Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 2

Kodi Mungatani Kuti Mukhalebe ndi Chikumbumtima Chabwino?

Kodi Mungatani Kuti Mukhalebe ndi Chikumbumtima Chabwino?

“Khalani ndi chikumbumtima chabwino.”—1 PETULO 3:16.

1, 2. Kodi kampasi ndi yofunika bwanji, nanga imafanana bwanji ndi chikumbumtima?

WOYENDETSA sitima yapamadzi akudutsa panyanja yaikulu yamafunde. Munthu wina ali pa ulendo ndipo akudutsa m’chipululu ali yekhayekha. Woyendetsa ndege akuiulutsa m’mwamba kwambiri kupitirira mitambo imene yayala kuchokera kum’mawa mpaka kumadzulo. Anthu atatu onsewa akufanana chinthu chimodzi. Onsewa moyo wawo ungakhale pangozi ngati alibe kampasi, makamakanso ngati alibe zida zina zamakono zomwe zingawathandize pa ulendowo.

2 Kampasi ndi kachipangizo kofanana ndi wotchi yamivi, koma kamakhala ndi muvi umodzi wa maginito umene nthawi zonse umaloza kumpoto. Ngati kampasi ikugwira bwino ntchito komanso ngati ikugwiritsidwa ntchito motsatira mapu olondola, ingathe kupulumutsa moyo. Kampasi ingafanane ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova anatipatsa. Mphatso imeneyi ndi chikumbumtima. (Yakobo 1:17) Popanda chikumbumtima, tingasochere ndipo tingasowe kolowera. Ngati tigwiritsa ntchito bwino chikumbumtima chathu, chingatithandize kudziwa koyenera kupita ndi kupitirizabe kuyenda m’njira yoyenera pa moyo wathu. Kodi chikumbumtima n’chiyani, nanga chimagwira ntchito bwanji? Tiyeni tikambirane zimenezi komanso mafunso otsatirawa: (1) Kodi tingatani kuti tiphunzitse chikumbumtima chathu? (2) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira chikumbumtima cha anthu ena? (3) Kodi chikumbumtima chabwino chili ndi phindu lotani?

KODI CHIKUMBUMTIMA N’CHIYANI, NANGA CHIMAGWIRA NTCHITO BWANJI?

3. Kodi mawu Achigiriki omasuliridwa kuti “chikumbumtima” amatanthauza chiyani kwenikweni, ndipo amanena za luso lapadera lotani limene anthufe tili nalo?

3 M’Baibulo, mawu Achigiriki omasuliridwa kuti “chikumbumtima,” kwenikweni amatanthauza “kudzidziwa tokha.” Mosiyana ndi zolengedwa zina zonse padziko lapansi, anthufe Mulungu anatipatsa luso lotha kudzidziwa tokha. Tingati timatha kudziyang’ana n’kudziweruza kuti tione ngati tili ndi makhalidwe abwino kapena ayi. Pokhala ngati mboni kapena woweruza wamumtima mwathu, chikumbumtima chimatha kuunika zochita, maganizo ndiponso zosankha zathu. Chingatithandize kusankha zinthu mwanzeru kapena kutichenjeza kuti tisasankhe zoipa. Tikasankha mwanzeru, chimatilimbikitsa. Koma tikasankha mopanda nzeru, chimatisowetsa mtendere.

4, 5. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Adamu ndi Hava anali ndi chikumbumtima, ndipo chinachitika n’chiyani iwo ataswa lamulo la Mulungu? (b) Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza kuti chikumbumtima chinkagwira ntchito mwa anthu okhulupirika akale?

4 Kuchokera pa chiyambi, mwamuna ndi mkazi woyamba analengedwa ndi luso limeneli. Adamu ndi Hava anasonyeza kuti anali ndi chikumbumtima. Umboni wa zimenezi ndi wakuti atachimwa, anachita manyazi. (Genesis 3:7, 8) Koma n’zomvetsa chisoni kuti pa nthawiyi, chikumbumtima chawo sichikanatha kuwathandiza ngakhale kuti chinkawasowetsa mtendere. Iwo anali ataswa lamulo la Mulungu mwadala. Choncho, iwo anachita kusankha okha kukhala oukira komanso kukhala adani a Yehova Mulungu. Popeza kuti anali anthu angwiro, iwo ankadziwa chimene ankachita, ndipo sizikanatheka kuti abwererenso kwa Mulungu.

5 Mosiyana ndi Adamu ndi Hava, anthu ambiri opanda ungwiro amvera chikumbumtima chawo. Mwachitsanzo, munthu wokhulupirika Yobu anati: “Ndagwira chilungamo changa ndipo sindichitaya. Mtima wanga sudzandinyoza masiku anga onse.” * (Yobu 27:6) Yobu ankayesetsa kumvera chikumbumtima chake, ndipo ankachilola kuti chimutsogolere pa zochita ndi zosankha zake. N’chifukwa chake iye anatha kunena mochokera pansi pa mtima kuti chikumbumtima chake sichinkamutsutsa, kapena kumusowetsa mtendere, pomuchititsa manyazi ndi kumuimba mlandu. Mosiyana ndi Yobu, chikumbumtima cha Davide chinamusowetsa mtendere. Pa nthawi ina Davide sanasonyeze ulemu kwa Sauli, yemwe anali mfumu yodzozedwa ndi Yehova. “Pambuyo pake, Davide anavutika mumtima mwake.” (1 Samueli 24:5) Kuvutika ndi chikumbumtima kunamuthandiza, ndipo iye anaphunzira kusachitiranso chipongwe mfumu.

6. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti anthu onse ali ndi mphatso ya chikumbumtima?

6 Kodi ndi atumiki a Yehova okha amene ali ndi mphatso ya chikumbumtima imeneyi? Taganizirani mawu ouziridwa a mtumwi Paulo awa: “Nthawi zonse anthu a mitundu amene alibe chilamulo akamachita mwachibadwa zinthu za m’chilamulo, amakhala chilamulo kwa iwo eni ngakhale kuti alibe chilamulo. Amenewa ndiwo amasonyeza kuti mfundo za m’chilamulo zinalembedwa m’mitima mwawo, pamene chikumbumtima chawo chimachitira umboni pamodzi ndi iwowo, ndipo maganizo awo amawatsutsa ngakhalenso kuwavomereza.” (Aroma 2:14, 15) Ngakhale anthu amene sadziwa malamulo a Yehova m’pang’ono pomwe, nthawi zina mboni yamumtima imeneyi ingawalimbikitse kuchita zinthu zogwirizana ndi mfundo za Mulungu.

7. Kodi n’chifukwa chiyani chikumbumtima chingatisocheretse nthawi zina?

7 Koma nthawi zina chikumbumtima chingatisocheretse. N’chifukwa chiyani tikutero? Tiyeni tiganizirenso chitsanzo cha kampasi ija. Ngati kampasi itayandikana ndi chitsulo, ingasokonezeke ndipo muvi wake ungasiye kuloza kumpoto, n’kuloza kumene kuli chitsuloko. Komanso kampasi singathandize kwenikweni ngati igwiritsidwa ntchito popanda mapu olondola. Mofanana ndi zimenezi, ngati chikumbumtima chathu chitsatira kwambiri zolakalaka zadyera za mtima wathu, chingatilozere kolakwika. Komanso ngati tichigwiritsa ntchito popanda kutsogoleredwa ndi Mawu a Mulungu, sitingathe kusiyanitsa chabwino ndi choipa pa nkhani zofunika kwambiri. Choncho, kuti chikumbumtima chathu chizigwira ntchito bwino, tiyenera kutsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Yehova. Paulo analemba kuti: “Ine pamodzi ndi chikumbumtima changa tikuchitira umboni mwa mzimu woyera.” (Aroma 9:1) Koma kodi tingatani kuti chikumbumtima chathu chizigwira ntchito motsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Yehova? Tiyenera kuchiphunzitsa bwino.

MMENE TINGAPHUNZITSIRE CHIKUMBUMTIMA CHATHU

8. (a) Kodi mtima ungasokoneze bwanji chikumbumtima, nanga kodi chofunika kuchiganizira kwambiri posankha zochita n’chiyani? (b) Kodi n’chifukwa chiyani Mkhristu sayenera kuganiza kuti zili bwino potengera kuti chikumbumtima chake sichikumutsutsa? (Onani mawu a m’munsi.)

8 Kodi mungasankhe bwanji zochita pogwiritsa ntchito chikumbumtima chanu? Zikuoneka kuti anthu ena akafuna kusankha zochita, amangoganizira zimene mtima wawo ukufuna basi. Kenako iwo amati, “Zili bwino, chifukwa chikumbumtima changa sichikunditsutsa.” Koma mtima wathu umakakamira kwambiri zimene ukufuna moti umasokoneza chikumbumtima. Baibulo limati: “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa. Ndani angaudziwe?” (Yeremiya 17:9) Choncho, tisamasankhe zochita pongoganizira zofuna za mtima wathu. Chofunika kwambiri n’choti tiziyamba taganizira kaye zimene Yehova Mulungu angakondwere nazo. *

9. Kodi kuopa Mulungu kumatanthauza chiyani, nanga kodi mantha amenewa angatithandize kukhala ndi chikumbumtima chotani?

9 Ngati posankha zochita titsatiradi chikumbumtima chathu chophunzitsidwa bwino, zidzasonyeza kuti timaopa Mulungu komanso kuti sitiyendera zofuna za mtima wathu. Chitsanzo pa nkhani imeneyi ndi kazembe wokhulupirika Nehemiya. Monga kazembe, iye anali ndi ufulu wolamula anthu a ku Yerusalemu kumupatsa malipiro ake ndi ndalama za misonkho yosiyanasiyana. Koma iye sanatero. Kodi n’chifukwa chiyani? Iye sankafuna ngakhale pang’ono kuchita zinthu zimene Yehova sakanakondwera nazo, monga kupondereza anthu a Mulunguwo. Iye anati: “Sindinachite zimenezo chifukwa choopa Mulungu.” (Nehemiya 5:15) Kuopadi Mulungu n’kofunika kwambiri. Mantha amenewa amatanthauza kukhala ndi mtima waulemu woopa kuchita zinthu zimene Atate wathu wakumwamba sasangalala nazo. Ngati tili ndi mantha aulemu amenewa, tidzafuna kutsogoleredwa ndi Mawu a Mulungu posankha zochita.

10, 11. Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zimakhudza nkhani ya kumwa mowa, nanga tingatani kuti Mulungu atitsogolere pofuna kuzigwiritsa ntchito?

10 Mwachitsanzo, taganizirani nkhani ya mowa. Tonsefe tikamapita kokacheza, timafunikira kusankha kukamwa kapena kusakamwa mowa. Tisanapite, choyamba tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndi mfundo ziti za m’Baibulo zimene zimakhudza nkhaniyi?’ Baibulo sililetsa kumwa mowa pang’ono. Ndipo limatamanda Yehova chifukwa chopereka mphatso ya vinyo. (Salimo 104:14, 15) Komabe, Baibulo limaletsa kumwa kwambiri ndiponso maphwando aphokoso a anthu oledzera. (Luka 21:34; Aroma 13:13) Limatchulanso uchidakwa limodzi ndi machimo ena aakulu, monga dama ndi chigololo. *1 Akorinto 6:9, 10.

11 Mfundo ngati zimenezi zimaphunzitsa ndi kupatsa mphamvu chikumbumtima cha Mkhristu. Choncho tikasankha kuti tikamwe kapena tisakamwe mowa kuphwando, tiyenera kudzifunsa mafunso ngati awa: ‘Kodi phwando limene akukonzalo likakhala lotani? Kodi zinthu zingakasokonekere kumeneko n’kukhala phwando laphokoso la anthu oledzera? Kodi ineyo ndimamwa mowa kufika pati? Kodi ndimalakalaka kwambiri mowa? Kodi sinditha kuchita zinthu zina popanda kumwa mowa? Kodi ndimamwa mowa pofuna kuiwala mavuto? Kodi ndimatha kudziletsa kuti ndisamwe mopitirira malire?’ Tikamaganizira mfundo za m’Baibulo komanso mafunso amene tingakhale nawo chifukwa choganizira mfundozo, tingachite bwino kupemphera kuti Yehova atitsogolere. (Werengani Salimo 139:23, 24.) Tikamachita zimenezi, ndiye kuti tikupempha Yehova kuti atitsogolere ndi mzimu wake woyera. Komanso timakhala tikuphunzitsa chikumbumtima chathu kuti chizitsatira mfundo za Mulungu. Komabe, palinso mfundo ina yofunika kwambiri kuiganizira tikamasankha zochita.

KODI N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUGANIZIRA CHIKUMBUMTIMA CHA ENA?

Chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo chingakuthandizeni kusankha kumwa kapena kusamwa mowa

12, 13. Kodi zifukwa zina zimene zimachititsa kuti chikumbumtima cha Akhristu chizikhala chosiyanasiyana ndi ziti, ndipo tingatani ngati chikumbumtima chathu chikusiyana ndi cha ena?

12 Nthawi zina mungadabwe kuona kuti chikumbumtima cha Akhristu chimakhala chosiyanasiyana. Mkhristu wina angaone kuti si koyenera kuchita zinthu zina, pamene wina angathe kusangalala ndi zomwezo ndipo angaone kuti palibe chifukwa choletsera zimenezo. Mwachitsanzo, pa nkhani ya kumwa mowa, wina angasangalale kumwa mowa limodzi ndi anzake angapo pocheza madzulo, pamene wina chikumbumtima chake sichingamulole kuchita zimenezi. Kodi n’chifukwa chiyani chikumbumtima chimasiyana chonchi, nanga kodi kusiyana kumeneku kuyenera kukhudza bwanji zosankha zathu?

13 Pali zifukwa zambiri zimene zimachititsa kuti anthu akhale osiyana. Nthawi zina, chifukwa cha mmene tinakulira timasiyana mmene timaonera zinthu pa nkhani inayake. Mwachitsanzo, ena amadziwa bwino vuto limene akhala akulimbana nalo m’mbuyomo, ndipo mwina zinkawavuta kwambiri kulithetsa. (1 Mafumu 8:38, 39) Choncho, ngati vuto lawo linali mowa, anthu otero sangaufunenso ngakhale pang’ono. Ndiye munthu ngati ameneyu atabwera kudzacheza kunyumba kwanu, angakane mutamupatsa mowa, chifukwa cha chikumbumtima chake. Kodi inuyo muyenera kukhumudwa ndi zimenezi? Kapena kodi muyenera kumukakamiza? Ayi. Mwina iye sangafune kukuuzani zifukwa zimene akukanira. Komabe, kaya mukudziwa kapena simukudziwa zifukwa zake, chikondi chidzakuthandizani kumuganizira mnzanuyo.

14, 15. Kodi chikumbumtima cha Akhristu akale chinasiyana pa nkhani yotani, ndipo Paulo anawalimbikitsa kuchita chiyani?

14 Mtumwi Paulo anaona kuti chikumbumtima cha Akhristu chinkasiyana kwambiri pa zinthu zina. Mwachitsanzo, kalelo Akhristu ena chikumbumtima chawo sichinkawalola kudya zakudya zimene zinali zitaperekedwa nsembe kwa mafano. (1 Akorinto 10:25) Koma chikumbumtima cha Paulo sichinamuletse kudya zakudya ngati zimenezi, zomwe zinkagulitsidwa m’misika pambuyo poti zaperekedwa nsembe. Kwa iye mafano analibe ntchito, ndipo mafanowo si amene anapanga chakudyacho koma Yehova. Choncho chakudyacho chinali cha Yehova. Ngakhale zinali choncho, Paulo anawamvetsa anthu ena amene ankaganiza mosiyana ndi iyeyo pa nkhani imeneyi. N’kutheka kuti ena a iwo kale asanakhale Akhristu, ankapembedza ndi kukhulupirira kwambiri mafano. Choncho, iwo ankaona kuti chilichonse chomwe poyamba ankachigwiritsa ntchito polambira mafano chinali chosayenera. Kodi Paulo anatani ndi nkhani imeneyi?

15 Paulo anati: “Ife olimba tiyenera kunyamula zofooka za osalimba, osati kumadzikondweretsa tokha ayi. Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretse yekha.” (Aroma 15:1, 3) Paulo anaona kuti tiyenera kuika patsogolo zofuna za abale athu, monga mmene anachitira Khristu. Pa nthawi ina, Paulo ananenanso kuti iye anaona kuti ndi bwino kusadya nyama pofuna kupewa kukhumudwitsa nkhosa yamtengo wapatali imene Khristu anaifera.—Werengani 1 Akorinto 8:13; 10:23, 24, 31-33.

16. Kodi n’chifukwa chiyani anthu amene chikumbumtima chawo chimawaletsa kuchita zinthu zina sayenera kuweruza anzawo amene chikumbumtima chawo chimawalola kuchita zinthuzo?

16 Komanso, anthu amene chikumbumtima chawo chimawaletsa zinthu zina, sayenera kuweruza anzawo, n’kumawakakamiza kuti aziona nkhani zofuna chikumbumtima ngati mmene iwowo amaonera. (Werengani Aroma 14:10.) Kunena zoona, tiyenera kugwiritsa ntchito chikumbumtima chathu podziweruza tokha, osati kuweruzira anzathu. Kumbukirani kuti Yesu anati: “Lekani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe.” (Mateyu 7:1) Tonse mumpingo tiyenera kupewa kulimbana pa nkhani zimene aliyense angasankhe malingana ndi chikumbumtima chake. M’malomwake, tiyenera kupeza njira zolimbikitsa chikondi ndi umodzi komanso zolimbikitsira ena, osati zowafooketsa.—Aroma 14:19.

PHINDU LOKHALA NDI CHIKUMBUMTIMA CHABWINO

Chikumbumtima chabwino chingathe kutitsogolera pa ulendo wathu wa ku moyo ndi kutithandiza kukhala ndi chimwemwe ndiponso mtendere wamumtima

17. Kodi n’chiyani chachitikira chikumbumtima cha anthu ambiri masiku ano?

17 Mtumwi Petulo analemba kuti: “Khalani ndi chikumbumtima chabwino.” (1 Petulo 3:16) Tingapeze madalitso aakulu ngati tikutumikira Yehova Mulungu ndi chikumbumtima choyera. Anthu ambiri masiku ano alibe chikumbumtima chotere. Paulo anafotokoza za anthu amenewa kuti, “chikumbumtima chawo chili ngati chipsera chobwera chifukwa chopsa ndi chitsulo chamoto.” (1 Timoteyo 4:2) Chitsulo chamoto chikakhudza pakhungu, pamapseratu ndipo pamatsala chipsera komanso pamafa. Anthu ambiri chikumbumtima chawo ndi chotere, ndipo chili ndi chipsera chachikulu, tingoti chinaferatu, moti sichithanso kuwachenjeza, kuwatsutsa, kuwachititsa manyazi kapena kuwaimba mlandu akachita zoipa. Inde, anthu ambiri masiku ano amanyalanyaza chikumbumtima chawo chikamawaimba mlandu.

18, 19. (a) Kodi kudziimba mlandu kapena kuchita manyazi tikalakwitsa kuli ndi phindu lotani? (b) Kodi tingatani ngati chikumbumtima chathu chikutisowetsabe mtendere pa machimo amene tinachita kale ngakhale kuti tinalapa?

18 Kunena zoona, tikamadziimba mlandu, ndiye kuti chikumbumtima chathu chikutiuza kuti talakwitsa chinachake. Munthu amene wachimwa akamadziimba mlandu, zingamuthandize kulapa ndipo angakhululukidwe ngakhale machimo ake atakhala aakulu kwambiri. Mwachitsanzo, Mfumu Davide anachita machimo aakulu koma anakhululukidwa, makamaka chifukwa chakuti analapa moona mtima. Iye ananyansidwa ndi machimo akewo ndipo anatsimikiza kuti kuyambira pamenepo, adzamvera malamulo a Yehova. Zimenezi zinamuthandiza kuona kuti Yehova ndi ‘wabwino ndi wokonzeka kukhululuka.’ (Salimo 51:1-19; 86:5) Koma nanga bwanji ngati tikudziimbabe mlandu kwambiri ndipo manyazi sakutha ngakhale kuti tinalapa ndipo tinakhululukidwa?

19 Nthawi zina munthu amene anachimwa, chikumbumtima chake chingamusowetse mtendere monyanyira ngakhale kuti iye analapa, ndipo chingachite zimenezi kwa nthawi yaitali. Ngati mtima wathu ukutiimba mlandu choncho, ndi bwino kuutsimikizira kuti Yehova ndi wamkulu kuposa mtima wa munthu. Tiyenera kukhulupiriradi ndi kuvomereza kuti iye amatikonda ndipo anatikhululukira. Zimenezi ndi zimenenso ife timalimbikitsa ena kuchita. (Werengani 1 Yohane 3:19, 20.) Komabe, chikumbumtima choyera chimatibweretsera mtendere wamumtima ndiponso chimwemwe chachikulu chimene sichipezeka wamba m’dzikoli. Anthu ambiri amene m’mbuyomu anachita machimo aakulu, apeza mtendere umenewu ndipo masiku ano amatha kukhalabe ndi chikumbumtima chabwino pamene akutumikira Yehova Mulungu.—1 Akorinto 6:11.

20, 21. (a) Kodi bukuli lakonzedwa kuti likuthandizeni kuchita chiyani? (b) Kodi ife Akhristu tili ndi ufulu wotani, koma kodi tiyenera kuugwiritsa ntchito bwanji?

20 Cholinga cha bukuli ndi kukuthandizani kupeza chimwemwe pamene mukupitiriza kukhala ndi chikumbumtima chabwino m’masiku otsiriza a dziko la Satanali. Komabe, bukuli silingafotokoze malamulo ndi mfundo zonse za m’Baibulo zimene mufunikira kuziganizira ndi kuzigwiritsa ntchito pa moyo wanu wa tsiku ndi tsiku. Ndiponso musayembekezere kuti mupeza malamulo oneneratu choyenera kapena chosayenera kuchita pa nkhani zofuna chikumbumtima. Bukuli lakonzedwa kuti likuthandizeni kuphunzitsa ndi kupatsa mphamvu chikumbumtima chanu. Mungachite zimenezi pophunzira mmene mungagwiritsire ntchito Mawu a Mulungu tsiku lililonse. Mosiyana ndi Chilamulo cha Mose, “chilamulo cha Khristu” chimafuna kuti anthu amene akuchitsatira aziyendera kwambiri chikumbumtima ndi mfundo za m’Baibulo m’malo modalira kwambiri malamulo olembedwa. (Agalatiya 6:2) Mwanjira imeneyi, Yehova amapatsa Akhristu ufulu waukulu. Komabe, Mawu ake amatichenjeza kuti tisagwiritse ntchito ufulu umenewu ngati “chophimbira zoipa.” (1 Petulo 2:16) M’malomwake, ufulu umenewu umatipatsa mwayi waukulu wosonyeza kuti timakondadi Yehova.

21 Musanasankhe zochita, muzipemphera ndi kuganizira mmene mungagwiritsire bwino ntchito mfundo za m’Baibulo. Mukamachita zimenezi, mudzapitiriza ntchito yofunika kwambiri imene munaiyamba mutangodziwa Yehova, yophunzitsa ‘mphamvu zanu za kuzindikira’ ‘pozigwiritsa ntchito.’ (Aheberi 5:14) Chikumbumtima chanu chophunzitsidwa Baibulo chidzakuthandizani kwambiri pa moyo wanu wonse. Mofanana ndi kampasi imene imatsogolera apaulendo, chikumbumtima chanu chidzakuthandizani kusankha kuchita zimene Atate wanu wakumwamba adzakondwera nazo. Izi ndi zimene zingakuthandizeni kupitiriza kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kukukondani.

^ ndime 5 M’Malemba Achiheberi mulibe mawu enieni akuti “chikumbumtima.” Komabe, chitsanzo chimenechi chikusonyeza kuti anthu ankagwiritsa ntchito chikumbumtima. Mawu akuti “mtima” nthawi zambiri amanena za munthu wamkati. M’nkhani ya Yobu, zikuoneka kuti mawuwa akutchula za munthu wamkati, chomwe ndi chikumbumtima. M’Malemba Achigiriki Achikhristu, mawu Achigiriki otanthauza “chikumbumtima” amapezeka pafupifupi malo 30.

^ ndime 8 Baibulo limasonyeza kuti, ngati munthu chikumbumtima chake sichikumutsutsa, sizitanthauza kuti basi zonse zili bwino. Mwachitsanzo, Paulo anati: “Sindikudziwa kanthu kalikonse konditsutsa mumtima mwanga. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti basi ndine wolungama, koma Yehova ndiye amandifufuza.” (1 Akorinto 4:4) Ngakhale anthu amene amazunza Akhristu, monga mmene Paulo ankachitira asanakhale Mkhristu, angazunze Akhristu popanda kutsutsidwa ndi chikumbumtima chawo chifukwa choganiza kuti akuchita zimene Mulungu amakondwera nazo. Choncho, chofunika kwambiri sikungokhala ndi chikumbumtima chosatitsutsa, koma chiyeneranso kukhala choyera pamaso pa Mulungu.—Machitidwe 23:1; 2 Timoteyo 1:3.

^ ndime 10 Madokotala ambiri amanena kuti anthu amene mowa unawalowerera m’magazi, sangathe kumwa modziletsa. Kwa anthu amenewa, “kudziletsa” kumatanthauza kusamwa mowa ngakhale pang’ono.