Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GAWO 9

Lambilani Yehova Monga Banja

Lambilani Yehova Monga Banja

“Lambilani iye amene anapanga kumwamba, dziko lapansi.”—Chivumbulutso 14:7

Monga mmene taphunzilila m’kabuku kano, m’Baibulo muli mfundo zambili zimene zingakuthandizeni pamodzi ndi banja lanu. Yehova afuna kuti mukhale acimwemwe. Iye walonjeza kuti ngati muika kulambila koona patsogolo, zinthu “zina zonsezi zidzaonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Iye afunitsitsa kuti mukhale bwenzi lake. Gwilitsilani nchito mpata uliwonse kuti mukulitse ubwenzi wanu ndi Mulungu. Uwu ndi mwai waukulu kwambili umene munthu angakhale nao.—Mateyu 22:37, 38.

1 LIMBITSANI UBWENZI WANU NDI YEHOVA

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “‘Ndidzakhala atate wanu, ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,’ watelo Yehova.” (2 Akorinto 6:18) Mulungu afuna kuti mukhale bwenzi lake la pamtima. Pemphelo ndi njila imodzi imene ingakuthandizeni kucita zimenezo. Yehova akupemphani kuti “muzipemphela mosalekeza.” (1 Atesalonika. 5:17) Iye ndi wofunitsitsa kumva zakukhosi kwanu ndi nkhawa zanu. (Afilipi 4:6) Mukamapemphela ndi banja lanu io adzaona kuti Mulungu ndi weniweni kwa inu.

Kuonjezela pa kukamba ndi Mulungu, muyenelanso kumumvela. Mungacite zimenezo mwa kuphunzila Mau ake ndi mabuku ofotokoza Baibulo. (Salimo 1:1, 2) Muzisinkhasinkha zimene mwaphunzila. (Salimo 77:11, 12) Kumvetsela kwa Mulungu kumafunanso kuti tizipezeka pa misonkhano yacikristu nthawi zonse.—Salimo 122:1-4.

Kulalikila kwa ena za Yehova ndi njila inanso yofunika yolimbitsila ubwenzi wanu ndi iye. Kulalikila kaŵilikaŵili kudzakuthandizani kumuyandikila kwambili.—Mateyu 28:19, 20.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Tsiku lililonse muzipatula nthawi yoŵelenga Baibulo ndi kupemphela

  • Monga banja, ikani zinthu za kuuzimu pamalo oyamba, m’malo mwa zosangulutsa ndi kupumula

2 SANGALALANI NDI KULAMBILA KWANU KWA PABANJA

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.” (Yakobo 4:8) Muyenela kukhala ndi ndandanda yokhazikika yocita kulambila kwa pabanja, ndipo muyenela kuitsatila. (Genesis 18:19) Koma muyenela kucita zambili kuposa pamenepa. Mulungu ayenela kukhala mbali ya moyo wanu watsiku ndi tsiku. Muyenela kulimbitsa ubwenzi wa banja lanu ndi Mulungu mwa kulankhula za iye ‘mukakhala pansi m’nyumba mwanu, poyenda pamseu, pogona ndi podzuka.’ (Deuteronomo 6:6, 7) Yesetsani kukhala ngati Yoswa, amene anati: “Koma ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikila Yehova.”—Yoswa 24:15.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Khalani ndi pulogalamu yophunzitsa yodalilika imene idzakuthandizani kudziŵa zosoŵa za aliyense m’banja lanu