Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Yohane 1:1​—“Pachiyambi Panali Mawu”

Yohane 1:1​—“Pachiyambi Panali Mawu”

 “Pa chiyambi, panali wina wotchedwa Mawu, ndipo Mawuyo anali ndi Mulungu, komanso Mawuyo anali mulungu.”​—Yohane 1:1, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu ndiye Mulungu.​—Yohane 1:1, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Yohane 1:1

 Lembali limatiuza zinthu zokhudza moyo wa Yesu Khristu asanabwere padzikoli. (Yohane 1:14-17) M’vesi 14, dzina lakuti “Mawu” (kapena kuti ho loʹgos M’Chigiriki) ndi dzina laudindo. Dzinali limanena za udindo wa Yesu wouza ena malamulo komanso malangizo a Mulungu. Yesu anapitiriza kuuza ena mawu a Mulungu pa utumiki wake wapadzikoli komanso atabwerera kumwamba.​—Yohane 7:16; Chivumbulutso 1:1.

 Mawu oti “pa chiyambi” akunena za nthawi imene Mulungu anayamba kulenga zinthu ndipo analenga Mawuyo. Kenako, Mulungu anagwiritsa ntchito Mawuyo kuti polenga zinthu zina zonse. (Yohane 1:2, 3) Baibulo limanena kuti Yesu anali “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse” ndipo “kudzera mwa iye zinthu zina zonse zinalengedwa.”​—Akolose 1:15, 16.

 Mawu akuti “Mawuyo anali mulungu” akunena za mmene Yesu analili asanabwere padzikoli. Iye anali wofanana ndi Mulungu. Tingamufotokoze chonchi chifukwa choti anali Womulankhulira Mulungu komanso anali Mwana wake woyamba yemwe Mulungu anamugwiritsa ntchito polenga zinthu zina zonse.

Nkhani Yonse ya Yohane 1:1

 Buku la m’Baibulo la Yohane limafotokoza moyo komanso utumiki wa Yesu ali padzikoli. Mavesi oyamba am’chaputala choyamba amanena za moyo wa Yesu asanabwere padzikoli, ubwenzi wake wapadera ndi Mulungu komanso udindo wake wofunika pa zimene Mulungu amachita ndi anthu. (Yohane 1:1-18) Zimenezi zimatithandiza kumvetsa zimene Yesu ananena komanso kuchita pa utumiki wake wapadzikoli.​—Yohane 3:16; 6:38; 12:49, 50; 14:28; 17:5.

Maganizo Olakwika Okhudza Yohane 1:1

 Maganizo olakwika: Mawu omaliza a Yohane 1:1 ayenera kumasuliridwa kuti “Mawu ndiye Mulungu.”

 Zoona zake: Anthu ambiri omasulira Baibulo amamasulira vesili m’njira imeneyi, koma ena amalimasulira m’njira ina. M’Baibulo lakale la m’chilankhulo choyambirira, mawu oti “Mulungu” (kapena kuti the·osʹ m’Chigiriki) analembedwa mosiyana pamalo awiri am’vesili. Pamalo oyamba, mawu oti “Mulungu” ali ndi mperekezi wa m’Chigiriki, pomwe pamalo achiwiri palibe mperekezi. Akatswiri ambiri amanena kuti mfundo yoti pamalo achiwiri mawu oti the·osʹ alibe mperekezi ndi yofunika kwambiri. Mwachitsanzo, Baibulo lina (The Translator’s New Testament) limanena za mfundoyi kuti: “Kusowa kwa mperekezi kumasonyeza kuti mawu oti Theos (kapena kuti Mulungu) pamalo achiwiri ndi ongofotokoza mmene Mawuyo alili. Choncho akutanthauza kuti ‘Mawuyo anali wofanana ndi Mulungu.’” a Akatswiri ena b komanso Mabaibulo ena amagwirizana ndi zimenezi.​—Onani “ Yohane 1:1 M’Mabaibulo Ena.”

 Maganizo olakwika: Vesili limaphunzitsa kuti Mawuyo ndiye Mulungu Wamphamvuyonse.

 Zoona zake: Mawu oti “Mawuyo anali ndi Mulungu” amasonyeza kuti vesili likunena za anthu awiri. N’zosatheka kuti Mawu akhale “ndi Mulungu” ndipo pa nthawi imodzimodziyo akhalenso Mulungu Wamphamvuyonse. Mavesi ena am’chaputalachi amasonyezanso kuti Mawu si Mulungu Wamphamvuyonse. Vesi la Yohane 1:18 limanena kuti “palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse.” Koma anthu anaona Mawu, kapena kuti Yesu, chifukwa vesi la Yohane 1:14 limanena kuti “Mawu ameneyo anakhala ndi thupi la nyama ndi kukhala pakati pathu, ndipo tinaona ulemerero wake.”

 Maganizo olakwika: Mawuyo alibe chiyambi.

 Zoona zake: Mawu oti “pa chiyambi” pavesili sakunena za chiyambi cha Mulungu chifukwa Mulungu alibe chiyambi. Yehova c Mulungu anakhalapo “kuyambira kalekale mpaka kalekale.” (Salimo 90:1, 2) Koma Mawu, kapena kuti Yesu Khristu, anali ndi chiyambi. Iye ndi “woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.”​—Chivumbulutso 3:14.

 Maganizo olakwika: Kunena kuti Mawuyo ndi “mulungu” kumasonyeza kuti Mulungu si mmodzi yekha koma pali milungu ina imene tiyenera kulambira.

 Zoona zake: Mawu a Chigiriki akuti “Mulungu” kapena “mulungu” (the·osʹ) nthawi zambiri amafanana ndi mawu a Chiheberi akuti ʼel ndi ʼelo·himʹ, omwe amagwiritsidwa ntchito m’Malemba amene ambiri amati Chipangano Chakale. Akatswiri amati mawu a Chiheberiwa amatanthauza kuti “Wamphamvu” ndipo amagwiritsidwa ntchito ponena za Mulungu wamphamvuyonse, milungu ina komanso ngakhale anthu. (Salimo 82:6; Yohane 10:34) Mawuyo ndi amene Mulungu anamugwiritsa ntchito polenga zinthu zina zonse. Choncho tinganenedi kuti ndi wamphamvu. (Yohane 1:3) Kunena kuti Mawuyo anali “mulungu” kumagwirizana ndi ulosi wa mu Yesaya 9:6. Ulosiwu unaneneratu kuti wosankhidwa ndi Mulungu, kapena kuti Mesiya kapena Khristu, adzapatsidwa dzina lakuti “Mulungu Wamphamvu” (kapena kuti ʼEl Gib·bohrʹ m’Chiheberi) osati dzina lakuti “Mulungu Wamphamvuyonse” (kapena kuti ʼEl Shad·daiʹ m’Chiheberi limene likupezeka m’lemba la Genesis 17:1; 35:11; Ekisodo 6:3; ndi la Ezekieli 10:5).

 Baibulo siliphunzitsa kuti tiyenera kulambira milungu yambiri. Paja Yesu Khristu anena kuti: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.” (Mateyu 4:10) Baibulo limanenanso kuti: “Pakuti ngakhale ilipo yotchedwa ‘milungu,’ kaya kumwamba kapena padziko lapansi, ndipo n’zoona ilipodi ‘milungu’ yambiri ndi ‘ambuye’ ambiri, kwa ife Mulungu alipo mmodzi yekha basi amene ndi Atate. Iye ndi amene zinthu zonse zinachokera mwa iye, ndipo ifeyo ndife ake. Ndipo pali Ambuye mmodzi, Yesu Khristu, amene zinthu zonse zinakhalapo kudzera mwa iye, ndipo ifeyo kudzera mwa iyeyo.”​—1 Akorinto 8:5, 6.

 Yohane 1:1 M’Mabaibulo Ena

 “Pa chiyambi, panali Mawu. Mawuyo anali ndi Mulungu, komanso Mawuyo anali wofanana ndi mulungu.”​—The Bible​—An American Translation, 1935, womasuliridwa ndi J.M.P. Smith ndi E. J. Goodspeed.

 “Mawu analipo pa chiyambi, Mawuyo anali ndi Mulungu ndipo Mawuyo anali wofanana ndi Mulungu.”​—The Bible​—Containing the Old and New Testaments, 1950, womasuliridwa ndi James Moffatt.

 “Mawu analipo pa chiyambi, ndipo mawuyo anali ndi Mulungu komanso mawuyo anali mulungu.”​—The New Testament in an Improved Version, 1808, lokonzedwanso ndi Thomas Belsham, kuchokera ku Baibulo la Chipangano Chakale lomasuliridwa ndi William Newcome.

 “Pa chiyambi panali Mawu. Ndipo Mawuyo anali ndi Mulungu. Choncho Mawuyo anali wofanana ndi Mulungu.”​—The Authentic New Testament, 1958, lomasuliridwa ndi Hugh H. Schonfield

a The Translator’s New Testament, tsamba 451.

b Katswiri wina dzina lake Jason David BeDuhn ananena kuti kusowa kwa mperekezi kumachititsa kuti malo awiri omwe amapezeka mawu oti “Mulungu” akhale “osiyana kwambiri ngati mmene alili mawu a Chingelezi akuti ‘mulungu winawake’ ndi ‘Mulungu.’” Iye ananenanso kuti: “Pa Yohane 1:1, Mawuyo si Mulungu woona yekha, koma ndi mulungu winawake, kapena kuti wofanana ndi Mulungu.”​—Truth in Translation: Accuracy and Bias in English Translations of the New Testament, tsamba 115, 122 ndi 123.

c Yehova ndi dzina la Mulungu.​—Salimo 83:18..