Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?

Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?

Anthu oposa 2 biliyoni amanena kuti ndi Akhristu. Ambiri mwa anthu amenewa amapita m’matchalitchi amene amaphunzitsa zoti pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu mzimu woyera, ndipo zonsezi zimapanga Mulungu mmodzi. Kodi zinatheka bwanji kuti anthu ambiri azikhulupirira chiphunzitso chimenechi? Komanso kodi chimagwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa?

BAIBULO linamalizidwa kulembedwa patangopita zaka zochepa atumwi atamwalira. Koma chiphunzitso cha Utatu chinayamba kutchuka patadutsa zaka pafupifupi 200. Chiphunzitsochi chinayamba kutchuka m’chaka cha 325 C.E., pa msonkhano umene unachitika mumzinda wa Nicaea ku Asia Minor, komwe pano ndi ku Iznik, m’dziko la Turkey. Buku lina linanena kuti pa msonkhanowu, akuluakulu azipembedzo anagwirizana zokhazikitsa matanthauzo a ziphunzitso za matchalitchi, kuphatikizapo nkhani yakuti Mulungu ndiponso Khristu ndi ndani. Koma n’chifukwa chiyani iwo anaganiza zokambirana kuti Mulungu komanso Khristu ndi ndani pambuyo poti padutsa zaka 200 Baibulo litamalizidwa kulembedwa? Kodi ndiye kuti Baibulo silifotokoza bwinobwino za Mulungu komanso Yesu?—New Catholic Encyclopedia.

KODI YESU NDI MULUNGU?

Constantine atayamba kulamulira ufumu wonse wa Roma, anthu amene ankati ndi Akhristu anayamba kusiyana maganizo pa nkhani ya Yesu komanso Mulungu. Ena ankanena kuti Yesu ndi Mulungu pomwe ena ankati Yesu analengedwa ndi Mulungu. Pofuna kuthetsa nkhaniyi, Constantine analamula atsogoleri azipembedzo kuti akumane pamodzi ku Nicaea. Constantine sanachite zimenezi n’cholinga choti adziwe zoona zenizeni za nkhaniyi, koma ankangofuna kuti nkhani za chipembedzo zisagawanitse ufumu wake.

“Kwa ife Mulungu alipo mmodzi yekha basi.”—1 Akorinto 8:6

Choncho iye anapempha mabishopu kuti agwirizane chimodzi koma zinakanika. Kenako Constantine anauza anthu omwe anali pa msonkhanowo kuti angotsatira mfundo yoti Yesu ndi “munthu mmodzi” (homoousios) ndi Atate, yomwe inali yosamveka. Mfundo imeneyi inapangitsa kuti matchalitchi ambiri ayambe kukhulupirira Utatu. Pofika chakumapeto kwa zaka za m’ma 300 C.E., chiphunzitso cha Utatu chinali chitatchuka kwambiri ngati mmene chilili masiku ano ndipo pa nthawi imeneyi anthu anali atayamba kukhulupiriranso kuti mzimu woyera ndi mbali ya mulungu ameneyu.

N’CHIFUKWA CHIYANI NKHANIYI IKUKUKHUDZANI?

Yesu ananena kuti: “Olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa . . . ndi choonadi.” (Yohane 4:23) Choonadi chimenechi chimapezeka m’Baibulo. (Yohane 17:17) Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti Atate, Mwana komanso  mzimu woyera amapanga Mulungu mmodzi?

Choyamba, mawu akuti “Utatu” sapezeka m’Baibulo. Chachiwiri, Yesu sananenepo kuti ndi wofanana ndi Mulungu. Koma m’malomwake Yesu ankalambira Mulungu. (Luka 22:41-44) Umboni wachitatu ndi mmene Yesu ankaonera ophunzira ake. Yesu ataukitsidwa anatchula ophunzira ake kuti ndi “abale” ake. (Mateyu 28:10) Ngati Mulungu ndi Yesu ali ofanana, kodi zimenezi zikutanthauza kuti ophunzira a Yesu analinso abale ake a Mulungu Wamphamvuyonse? Ayi. Koma chifukwa chakuti ophunzira akewo ankakhulupirira Yesu, yemwe ndi Mwana wapadera kwambiri wa Mulungu, nawonso ankatchedwa ana a Mulungu. (Agalatiya 3:26) Taonani kusiyana pakati pa zimene Baibulo limanena ndi zimene atsogoleri azipembedzo anagwirizana pa msonkhano wa ku Nicaea.

Zimene anagwirizana:

“Timakhulupirira . . . mwa Ambuye mmodzi Yesu Khristu . . . kuti ndi munthu mmodzi ndi Atateyo, Mulungu wochokera kwa Mulungu, kuunika kochokera ku kuunika, Mulungu woona wochokera kwa Mulungu woona.”

Zimene Baibulo limanena:

  • “Atate ndi wamkulu kuposa ine [Yesu].”—Yohane 14:28.

  • “Ine [Yesu] ndikukwera kwa Atate wanga ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanu.”—Yohane 20:17.

  • “Kwa ife Mulungu alipo mmodzi yekha basi amene ndi Atate.”—1 Akorinto 8:6.

  • “Atamandike Mulungu amenenso ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.”—1 Petulo 1:3.

  • “Izi ndi zimene akunena Ame [Yesu], . . . woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.”Chivumbulutso 3:14. *

^ ndime 17 Buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? muli mutu wakuti: “Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?” ndi wakuti “Kodi Yesu Kristu Ndani?” Kuti mupeze bukuli mukhoza kupempha aliyense wa Mboni za Yehova kapena mukhoza kuliwerenga pa webusaiti ya www.pr418.com.