Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GAWO 8

Mavuto Akayamba

Mavuto Akayamba

“Pa cifukwa cimeneci, mukusangalala kwambili ngakhale kuti padakali pano n’koyenela kuti muvutike kwa kanthawi cifukwa ca mayeselo osiyanasiyana amene akukucititsani mavuto.”—1 Petulo 1:6

Ngakhale mutayesetsa bwanji kukhala ndi banja lacimwemwe, zinthu zosayembekezeleka zingacitike zimene zingapangitse kuti zikhale zovuta kuti mukhale ndi cimwemwe. (Mlaliki 9:11) Tikakumana ndi zovuta, Mulungu mwacikondi amatipatsa thandizo. Mukatsatila mfundo za m’Baibulo zotsatilazi, inu ndi banja lanu mudzakwanitsa kulimbana ndi mavuto, ngakhale aakulu kwambili.

1 DALILANI YEHOVA

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: ‘Mutulileni nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.’ (1 Petulo 5:7) Nthawi zonse kumbukilani kuti Mulungu sindiye akucititsa mavuto anu. (Yakobo 1:13) Ngati mudzamuyandikila, iye adzakuthandizani m’njila yoyenelela. (Yesaya 41:10) “Mukhutulileni za mumtima mwanu.”—Salimo 62:8.

Kuŵelenga ndi kuphunzila Baibulo kudzakuthandizaninso kupeza citonthozo. Mukatelo, mudzaona mmene Yehova ‘amatitonthozela m’masautso amtundu uliwonse.’ (2 Akorinto 1:3, 4; Aroma 15:4) Iye amalonjeza kuti adzakupatsani “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.”—Afilipi 4:6, 7, 13.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Pemphelani kwa Yehova kuti mukhale odekha ndi oganiza bwino

  • Onaninso zonse zimene mufuna kucita ndipo sankhani zimene muona kuti zili bwino

2 SAMALILANI THANZI LANU NDI BANJA LANU

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Mtima wa munthu womvetsa zinthu umadziŵa zinthu, ndipo khutu la anzelu limafunafuna kudziŵa zinthu.” (Miyambo 18:15) Mvetsetsani mfundo zonse. Onani zimene aliyense m’banja akufunikila. Kambani nao ndipo mvetselani akamakamba.—Miyambo 20:5.

Bwanji ngati wokondedwa wanu wamwalila? Musaope kuonetsa cisoni canu. Kumbukilani kuti ngakhale “Yesu anagwetsa misozi.” (Yohane 11:35; Mlaliki 3:4) Kupuma ndi kugona mokwanila n’kofunika kwambili. (Mlaliki 4:6) Kucita zimenezi kudzakuthandizani kuti muthe kulimbana ndi vuto limene likuvutitsa maganizo anu.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Mavuto asanayambe, khalani ndi cizoloŵezi cokambitsilana ndi a m’banja lanu. Kucita zimenezi kudzawathandiza kulankhula nanu momasuka pamene mavuto ayamba

  • Mungauzeko ena amene anakumanako ndi vuto lofanana ndi limenelo

3 PEZANI THANDIZO LIMENE MUFUNIKILA

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Bwenzi lenileni limakonda nthawi zonse ndipo ilo ndi mbale amene anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.” (Miyambo 17:17) Anzanu angafune kukuthandizani koma sangadziŵe zimene mukufuna. Conco, musalephele kuwauza zimene mufuna. (Miyambo 12:25) Komanso pezani thandizo la kuuzimu kwa amene amamvetsetsa Baibulo. Malangizo a m’Baibulo amene angakuuzeni angakuthandizeni.—Yakobo 5:14.

Mudzapeza thandizo limene mukufunikila ngati mugwilizana nthawi zonse ndi anthu amene amakhulupililadi Mulungu ndipo amadalila malonjezo ake. Mudzapezanso citonthozo pamene muthandiza anthu ofunika kuwalimbikitsa. Auzeni za cikhulupililo canu mwa Yehova ndi malonjezo ake. Khalani otangwanika ndi kuthandiza anthu ena ofunika thandizo, musadzipatule kwa anthu amene amakukondani ndiponso amene amasamala za inu.—Miyambo 18:1; 1 Akorinto 15:58.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Fotokozelani mnzanu wapamtima ndipo landilani thandizo limene angakupatseni

  • Khalani oona mtima ndipo osapita m’mbali ponena za thandizo limene mukufuna