Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GAWO 4

Mmene Mungagwilitsile Nchito Ndalama

Mmene Mungagwilitsile Nchito Ndalama

“Zolinga zimakhazikika anthu akakambilana.”—Miyambo 20:18

Tonse timafunika ndalama kuti tisamalile zofunika za mabanja athu. (Miyambo 30:8) Ndipo, “ndalama zimatetezela.” (Mlaliki 7:12) Monga banja, zingakhale zovuta kukambilana za ndalama. Koma musalole kuti ndalama ziyambitse mavuto m’cikwati canu. (Aefeso 4:32) Pokambilana mmene angagwilitsile nchito ndalama, anthu okwatilana ayenela kukhulupililana ndi kucitila zinthu pamodzi.

1 KONZANI ZINTHU MOSAMALA

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Ndani wa inu akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi kuŵelengela ndalama zimene adzaononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanila kumalizila nsanjayo?” (Luka 14:28) Ndi bwino kukonzela pamodzi mmene mudzagwilitsila nchito ndalama. (Amosi 3:3) Sankhani zimene mufuna kugula ndipo muone ndalama zimene mungagwilitsile nchito. (Miyambo 31:16) Kukhala ndi ndalama zogulila cinacake sikutanthauza kuti mungangogula cinthu ciliconse. Yesetsani kupewa nkhongole. Gwilitsilani nchito ndalama zimene muli nazo.—Miyambo 21:5; 22:7.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Ngati pakutha kwa mwezi mwatsalako ndi ndalama zina, muzikambilana mmene mudzazigwilitsila nchito

  • Ngati ndalama n’zocepa, kambilanani mmene mungacepetsele zogula. Mwacitsanzo, m’malo mogula cakudya cophikidwa kale, ndi bwino kuphika nokha

2 KHALANI OONA MTIMA NDI KUONA NDALAMA MOYENELA

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: ‘Samalilani zinthu zonse moona mtima, osati pamaso pa Yehova yekha ayi, komanso pamaso pa anthu.’ (2 Akorinto 8:21) Khalani woona mtima kwa mnzanu wa m’cikwati pa ndalama zimene mumapeza ndi kugwilitsila nchito.

Nthawi zonse muzifunsa mnzanu wa m’cikwati pamene mupanga zosankha zikuluzikulu zokhudza ndalama zanu. (Miyambo 13:10) Kukambilana za ndalama kudzathandiza kusunga mtendele m’cikwati canu. Muziona ndalama zimene mumapeza monga za banja osati zanu.—1 Timoteyo 5:8.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Gwilizanani kuti ndi ndalama zingati zimene aliyense wa inu azigwilitsila nchito popanda kufunsa mnzake

  • Musamangokambilana za ndalama pakakhala vuto