Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yomalizitsa Munthu Amene Akuvutika Kwambiri ndi Ululu?

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yomalizitsa Munthu Amene Akuvutika Kwambiri ndi Ululu?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo silifotokoza mwachindunji za nkhaniyi. a Koma zimene limanena zokhudza moyo ndi imfa zingatithandize kudziwa zoyenera kuchita. Kupha munthu ndi tchimo. Koma zimenezi sizikusonyeza kuti ndi bwino kutalikitsa moyo wa munthu amene watsala pang’ono kumwalira.

 Baibulo limanenanso kuti Mulungu ndi Mlengi wathu kutanthauza kuti iye ndi “kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9; Machitidwe 17:28) Mulungu amaona kuti moyo ndi wofunika kwambiri. N’chifukwa chake salola kuti munthu adziphe yekha kapena kupha munthu wina. (Ekisodo 20:13; 1 Yohane 3:15) Kuwonjezera pamenepo Baibulo limatilimbikitsa kuti tizisamala ndi zinthu zimene zingaike moyo wathu kapena wa anthu ena pangozi. (Deuteronomo 22:8) Choncho n’zodziwikiratu kuti Mulungu amafuna tiziona moyo kuti ndi wamtengo wapatali.

Bwanji ngati munthuyo akudwala kwambiri ndipo wafika poti sangachirenso?

 Baibulo sililola kupha munthu ngakhale zitadziwikiratu kuti sachira. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zomwe zinachitikira Mfumu Sauli. Nthawi ina atavulazidwa kwambiri kunkhondo, anauza wantchito wake kuti amumalizitse. (1 Samueli 31:3, 4) Koma wantchito wakeyo anakana. Munthu wina ndi amene anapha Sauli ponamizira kuti amakwaniritsa zomwe mfumuyi imafuna. Davide anadzudzula munthuyu ndipo ananena kuti anali ndi mlandu wa magazi. Zimene Davide anachitazi zinasonyeza mmene Mulungu amaonera nkhaniyi.​—2 Samueli 1:6-16.

Kodi kutalikitsako moyo wa munthu kuli ndi vuto lililonse?

 Ngati zadziwikiratu kuti munthu sachira, Baibulo silivomereza zotalikitsako moyo wa munthuyo. Komabe zomwe limanena zingatithandize kudziwa zoyenera kuchita pa nkhaniyi. Imfa ndi mdani wathu wamkulu komanso chizindikiro choti anthufe ndife ochimwa. (Aroma 5:12; 1 Akorinto 15:26) Ngakhale kuti sitiyenera kutalikitsa moyo, sitifunikanso kuopa imfa chifukwa Mulungu anatilonjeza kuti adzaukitsa amene anamwalira. (Yohane 6:39, 40) Munthu amene amalemekeza moyo angafufuze chithandizo choyenera cha kuchipatala. Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti munthuyo akufunika kusankha chithandizo cha kuchipatala chomwe cholinga chake ndi kutalikitsa moyo ngakhale zitadziwikiratu kuti afa.

Kodi Mulungu sangakhululukire munthu amene wadzipha?

 Baibulo silinena kuti kudzipha kuli m’gulu la machimo osakhululukidwa. Ngakhale kuti n’zoona kuti kudzipha ndi tchimo lalikulu, b Mulungu amamvetsa zinthu zimene zingapangitse kuti munthu adziphe monga matenda a kusokonezeka maganizo komanso mavuto a chibadwa. (Salimo 103:13, 14) M’Baibulo muli mawu omwe amalimbikitsa anthu omwe ali ndi vuto la maganizo. Komanso Baibulo limanena kuti “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15) Zimenezi zikusonyeza kuti pali chiyembekezo choti anthu omwe analakwitsa zinthu zikuluzikulu monga kudzipha, akhoza kudzaukitsidwa.

a Dikishonale ina inanena kuti “kumalizitsa munthu amene akuvutika ndi ululu kumatanthauza kupha munthu amene akudwala kwambiri kapena amene anavulala modetsa nkhawa ndi cholinga choti munthuyo asavutike kwambiri ndi ululu.” (Merriam-Webster Learner’s Dictionary) Nthawi zina madokotala amatha kupereka mankhwala omalizitsira munthu ngati njira yothandizira munthu amene akudwalayo.

b Nkhani zochepa zotchulidwa m’Baibulo za anthu omwe anadzipha, zimasonyeza kuti anthuwo sanali paubwenzi ndi Mulungu.​—2 Samueli 17:23; 1 Mafumu 16:18; Mateyu 27:3-5.