Pitani ku nkhani yake

Kodi Pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu mwa Mulungu M’modzi?

Kodi Pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu mwa Mulungu M’modzi?

Yankho la m’Baibulo

 Zipembedzo zambiri zachikhristu zimaphunzitsa kuti pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu mwa Mulungu M’modzi. Komabe, taonani zimene buku linalake (Encyclopædia Britannica) limanena: “M’Chipangano Chatsopano mulibe chiphunzitso chakuti pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu mwa Mulungu M’modzi . . . Chiphunzitsochi chinayamba pang’onopang’ono zaka mahandiredi ambiri zapitazo ngakhale kuti panali kutsutsana kwambiri.”

 Ndipo kunena mosapita m’mbali, palibe paliponse m’Baibulo pamene pamanena kuti pali milungu itatu mwa Mulungu m’modzi. Mwachitsanzo, taonani mavesi a m’Baibulo otsatirawa:

 Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.”—Deuteronomo 6:4.

 Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.”—Salimo 83:18.

 Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”—Yohane 17:3.

Mulungu alipo mmodzi yekha basi.”—1 Akorinto 8:6.

 N’chifukwa chiyani zipembedzo zambiri zachikhristu zimaphunzitsa kuti pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu mwa Mulungu M’modzi?