinthu ziti?

17 “Chikondi . . . sichichita zosayenera.” Munthu amene amachita zosayenera amachita zinthu zochititsa manyazi komanso zosonyeza kupanda ulemu. Kuchita zimenezi ndi kupanda chikondi chifukwa zimasonyeza kuti munthuyo saganizira ena. Mosiyana ndi zimenezi, chikondi chimathandiza kuti tizikhala okoma mtima kwa ena komanso kuwasonyeza kuti timawaganizira. Chikondi chimatichititsa kuti tizisonyeza makhalidwe abwino, tizichita zinthu zimene Yehova amasangalala nazo komanso tizilemekeza Akhristu anzathu. Ngati tili ndi chikondi, tidzapewa khalidwe lililonse lochititsa manyazi, lomwe lingakhumudwitse kwambiri Akhristu anzathu.​—Aefeso 5:3, 4.

18. N’chifukwa chiyani munthu wachikondi sakakamira kuti chilichonse chizichitika mmene iye akufunira?

18 “Chikondi . . . sichisamala zofuna zake zokha.” Baibulo lina limati: “Chikondi sichiumirira maganizo ake.” (Revised Standard Version) Munthu wachikondi sakakamira kuti chilichonse chizichitika mmene iye akufunira, ngati kuti nthawi zonse maganizo ake ndi amene amakhala olondola. Sakakamiza ena omwe ali ndi maganizo osiyana ndi ake kuti agwirizane ndi maganizo ake komanso kuti achite zinthu mmene iye akufunira. Ngati atamachita zimenezo, angasonyeze kuti ndi wonyada ndipo Baibulo limati: “Kunyada kumachititsa kuti munthu awonongeke.” (Miyambo 16:18) Ngati timakondadi abale athu, timalemekeza maganizo awo ndipo timakhala ololera ngati pakufunika kutero. Kukhala ololera n’kogwirizana ndi mawu a Paulo akuti: “Aliyense asamangofuna zopindulitsa iyeyo basi, koma zopindulitsanso ena.”​—1 Akorinto 10:24.

19. Kodi chikondi chimatithandiza kuchita chiyani ena akatilakwira?

19 “Chikondi . . . sichikwiya ndipo sichisunga zifukwa.” Munthu wachikondi safulumira kupsa mtima ndi zimene ena anena kapena kuchita. N’zoona kuti mwachibadwa anthu ena akatichitira zoipa, timakhumudwa. Koma ngakhale titakwiya pa zifukwa zomveka, chikondi chimatithandiza kuti tisapitirize kukhala okwiya. (Aefeso 4:26, 27) Sitisunga zinthu zoipa zimene ena anatinenera kapena kutichitira ngati kuti tinazilemba m’buku kuti tisaziiwale. Chikondi chimatichititsa kuti tizitsanzira Mulungu wathu. Monga tinaonera m’Mutu 26, Yehova amatikhululukira pakakhala zifukwa zomveka. Akatero amaiwala, kutanthauza kuti pa nthawi ina m’tsogolo satiimbanso mlandu chifukwa cha machimo omwe anatikhululukirawo. Timathokozatu kwambiri kuti Yehova satisungira zifukwa.

20. Kodi tiyenera kutani Mkhristu mnzathu akachita tchimo kenako n’kumavutika ndi zotsatira zake?

20 “Chikondi . . . sichisangalala ndi zosalungama.” Baibulo lina limati: “Chikondi . . . sichinyadira anthu ena akachita machimo.” (New English Bible) Baibulo lomasuliridwa ndi Moffatt limati: “Chikondi sichisangalala ena akalakwitsa.” Munthu wachikondi sasangalala ndi zosalungama, choncho pakachitika khalidwe loipa lililonse sitisangalala. Ndiye kodi timatani Mkhristu mnzathu akachita tchimo kenako n’kumavutika ndi zotsatira zake? Ngati ndife achikondi sitingasangalale chifukwa zingakhale ngati tikunena kuti, ‘Zakhala bwino! Akhaule.’ (Miyambo 17:5) Koma timasangalala m’bale yemwe wachita tchimo akayamba kuchita zoyenera kuti akonzenso ubwenzi wake ndi Yehova.

“Njira Yopambana”

21-23. (a) Kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti “chikondi sichitha?” (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’mutu womaliza?

21 “Chikondi sichitha.” Kodi Paulo ankatanthauza chiyani ponena mawu amenewa? Tikawerenga nkhani yonse, zikuoneka kuti ankafotokoza zokhudza mphatso za mzimu zimene Akhristu oyambirira anali nazo. Mphatso zimenezo zinali chizindikiro chosonyeza kuti Yehova wayamba kugwiritsa ntchito mpingo wa Chikhristu womwe unali utangokhazikitsidwa kumene. Koma si Akhristu onse omwe ankachiritsa odwala, kulosera kapena kulankhula malilime. Komabe imeneyi sinali nkhani yofunika kwambiri, chifukwa mphatso zochita zodabwitsa zinali zoti pakapita nthawi zidzatha. Koma panali chinthu china choti chidzapitiriza kukhalapo, chomwe Mkhristu aliyense akanatha kuyesetsa kuti akhale nacho. Chinali chapadera kwambiri ndiponso chokhalitsa kuposa mphatso yochita zodabwitsa iliyonse. Ndipotu Paulo anachitchula kuti “njira yopambana.” (1 Akorinto 12:31) Kodi “njira yopambana” imeneyi inali chiyani? Inali njira yachikondi.

22 Zoonadi, chikondi cha Akhristu chimene Paulo anafotokoza “sichitha” ndipo chidzakhalapo mpaka kalekale. Mpaka pano, otsatira oona a Yesu amadziwika kuti amasonyezana chikondi chololera kuvutikira ena. Chikondi chimenechi chimaoneka pakati pa atumiki a Yehova padziko lonse ndipo sichidzatha chifukwa Yehova analonjeza kuti adzapatsa atumiki ake okhulupirika moyo wosatha. (Salimo 37:9-11, 29) Tiyeni tizichita zonse zomwe tingathe kuti ‘tipitirize kusonyeza chikondi.’ Tikamachita zimenezi timasangalala kwambiri chifukwa chokhala wopatsa. Kuwonjezera pamenepo, tidzapitiriza kukhala ndi moyo ndiponso kusonyeza chikondi mpaka kalekale potsanzira Mulungu wathu wachikondi, Yehova.

Anthu a Yehova amadziwika ndi chikondi

23 M’mutuwu, womwe ndi womaliza pa gawo lonena za chikondi, takambirana mmene tingasonyezere ena chikondi. Chikondi cha Yehova chimatithandiza m’njira zambiri. N’chimodzimodzinso ndi mphamvu zake, chilungamo chake komanso nzeru zake. Tikaganizira zimenezi ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingamusonyeze bwanji Yehova kuti ndimamukondadi?’ Tidzakambirana funso limeneli m’mutu womaliza.

a Komabe, ngakhale kuti chikondi “chimakhulupirira zinthu zonse,” sizikutanthauza kuti tizilola anthu ena kutinamiza. Baibulo limatichenjeza kuti: “Musamale ndi amene amagawanitsa anthu ndiponso kuchita zinthu zokhumudwitsa . . . choncho muziwapewa.”​—Aroma 16:17.