Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Maremagnum/Corbis Documentary via Getty Images

KHALANI MASO!

Kodi Aramagedo Idzayambila ku Israel?—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

Kodi Aramagedo Idzayambila ku Israel?—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

 Baibo ikamakamba za Aramagedo sinena kuti ni nkhondo imene idzakhudza dela locepa cabe, koma imati ni nkhondo ya padziko lonse. Imeneyi idzakhala nkhondo ya pakati pa maboma onse a anthu na Mulungu.

  •   “Mauthenga ouzilidwa ndi ziwanda. . . akupita kwa mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti awasonkhanitse pamodzi kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse. . . . Anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene mʼCiheberi amachulidwa kuti Aramagedo.”—Chivumbulutso 16:14, 16.

 Liwu lakuti “Aramagedo” licokela ku mawu a Ciheberi akuti Har Meghid·dohnʹ, amene atanthauza “Phili la Megido.” Megido unali mzinda wakale ku Israel. Pa cifukwa cimeneci, anthu ambili amakhulupilila kuti Aramagedo idzacitikila ku Israel. Komabe, malo a ku Megido kapena malo ena alionse ku Middle East ni ocepa kwambili. Conco “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu” na magulu awo ankhondo sangakwane kusonkhana kumeneko.

 Buku la Chivumbulutso linalembedwa “pogwilitsa nchito zizindikilo,” kapena kuti pogwilitsa nchito mawu ophiphilitsa. (Chivumbulutso 1:1) Motelo Aramagedo si malo enieni, koma ni nthawi pamene mitundu yonse padziko lonse idzasonkhana kuti iukile ulamulilo wa Mulungu kothela.—Chivumbulutso 19:11-16, 19-21.