Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Zimene Zingakuthandizeni Mukasamukila mu Mpingo Watsopano

Zimene Zingakuthandizeni Mukasamukila mu Mpingo Watsopano

KODI munasamukilapo mu mpingo watsopano? Ngati n’conco, mungagwilizane na zimene Jean-Charles anakamba. Iye anati: “Munthu akasamukila mu mpingo wina si copepuka kwa iye pamodzi na a m’banja lake kupitiliza kukhala anthu auzimu.” Amene asamuka amafunika kupeza nchito, malo okhala, komanso masukulu atsopano. Kuwonjezela pa izi, amalimbananso na nyengo imene sanaizoloŵele, cikhalidwe cosiyana na cawo, komanso dela latsopano lolalikila.

Onani zimene Nicolas na Céline anakumana nazo. Ofesi ya nthambi ya ku France inawatumiza ku mpingo watsopano. Iwo anakamba kuti: “Paciyambi tinali acimwemwe, koma kenako tinayamba kuyewa mabwenzi amene tinasiya. Abale na alongo mu mpingo watsopano tinali tisanazoloŵelane nawo.” a Kodi mungathane nawo bwanji mavuto obwela cifukwa cosamukila mu mpingo watsopano? Kodi ena angakuthandizeni bwanji? Kodi anthu a mu mpingo watsopanowo angakulimbikitseni bwanji? Nanga inu mungawalimbikitse bwanji?

MFUNDO ZINAYI ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI KUGONJETSA ZOPINGA

Dalilani Yehova

1. Dalilani Yehova. (Sal. 37:5) Mlongo Kazumi wa ku Japan anasamuka mu mpingo umene anali atatumikilamo kwa zaka 20 mwamuna wake atasinthidwa malo ogwilila nchito. Kodi ‘analola bwanji Yehova kumutsogolela’? Iye anati: “N’nakhutulila Yehova zonse za mumtima mwanga, monga kupanikizika maganizo, kusungulumwa, komanso nkhawa. Nthawi zonse nikacita zimenezi anali kunipatsa mphamvu.”

Mungacite ciyani kuti muzim’dalila ngako Yehova? Monga mmene mtengo umafunikila madzi na zakudya zina m’nthaka, cikhulupililo cathu naconso cimafuna kudyetsedwa kuti cikule. Nicolas amene tam’chula uja, anapeza kuti kusinkhasinkha za anthu amene anadzimana zambili kuti acite cifunilo ca Mulungu monga Abulahamu, Yesu, komanso Paulo—kunalimbitsa cidalilo cake cakuti Yehova adzam’thandiza. Kukhala na pulogilamu yokhazikika yophunzila Baibo panokha kudzakuthandizani zinthu zikasintha pa umoyo wanu. Kuwonjezela apo, kudzakuthandizani kukhala na mphatso yauzimu, imene mungagaŵileko ena mu mpingo watsopano.

Pewani kuyelekezela na mpingo wanu wakale

2. Pewani kuyelekezela na mpingo wanu wakale. (Mlal. 7:10) Jules amene anacoka ku Benini kupita ku United States anapeza kuti zikhalidwe za maiko aŵiliwa zinali zosiyana zedi. Iye anati, “Nikakumana na munthu n’nali kudzimva wokakamizika kufotokoza mbili yonse ya moyo yanga.” Cifukwa izi zinali zosiyana na cikhalidwe ca kwawo, iye anayamba kuwapewa abale na alongo. Koma atawadziŵa bwino abale na alongo amenewo, anasintha kaonedwe kake ka zinthu. Anati: “Tsopano nazindikila kuti anthu n’cimodzi-modzi mosasamala kanthu kumene ali. Cimene cimaŵasiyanitsa ni kakambidwe na kacitidwe kawo ka zinthu. N’cinthu cofunika kutenga munthu aliyense mmene alili.” Conco pewani kuyelekezela mpingo watsopanowo na umene munacokela. Mlongo wina amene ni mpainiya dzina lake Anne-Lise, anakamba kuti: “Ninasamuka kuti nikaphunzile zinthu zatsopano, osati kuti nikapeze zinthu zimene n’nasiya kudela lakale.”

Akulu nawonso ayenela kupewa kuyelekezela mpingo watsopano na umene analiko kale. Dziŵani kuti si nthawi zonse pamene kumakhala kulakwitsa abale a mu mpingo wanu watsopano akamacita zinthu mosiyana na kumene munacokela. N’cinthu canzelu kudziŵa bwino mmene zinthu zilili kumaloko musanapelekepo malingalilo anu. (Mlal. 3:​1, 7b) Ni bwino kuphunzitsa ena mwa citsanzo canu, m’malo mokakamiza abale na alongo kuyendela zimene inu mufuna.—2 Akor. 1:24.

Muzitengamo mbali

3. Muzitengamo mbali m’zocitika za mpingo wanu watsopano. (Afil. 1:27) Kusamuka n’kotopetsa ndipo kumafuna nthawi. Koma ngakhale n’conco, mukangofika kudela latsopano, ni bwino kupezeka ku misonkhano pamaso-m’pamaso ngati mungathe. Ni iko komwe, ngati abale na alongo a ku mpingo wanu watsopano amakuonani mwa apa ni apo, kodi angakuthandizeni bwanji? Lucinda amene anasamukila ku mzinda waukulu ku South Africa pamodzi na ana ake aŵili anati: “Ena ananilimbikitsa kuti niyenela kudziŵana nawo bwino anthu a mu mpingo wanga watsopano, kulalikila nawo limodzi, komanso kuyankhapo pa misonkhano. Tinapelekanso nyumba yathu kuti tizicitilamo makambilano a ulaliki.

Kucita nawo zinthu “mogwilizana” abale na alongo anu mu mpingo watsopanowo kudzakulimbikitsani ndipo mudzalimbikitsanso ena. Anne-Lise amene tamuchula uja, akulu anamulimbikitsa kuti azilalikila na aliyense. Kodi panakhala zotulukapo zotani? Iye anati: “N’nazindikila kuti kucita izi n’kothandiza kuti uziona kuti uli mbali ya mpingo.” Kugwilako nawo nchito za Nyumba ya Ufumu monga kuyeletsa komanso kukonza zowonongeka, kumaonetsa abale na alongo kuti lomba umaona kuti uli mbali ya mpingo watsopanowo. Mukamacita zimenezi mobweleza-bweleza iwonso adzakulandilani, ndipo mudzazimva kuti mwafika m’banja latsopano lauzimu.

Pangani mabwenzi atsopano

4. Pangani mabwenzi atsopano. (2 Akor. 6:​11-13) Kuonetsa ena cidwi ni njila yabwino yopangila mabwenzi. Conco misonkhano isanayambe komanso ikatha, muzipeza nthawi yowadziŵa bwino abale na alongo. Muzicita khama kudziŵa maina awo. Kukhala waubwenzi, kukhala wofikilika, komanso kukumbukila maina ya anthu ena, mosakaikila kudzakuthandizani kuti akuyandikileni. Ndipo izi zidzapangitsa kuti mupange mabwenzi atsopano.

Pewani kufuna kukhala munthu amene simuli pofuna kukondweletsa ena. Koma lolani kuti ena akudziŵeni mmene mulili. Phunzilani ku zimene Lucinda ananena pomwe anati, “Tili na mabwenzi tsopano cifukwa coitanila ena ku nyumba kwathu.”

“MUZILANDILANA”

Ena angacite mantha kuloŵa m’Nyumba ya Ufumu mmene muli anthu acilendo. Kodi mungaŵathandize bwanji anthu amene asamukila mu mpingo wanu? Mtumwi Paulo anati, “Muzilandilana, ngati mmene Khristu anatilandilila.” (Aroma 15:7) Potengela citsanzo ca Khristu, akulu angathandize amene asamukila mu mpingo mwawo kuona kuti ni olandilidwa. (Onani bokosi lakuti “ Zimene Zingakuthandizeni Mukasamuka.”) Onse mu mpingo kuphatikizapo ana, ali na udindo wopangitsa ena kumva kuti ni olandilidwa.

Kulandila ena kumaphatikizapo kuŵaceleza, komanso kuŵathandiza na zinthu zimene tili nazo. Mwa citsanzo, mlongo wina anadzipeleka kuthandiza mlongo amene anali atangofika kumene m’dela lawo. Anamuonetsa tauni komanso kokwelela basi. Mlongo watsopanoyo anakhudzidwa ngako na zimene mlongo mnzakeyo anamucitila, ndipo izi zinamuthandiza kuzoloŵela dela latsopanolo.

KUSAMUKA KUMATIPATSA MWAYI WOTITHANDIZA KUKULA

Dzombe likamakula, limafunduka mobweleza-bweleza lisanayambe kuuluka. Mofananamo, mukasamukila mu mpingo wina, muyenela kuthetsa mantha amene angakulepheletseni kuuluka mu utumiki wa Yehova, titelo kunena kwina. Nicolas na Celine anati: “Kuyenda ni maphunzilo.” Anakambanso kuti, “Kuzoloŵelana na anthu komanso malo atsopano, kunatithandiza kukulitsa makhalidwe omwe tinalibe.” Ponena za mmene banja lake linapindulila, Jean-Charles amene tam’chula kuciyambi ananena kuti: “Kusamuka kwapangitsa ana athu kukula kuuzimu komanso kuyandikila Yehova. Titangokhala miyezi yocepa mu mpingo watsopano, mwana wathu wamkazi anayamba kukamba nkhani pa msonkhano wa mkati mwa mlungu, ndipo mwana wathu wamwamuna anakhala wofalitsa wosabatizika.”

Koma bwanji ngati simungathe kusamuka, monga kupita kukatumikila ku malo osoŵa? Kuseŵenzetsa mfundo zomwe zafotokozedwa m’nkhani ino kungapangitse mpingo wanu kuoneka ngati watsopano kwa inu. Pamene mukupitiliza kudalila Yehova, pitilizani kukhala na zocita zambili mu mpingo mwa kulalikila na ena, kupanga mabwenzi atsopano na kuwadziŵa bwino mabwenzi omwe muli nawo kale. Mwina mungathandize acatsopano kapena osoŵa mwakuthupi. Popeza cikondi cimadziŵikitsa Akhristu oona, mukamathandiza ena mudzamuyandikila ngako Yehova. (Yoh. 13:35) Ndipo dziŵani kuti “Mulungu amasangalala ndi nsembe zotelozo.”—Aheb. 13:16.

Akhristu ambili akwanitsa kupeza cimwemwe mu mpingo watsopano, mosasamala kanthu za mavuto amene akumana nawo. Inunso mungatelo. Mlongo Anne-Lise anakamba kuti, “Kusintha mpingo kunatsegula kwambili mtima wanga.” Nayenso Kazumi tsopano ni wotsimikiza mtima kuti “ukasamuka umaona thandizo la Yehova m’njila imene sunaiganizilepo.” Nayenso Jules anati: “Mabwenzi omwe napeza anithandiza kuti nisamadzimve wosungulumwa. Tsopano nimaona kuti ndine mbali ya mpingo moti cidzakhala covuta kwambili nikadzafuna kusamuka.”

a Kuti mudziŵe zimene zingakuthandizeni mukamayewa kunyumba pamene mukutumikila Mulungu, onani nkhani yakuti “Kulimbana ndi Malingalilo a Kulakalaka Kumudzi Kwanu mu Utumiki wa Mulungu,” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 1994.