Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

ZIMENE MUNGACITE PA PHUNZILO LA INU MWINI

Khalanibe Maso mwa Kuŵelenga Baibo Mwakhama

Khalanibe Maso mwa Kuŵelenga Baibo Mwakhama

Ŵelengani Danieli 9:​1-19 kuti mudziŵe kufunika koŵelenga Baibo mwakhama.

Mvetsani nkhani yonse. Ni zinthu ziti zimene zinali zitangocitika kumene? Nanga zinamukhudza bwanji Danieli? (Dan. 5:29–6:5) Mukanamva bwanji mukanakhala Danieli?

Kumbani mozamilapo. Ni “mabuku opatulika” ati amene Danieli ayenela kuti anali kuŵelenga? (Dan. 9:​2, mawu a m’munsi; w11 1/1 22 ¶2) N’cifukwa ciyani Danieli anavomeleza macimo ake komanso a mtundu wa Isiraeli? (Lev. 26:​39-42; 1 Maf. 8:​46-50; dp 182-184) Kodi pemphelo la Danieli lionetsa bwanji kuti anali kukonda kuŵelenga Mawu a Mulungu mwakhama?—Dan. 9:​11-13.

Onani maphunzilo amene mutengapo. Dzifunseni kuti:

  • ‘Ningapewe bwanji kuceutsidwa na zocitika za m’dzikoli?’ (Mika 7:7)

  • ‘Ningapindule bwanji nikamaŵelenga Mawu a Mulungu mwakhama mmene Danieli anali kucitila?’ (w04 8/1 12 ¶17)

  • ‘Ni nkhani ziti zimene ningaŵelenge pa phunzilo la ine mwini zimene zinganithandize ‘kukhalabe maso’?’ (Mat. 24:​42, 44; w12 8/15 5 ¶7-8)