Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MALEMBA A M’BAIBULO

Aroma 15:13​—“Mulungu amene amapereka chiyembekezo akudzazeni ndi chimwemwe chonse ndi mtendere.”

Aroma 15:13​—“Mulungu amene amapereka chiyembekezo akudzazeni ndi chimwemwe chonse ndi mtendere.”

 “Mulungu amene amapereka chiyembekezo akudzazeni ndi chimwemwe chonse ndi mtendere wonse chifukwa cha kukhulupirira kwanu, kuti mukhale ndi chiyembekezo chachikulu mwa mphamvu ya mzimu woyera.”​—Aroma 15:13, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m’kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.”—Aroma 15:13, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Aroma 15:13

 Pavesili, Paulo ananena zomwe ankalakalaka zoti Mulungu athandize okhulupirira anzake kuti akhale ndi “chimwemwe chonse ndi mtendere.” Makhalidwe awiriwa ndi ogwirizana ndi chiyembekezo chomwe Mulungu amatipatsa komanso ndi ogwirizana ndi mzimu wake woyera.

 M’Baibulo, omwe ndi mawu a Mulungu, timaphunzira za chiyembekezo chimene Mulungu amatipatsa. Mogwirizana ndi lemba la Aroma 15:4, “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale [m’Baibulo] zinalembedwa kuti zitilangize. Malembawa amatipatsa chiyembekezo chifukwa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.” Baibulo limatiuza zomwe Mulungu analonjeza zoti adzathetsa mavuto omwe amachititsa moyo wathu masiku ano kukhala wopanda chiyembekezo. Iye adzathetsa umphawi, kupanda chilungamo, matenda komanso imfa. (Chivumbulutso 21:4) Mulungu adzagwiritsa ntchito Yesu Khristu kuti akwaniritse malonjezo amenewa. Ichi n’chifukwa chake tikuyembekezera kuti m’tsogolomu moyo udzakhala wabwino kwambiri.​—Aroma 15:12.

 Tingakhale ndi chiyembekezo “chachikulu” kapena ‘chochuluka,’ pokhapokha ngati timakhulupirira Mulungu. Tikamaphunzira zambiri zokhudza iye, m’pamenenso timayamba kumudalira kwambiri. (Yesaya 46:10; Tito 1:2) Ndi pomveka kuti tiziyamikira chiyembekezo chomwe Mulungu anatipatsachi chifukwa chimatithandiza kukhala ndi chimwemwe komanso mtendere ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto.​—Aroma 12:12.

 Mtendere, chimwemwe ndi chiyembekezo ndi zogwirizananso ndi “mzimu woyera,” womwe ndi mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito. a Mulungu amagwiritsa ntchito mzimu woyera pokwaniritsa zomwe amalonjeza ndipo zimenezi zimatipatsa chiyembekezo. Mzimuwu umatithandizanso kuti tikhale ndi makhalidwe abwino monga chimwemwe ndi mtendere.​—Agalatiya 5:22.

Nkhani yonse ya Aroma 15:13

 Buku la Aroma ndi kalata yomwe mtumwi Paulo analembera Akhristu okhala mumzinda wa Roma. Ena mwa Akhristuwa anali Ayuda, pomwe ena sanali Ayuda. Paulo analimbikitsa Akhristu onsewa kuti ayesetse kukhala ogwirizana ngakhale kuti anali osiyana chikhalidwe komanso mmene anakulira.​—Aroma 15:6.

 Paulo anakumbutsa Akhristu a ku Roma kuti kalekale Mulungu anali ataneneratu za nthawi imene anthu a mitundu yonse adzamutamanda mogwirizana. Pofuna kutsindika mfundoyi, kwa nthawi zokwanira 4, Paulo anagwira mawu ochokera m’Malemba Achiheberi b. (Aroma 15:9-12) Mfundo yake inali yakuti: Anthu a mitundu ina limodzi ndi Ayuda, adzapindula ndi utumiki wa Khristu. Ndipo magulu awiri onsewa, ali ndi chiyembekezo chimodzi chochokera kwa Mulungu. Choncho Akhristu onse omwe anali mumpingo wa ku Roma posatengera kuti anali a chikhalidwe chotani, ankafunika ‘kulandirana’ kapena kuti kucherezana ndi kuchitirana zinthu mokoma mtima.​—Aroma 15:7.

a Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti “Kodi Mzimu woyera N’chiyani?

b Malemba Achiheberi, nthawi zina amadziwikanso kuti Chipangano Chakale.