Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Baibulo Limatiuza

Zimene Baibulo Limatiuza

“Iyi ndi nkhani yofotokoza mmene kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwera.” (Genesis 2:4) Ndi mawu amenewa, Baibulo limafotokoza mwachidule zimene zinachitika kuti dziko lathuli likhalepo. Kodi zimene Baibulo limanenazi zimagwirizana ndi zimene sayansi imanena? Taonani zitsanzo zotsatirazi:

Pachiyambi: Kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwa

Kodi chilengedwe chakhala chilipo kuyambira kalekale?

Lemba la Genesis 1:1 limati: “Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”

Zisanafike zaka za m’ma 1950 asayansi ambiri odziwika bwino ankakhulupirira kuti chilengedwechi chilibe chiyambi. Koma chifukwa cha zomwe apeza posachedwapa, asayansi ambiri ayamba kuvomereza kuti chilengedwechi chinali ndi chiyambi.

Kodi dzikoli linkaoneka bwanji poyamba?

Lemba la Genesis 1:2, 9 limafotokoza kuti poyamba, dzikoli “linali lopanda maonekedwe enieni komanso lopanda kanthu” ndipo panali madzi okhaokha.

Mogwirizana ndi zimene apeza, asayansi amavomereza zimenezi masiku ano. Wasayansi wina dzina lake Patrick Shih analemba kuti mmene dzikoli linkayamba, “mumlengalenga munalibe mpweya wa okosijeni woti munthu n’kupuma . . . komanso linalibe maonekedwe enieni.” Magazini ina ya sayansi (Astronomy) inanena kuti: “Kafukufuku wa posachedwa anapeza kuti poyamba dzikoli linali ndi madzi okhaokha, ndipo mwina nthaka inkangooneka pang’ono.”

Kodi mumlengalenga munasintha bwanji n’kupita kwa nthawi?

Lemba la Genesis 1:3-5 limasonyeza kuti mmene kuwala kunkayamba kudutsa mlengalenga, kumene kunkachokera kuwalako sikunkaoneka padziko lapansi. Koma kenako dzuwa ndi mwezi zinayamba kuonekera padziko lapansi.​—Genesis 1:14-18.

Baibulo silinena kuti zamoyo zinalengedwa m’masiku 6 okhala ndi maola 24

Bungwe lina lochita kafukufuku linanena kuti poyamba kuwala kochepa kokha ndi komwe kunkatha kudutsa mlengalenga n’kufika padzikoli. Bungweli linanena kuti: “Dzikoli litangokhalapo kumene, linazunguliridwa ndi mpweya wa methane. Kenako mpweyawu unachoka ndipo kumwamba kunayamba kuoneka kwa buluu.”​—Smithsonian Environmental Research Center.

Kodi ndi zamoyo ziti zimene zinayambirira kupezeka padzikoli?

Lemba la Genesis 1:20-27 limanena kuti nsomba ndi zimene zinayamba kulengedwa kenako mbalame, nyama za pamtunda ndipo pomalizira pake anthu. Asayansi amakhulupirira kuti nsomba zitayamba kuoneka padzikoli, panatenga nthawi kuti nyama zionekere ndipo anthu anadzaonekera pambuyo pake.

Baibulo silinena kuti pakapita nthawi zinthu zamoyo sizingasinthe mmene zinapangidwira

Zimene Baibulo Silinena

Anthu ena amanena kuti zimene Baibulo limanena zimasiyana ndi zimene asayansi apeza masiku ano. Komatu nthawi zambiri, anthu amanena zimenezi chifukwa chosamvetsa zimene Baibulo limafotokoza.

Baibulo silinena kuti zinthu zakuthambo kapena dzikoli zakhalapo kwa zaka 6,000 zokha. Koma m’malomwake limangonena kuti dzikoli komanso zinthu zakuthambo zinalengedwa “pachiyambi.” (Genesis 1:1) Baibulo silinena kuti zimenezi zinachitika liti.

Baibulo silinena kuti zamoyo zinalengedwa m’masiku 6 okhala ndi maola 24

Koma m’malomwake, limagwiritsa ntchito mawu akuti “tsiku” ponena za nthawi yaitali. Mwachitsanzo, limanena kuti m’masiku 6 a kulenga otchulidwa mu Genesis chaputala 1, Mulungu analenga dzikoli komanso zamoyo. Ndiyeno limati zonsezi zinachitika mu “tsiku limene Yehova * Mulungu anapanga dziko lapansi ndi kumwamba.” (Genesis 2:4) Choncho tsiku lililonse pa “masiku” 6 amene ankakonza dzikoli komanso kulenga zamoyo, akhoza kutanthauza nthawi yaitali kwambiri.

Baibulo silinena kuti pakapita nthawi zinthu zamoyo sizingasinthe mmene zinapangidwira.

Buku la Genesis limafotokoza kuti nyama zinalengedwa “monga mwa mitundu yake.” (Genesis 1:24, 25) Mawu a m’Baibulo akuti “mitundu” si mawu a sayansi, koma zikuoneka kuti akutanthauza magulu osiyanasiyana a zamoyo. Ndipotu mtundu umodzi ungakhale ndi mitundu inanso ing’onoing’ono. Mawu amenewa akusonyeza kuti n’zotheka kuti zamoyo za “mtundu” umodzi, n’kupita kwa nthawi zizisintha n’kupanga mitundu ing’onoing’ono, mogwirizana ndi malo amene zikukhala.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Monga mmene taonera, Baibulo limafotokoza molondola komanso mosavuta kumva mmene zinthu zakuthambo zinayambira, mmene dziko lapansi linalili poyamba komanso mmene zamoyo zinayambira. Kodi ndiye mwina n’kutheka kuti Baibulo limatchulanso molondola amene analenga zinthu zimenezi? Buku lina linati: “Mfundo yakuti winawake wamphamvu kwambiri kuposa anthu ndi amene anachititsa kuti zamoyo zikhalepo, siikutsutsana kwenikweni ndi zimene asayansi apeza posachedwapa.” *​—Encyclopædia Britannica.

^ ndime 18 Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.

^ ndime 22 Buku la Encyclopædia Britannica siliikira kumbuyo zakuti zamoyo zinachita kulengedwa.