Pitani ku nkhani yake

Kodi Sayansi Imagwirizana ndi Baibulo?

Kodi Sayansi Imagwirizana ndi Baibulo?

Yankho la m’Baibulo

 Inde. Ngakhale kuti Baibulo si buku la sayansi, limafotokoza molondola zinthu zokhudza sayansi. Tiyeni tione zitsanzo zingapo zimene zingatithandize kudziwa kuti Baibulo limagwirizana ndi sayansi. Tionanso mfundo zina zokhudza sayansi zopezeka m’Baibulo zimene zinkasiyana kwambiri ndi zikhulupiriro za anthu ambiri pa nthawi imene Baibulo linkalembedwa.

  •   Zinthu zonse zinachita kulengedwa. (Genesis 1:1) Koma nthano zambiri zakale zimafotokoza kuti zinthu zonse zimangokhalako zokha. Anthu a ku Babulo ankakhulupirira kuti milungu yochokera m’nyanja ziwiri ndi imene inabereka chilengedwe chonsechi. Ndiponso nthano zina zimanena kuti chilengedwechi chinachokera m’dzira linalake lalikulu.

  •   Zinthu zonse m’chilengedwe zimachita zinthu motsatira malamulo a m’chilengedwe osati motsatira milungu inayake. (Yobu 38:33; Yeremiya 33:25) Nthano zambiri m’dzikoli zimasonyeza kuti milungu ndi yamphamvu kwambiri moti ikhoza kuchitira anthu zilizonse zimene ikufuna, kaya zabwino kapena zoipa.

  •   Dziko lapansi lili m’malere. (Yobu 26:7) Anthu ambiri akale ankakhulupirira kuti dziko lapansi ndi lafulati ndipo lili pamsana pa nyama inayake yaikulu monga njati komanso kamba.

  •   Madzi amachoka m’nyanja, m’mitsinje komanso m’malo ena kupita kumwamba monga nthunzi ndipo kenako amagwanso padzikoli monga mvula, chipale chofewa kapena matalala ndipo amapitanso m’mitsinje. (Yobu 36:27, 28; Mlaliki 1:7; Yesaya 55:10; Amosi 9:6) Agiriki akale ankaganiza kuti madzi a m’mitsinje amachokera m’nyanja za pansi pa nthaka, ndipo anthu akhala akukhulupirira zimenezi mpaka m’zaka za m’ma 1700.

  •   Mapiri amatha kuphulika kuchokera pansi pa nthaka. Ndipo mapiri amene alipo panopa anali mkati mwa madzi a m’nyanja. (Salimo 104:6, 8) Koma nthano zambiri zimasonyeza kuti mapiri analengedwa m’mene alilimu ndi milungu.

  •   Malangizo okhudza ukhondo amene ankateteza anthu. M’malamulo amene anaperekedwa ku mtundu wa Aisiraeli munali lamulo oti azisamba m’manja akagwira mtembo. Lamulo lina linali loti anthu odwala matenda oti akhoza kupatsira anthu ena aziwapatula, ndipo lina linali loti komanso kufotsera zoipa akadzithandiza. (Levitiko 11:28; 13:1-5; Deuteronomo 23:13) Koma pa nthawi imene Aisiraeli ankapatsidwa malamulowa, Aiguputo ankaika pa zilonda mankhwala okhala ndi ndowe za munthu.

Kodi Baibulo lili ndi mfundo zolakwika zokhudza sayansi?

 Tikafufuza bwino zimene zili m’Baibulo, tingayankhe kuti ayi. Tiyeni tione zinthu zina zimene anthu amanena zokhudza mfundo za sayansi zimene zili m’Baibulo:

 Zimene ena amakhulupirira: Baibulo limanena kuti dzikoli linalengedwa kwa masiku 6 ndipo tsiku lililonse linali lamaola 24.

 Zoona: Baibulo limanena kuti Mulungu analenga zinthu zonse kale kwambiri. (Genesis 1:1) Ndiponso kutalika kwa nthawi imene Mulungu analengera zinthu zonse, imene yatchulidwa kuti masiku mu Genesis chaputala 1, sikunafotokozedwe. Ndipotu nthawi yonse imene Mulungu analengera dzikoli lapansi ndi kumwamba imatchulidwa kuti “tsiku.”​—Genesis 2:4.

 Zimene ena amakhulupirira: Baibulo limanena kuti Mulungu anayamba kulenga zomera asanalenge dzuwa kuti lizithandiza zomerazo.​—Genesis 1:​11, 16.

 Zoona: Baibulo limasonyeza kuti Mulungu analenga dzuwa, lomwe lili m’gulu la nyenyezi za “kumwamba,” zomera zisanalengedwe. (Genesis 1:1) Kuwala kochokera ku dzuwa kunayamba kuoneka padziko lapansi mkati mwa “tsiku” loyamba, lomwe linali nthawi yaitali kwambiri. Ndiyeno pa “tsiku” lachitatu, kuwala kwamphamvu kochokera kudzuwa kunafika padziko lapansi ndipo kukanatha kuthandiza zomera. (Genesis 1:​3-5, 12, 13) Zimenezi zitachitika dzuwa linayamba kuonekera bwinobwino padziko lapansi.​—Genesis 1:​16.

 Zimene ena amakhulupirira: Baibulo limanena kuti dzuwa limazungulira dziko lapansi.

 Zoona:Lemba la Mlaliki 1:5 limati: “Dzuwa limatuluka ndipo dzuwa limalowa, kenako limathamanga mwawefuwefu kupita kumalo ake kuti likatulukenso.” Komabe lembali likufotokoza zimene ife timaona padziko lapansi pano zokhudza kuyenda kwa dzuwa. Masiku ano anthu amanenabe kuti “dzuwa latuluka” ndiponso “dzuwa lalowa” ngakhale kuti amadziwa zoti dziko ndi limene limazungulira dzuwa.

 Zimene ena amakhulupirira: Baibulo limanena kuti dziko lapansi ndi lafulati.

 Zoona: M’Baibulo muli mawu akuti “kumalekezero a dziko lapansi.” Mawu amenewa sakutanthauza kuti dziko lapansi ndi lafulati kapena kuti lili ndi pothera. (Machitidwe 1:8) Zimenezi zikufanana ndi mawu ophiphiritsa akuti “kumalekezero anayi a dziko lapansi,” omwe amatanthauza dziko lonse lapansi. Masiku anonso, anthu amakonda kugwiritsa ntchito mawu akuti kum’mawa, kumadzulo, kumpoto ndi kum’mwera, mophiphiritsa.​—Yesaya 11:12; Luka 13:29.

 Zimene ena amakhulupirira: M’Baibulo muli mfundo yosonyeza kuti chingwe chokwanira kuzunguliza chinthu chinachake chozungulira ngati mpira, chingafunike kuchigawa patatu kuti chikwanire kudutsa pakati m’pakati pa chinthucho.

 Zoona: Miyezo ya “thanki yamkuwa” yomwe ili pa 1 Mafumu 7:23 ndi 2 Mbiri 4:2, ikusonyeza kuti pakamwa pa thankilo panali papakulu mikono 10, kuyeza modutsa pakati pa kamwayo. Ndiyeno ‘pankafunika chingwe chotalika mikono 30 kuti ayeze kuzungulira kwa thankiyo.’ Manambala a miyezoyi mwina sanali ndendende ngati mmene atchulidwira. N’kuthekanso kuti miyezoyi ndi yophatikiza miyezo ya kutalika kwa kunja ndi mkati mwa thankilo.