Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Yohane 15:13​—“Palibe Munthu Ali Nacho Chikondi Choposa Ichi”

Yohane 15:13​—“Palibe Munthu Ali Nacho Chikondi Choposa Ichi”

 “Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.”​—Yohane 15:13, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.”​—Yohane 15:13, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Yohane 15:13

 Yesu ankathandiza otsatira ake kudziwa kuti ayenera kusonyezana chikondi chachikulu chofika pololera kufera anzawo.

 Asananene mawuwa, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Lamulo langa ndi ili, mukondane monga mmene inenso ndakukonderani.” (Yohane 15:12) Kodi Yesu ankawasonyeza chikondi chotani? Iye sanali wodzikonda ndipo anali ndi chikondi chololera kuvutikira ena. Pa nthawi imene ankachita utumiki wake padzikoli, ankaika patsogolo zofuna za ophunzira ake ndi anthu ena, m’malo mwa zofuna zake. Anachiritsa anthu omwe ankadwala komanso anawaphunzitsa zokhudza Ufumu wa Mulungu. a Ankagwiranso ntchito zonyozeka ndi cholinga chofuna kuthandiza ena. (Mateyu 9:35; Luka 22:27; Yohane 13:3-5) Koma pa Yohane 15:13, Yesu ankanena za chikondi chachikulu kwambiri kuposa pamenepa. Ndipo patangodutsa maola ochepa atalankhula mawu amenewa, anasonyeza chikondi chimenechi pamene analolera ‘kupereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.’ (Mateyu 20:28; 22:39) Pamenepatu anasonyeza m’njira yapamwamba kwambiri kuti ankakonda anthu ena kuposa mmene ankadzikondera yekha.

 Yesu amakonda anthu onse. Koma amakonda kwambiri anthu omwe amatsatira zomwe anaphunzitsa. Iye ankaona ophunzira ake monga mabwenzi ake apamtima chifukwa ankatsatira zomwe ankawaphunzitsa komanso chifukwa choti sanamusiye pa nthawi yomwe ankakumana ndi mayesero. (Luka 22:28; Yohane 15:14, 15) Choncho zimenezi zinamulimbikitsanso kwambiri kuti apereke moyo wake chifukwa cha iwo.

 Akhristu amunthawi ya atumwi anagwiritsa ntchito mawu a Yesu aja ndipo anali okonzeka kufera Akhristu anzawo. (1 Yohane 3:16) Chikondi chololera kuvutikira ena chomwe Yesu anasonyezachi, chinadzakhala chizindikiro chachikulu cha Akhristu oona.​—Yohane 13:34, 35.

Nkhani yonse ya pa Yohane 15:13

 Muchaputala 13 mpaka 17 cha Uthenga Wabwino wa Yohane, muli nkhani yofotokoza zomwe Yesu anauza ophunzira ake okhulupirika okwana 11 komanso pemphero lomaliza lomwe anapemphera nawo limodzi. Pasanapite maola ambiri, Yesu anaphedwa. Muchaputala 15, Yesu anayerekezera ophunzira ake ndi zipatso za mtengo wa mpesa pofuna kuwathandiza kuona kufunika kochita zinthu mogwirizana ndi iye, zomwe zikanasonyezadi ngati anali otsatira ake enieni. Iye anawalimbikitsa kuti ‘abereke zipatso zochuluka.’ (Yohane 15:1-5, 8) Njira imodzi imene otsatira ake amachitira zimenezi ndi kusonyezana chikondi chololera kuvutikira ena, zomwe zikuphatikizapo kulalikira “uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu” umene Yesu ankalalikira.​—Luka 4:43; Yohane 15:10, 17.

 Onerani vidiyo yaifupiyi kuti muone mfundo zachidule zokhudza buku la Yohane

a Ufumu wa Mulungu ndi boma lomwe lili kumwamba. Mulungu anakhazikitsa Ufumuwu kuti udzalamulire dziko lapansi kuti cholinga chomwe analengera dzikoli chidzakwaniritsidwe. (Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10) Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti, “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?