Pitani ku nkhani yake

Kodi Yesu Ankaoneka Bwanji?

Kodi Yesu Ankaoneka Bwanji?

Yankho la m’Baibulo

 Palibe amene angafotokoze bwinobwino za mmene Yesu ankaonekera chifukwa Baibulo silifotokoza za maonekedwe ake. Zimenezi zikusonyeza kuti kudziwa mmene Yesu ankaonekera n’kosafunika kwenikweni. Komabe, mfundo zina zimene Baibulo limafotokoza zimatithandiza kudziwa mmene Yesu ankaonekera.

  •   Mmene ankaonekera: Yesu anali Myuda ndipo ayenera kuti anatengera mmene mayi ake ankaonekera. (Aheberi 7:14) Koma sikuti anali ndi maonekedwe osiyana ndi anthu ena moti nthawi ina iye anayenda kuchoka ku Galileya mpaka kukafika ku Yerusalemu anthu osamuzindikira. (Yohane 7:10, 11) Ndipotu mmene iye ankaonekera, sankasiyana kwambiri ndi ophunzira ake. Mwachitsanzo, Yudasi Isikariyoti anauza khamu lalikulu la anthu amene ankafuna kugwira Yesu kuti awapatsa chizindikiro choti amudziwe.​—Mateyu 26:47-49.

  •   Tsitsi: N’zodziwikiratu kuti Yesu sankasunga tsitsi lalitali chifukwa Baibulo limati “ngati mwamuna ali ndi tsitsi lalitali, zimenezi n’zochititsa manyazi kwa iye.”​—1 Akorinto 11:14.

  •   Ndevu: Yesu ankasunga ndevu chifukwa ankatsatira lamulo lachiyuda lomwe linkanena kuti amuna ‘asamamete ndiponso kudula nsonga za ndevu zawo.’ (Levitiko 19:27; Agalatiya 4:4) Komanso Baibulo linatchula ndevu za Yesu pamene linkafotokoza za ulosi woti adzazunzidwa.​—Yesaya 50:6.

  •   Thupi: Pali maumboni ambiri osonyeza kuti Yesu anali wamphamvu. Pa nthawi ya utumiki wake, iye ankayenda maulendo ataliatali. (Mateyu 9:35) Kawiri konse, iye anayeretsa kachisi pogubuduza matebulo a osintha ndalama ndipo nthawi ina anatulutsa m’kachisi ziweto ndi chikwapu. (Luka 19:45, 46; Yohane 2:14, 15) Buku lina limati: “Mabuku ambiri ofotokoza za ntchito yolalikira imene ankagwira amasonyeza kuti [Yesu] anali wamphamvu komanso wathanzi.”​—McClintock and Strong’s Cyclopedia, Volume IV, tsamba 884.

  •   Nkhope: Yesu anali wokoma mtima komanso wachifundo ndipo n’zosakayikitsa kuti nkhope yake inkaoneka mogwirizana ndi makhalidwe amenewa. (Mateyu 11:28, 29) Anthu osiyanasiyana ankafunitsitsa kuti Yesu awathandize komanso kuwalimbikitsa. (Luka 5:12, 13; 7:37, 38) Ngakhalenso ana aang’ono ankacheza naye momasuka.​—Mateyu 19:13-15; Maliko 9:35-37.

Zimene anthu ena amanena zokhudza mmene Yesu ankaonekera

 Zimene anthu ena amanena: Ambiri amanena kuti Yesu ayenera kuti anali munthu wakuda chifukwa choti buku la Chivumbulutso limayerekezera tsitsi lake ndi ubweya komanso miyendo yake ndi “mkuwa woyengedwa bwino.”​—Chivumbulutso 1:14, 15.

 Zoona zake: Buku la Chivumbulutso limafotokoza nkhani zambiri pogwiritsa ntchito “zizindikiro.” (Chivumbulutso 1:1) Choncho m’bukuli, tsitsi la Yesu komanso miyendo yake zikuimira makhalidwe amene iye anali nawo ataukitsidwa, osati maonekedwe ake pamene anali padzikoli. Ponena kuti ‘mutu ndi tsitsi lake zinali zoyera ngati ubweya wa nkhosa, woyera kwambiri kuti mbee,’ lemba la Chivumbulutso 1:14, limanena za mtundu osati mmene tsitsi limamvekera munthu akaligwira. Izi zikusonyeza kuti Yesu ali ndi nzeru chifukwa choti wakhalapo kwa zaka zambiri. (Chivumbulutso 3:14) Choncho lembali likungonena maonekedwe a tsitsi la Yesu osati mmene lingamvekere mukalikhudza.

 Miyendo ya Yesu inkaoneka ngati “mkuwa woyengedwa bwino ukamanyezimira m’ng’anjo.” (Chivumbulutso 1:15) Komanso nkhope yake “inali yowala ngati dzuwa limene likuwala kwambiri.” (Chivumbulutso 1:16) Popeza kuti palibe munthu amene khungu lake lingaoneke chonchi, masomphenyawa ndi ophiphiritsira. Akuimira Yesu yemwe anali ataukitsidwa monga “amene amakhala m’kuwala kosafikirika.”​—1 Timoteyo 6:16.

 Zimene anthu ena amanena: Yesu anali wofooka komanso wopanda mphamvu.

 Zoona zake: Yesu sanali munthu wofooka. Mwachitsanzo, iye sanaope kudzidziwikitsa kwa khamu la anthu lomwe linabwera kudzamugwira. (Yohane 18:4-8) Yesu ayeneranso kuti anali munthu wamphamvu chifukwa ntchito ya ukalipentala imene ankagwira, ankagwiritsa ntchito zipangizo zofuna mphamvu.​—Maliko 6:3.

 Koma, nanga n’chifukwa chiyani Yesu ankafunika kuthandizidwa kunyamula mtengo wake wozunzikirapo? Ndipo n’chifukwa chiyani anafa mofulumira kusiyana ndi anthu ena amenenso anapachikidwa naye limodzi? (Luka 23:26; Yohane 19:31-33) Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, thupi lake linafooka kwambiri. Izi zinachitika chifukwa choti sanagone usiku wonse komanso anali ndi nkhawa kwambiri. (Luka 22:42-44) Ayuda anali atamuchitira nkhanza usiku wonse, ndipo m’mawa wake Aroma anayambanso kumuzunza. (Mateyu 26:67, 68; Yohane 19:1-3) Zinthu ngati zimenezi ziyenera kuti ndi zomwe zinapangitsa kuti afe mofulumira.

 Zimene anthu ena amanena: Yesu ankangokhala wachisoni komanso wosasangalala nthawi zonse.

 Zoona zake: Yesu anasonyeza bwino makhalidwe a Atate wake wakumwamba Yehova, yemwe Baibulo limamutchula kuti ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteyo 1:11; Yohane 14:9) Ndipotu Yesu ankaphunzitsa anthu zimene angachite kuti akhale osangalala. (Mateyu 5:3-9; Luka 11:28) Mfundo zimenezi zikusonyeza kuti nthawi zonse nkhope yake inkaoneka yosangalala.