Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GAWO 5

Mmene Mungakhalile Mwamtendele ndi Acibale Anu

Mmene Mungakhalile Mwamtendele ndi Acibale Anu

“Valani . . . kukoma mtima, kudzicepetsa, kufatsa ndi kuleza mtima.”—Akolose 3:12

Anthu akakwatilana amayamba banja latsopano. Ngakhale kuti mudzapitilizabe kukonda makolo anu ndi kuwalemekeza, munthu wofunika kwambili kwa inu tsopano ndi mwamuna kapena mkazi wanu. Acibale anu ena zingawavute kuvomeleza zimenezi. Koma mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni kucita zinthu bwinobwino kuti mukhale mwamtendele ndi acibale anu pamene mukuyesetsanso kulimbitsa ubale wa banja lanu latsopano.

1 PITILIZANI KUONA MOYENELELA ACIBALE ANU

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Uzilemekeza bambo ako ndi mai ako.” (Aefeso 6:2) Zilibe kanthu kuti muli pa msinkhu uti, muyenela kulemekezabe makolo anu. Dziŵaninso kuti naye mnzanu wa m’cikwati ali ndi makolo, ndipo afunika kuwasamalila. Popeza kuti “cikondi sicicita nsanje,” pewani kukalipa mnzanu wa m’cikwati akamaceza ndi acibale ake.—1 Akorinto 13:4; Agalatiya 5:26.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Pewani kulankhula mau monga akuti, “Acibale ako nthawi zonse sandiŵelengela” kapena “Nthawi zonse amai ako sakonda zimene ndimacita”

  • Yesani kuona zinthu mmene mnzanu wa m’cikwati akuzionela

2 KHALANI OSASUNTHIKA NGATI M’POFUNIKA KUTELO

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mai ake n’kudziphatika kwa mkazi wake ndipo io adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Mukaloŵa m’banja, makolo anu angamaone kuti akali ndi udindo wofunika kukusamalilani, ndipo akhoza kumafuna kuloŵelela kwambili m’cikwati canu.

Zili kwa inu ndi mnzanu wa m’cikwati kugwilizana pamene io angalekezele ndipo mungawadziŵitse mwacikondi. Khalani omasuka pokamba nao ndipo musawapite m’mbali koma kambani mwaulemu osati monyoza. (Miyambo 15:1) Kudzicepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima kudzakuthandizani kukhala paubale wabwino ndi acibale anu ndipo mudzapitiliza “kulolelana m’cikondi.”—Ephesians 4:2.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Ngati mwakhudzidwa kwambili ndi mmene acibale aloŵelela mu umoyo wanu wabanja, kambilanani ndi mnzanu wa m’cikwati mtima ukakhala pansi

  • Kambilanani mmene mungathetsele mavuto amenewa