Pitani ku nkhani yake

Kodi Nkhani Zokhudza Moyo wa Yesu Zinalembedwa Liti?

Kodi Nkhani Zokhudza Moyo wa Yesu Zinalembedwa Liti?

Yankho la m’Baibulo

 Ponena za nkhani imene analemba yokhudza moyo wa Yesu, mtumwi Yohane anati: “Munthu amene anaona zimenezo akuchitira umboni, ndipo umboni wakewo ndi woona. Munthu ameneyu akudziwa kuti amanena zoona, kuti inunso mukhulupirire.”—Yohane 19:35.

 Pali chifukwa chinanso chimene tiyenera kukhulupirira nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino zimene zinalembedwa ndi Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane. Chifukwa chake n’chakuti iwo analemba nkhanizo pa nthawi imene anthu ambiri omwe anaona ndi maso zimene analembazo, anali adakali moyo. Malinga ndi maumboni ena, buku la Uthenga Wabwino la Mateyu linalembedwa mu 41 C.E., patangopita zaka 8 zokha kuchokera pamene Khristu anamwalira. Akatswiri ena a Baibulo amati bukuli linalembedwa nthawi ina m’tsogolo. Komabe, pafupifupi akatswiri onse a Baibulo amavomereza kuti mabuku onse a Malemba Achigiriki (Chipangano Chatsopano) analembedwa m’nthawi ya atumwi.

 Panali anthu ambiri omwe analipo pamene Yesu anali ndi moyo padziko lapansi, pa nthawi imene anaphedwa ndiponso pamene anaukitsidwa. Anthu amenewa akanatha kutsutsa nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino zikanakhala kuti nkhanizo sizinali zolondola. Mwachitsanzo, pulofesa Frederick F. Bruce ananena kuti: “Umboni wamphamvu pa nkhani imeneyi ndi zimene atumwi ananena polalikira. Iwo ankadziwa zoti anthu amene ankamvetserawo ankadziwanso zinthu zokhudza Yesu zimene atumwiwo ankalalikira. N’chifukwa chake iwo atanena kuti ‘ife ndife mboni za choonadi chimenechi,’ ananenanso kuti ‘monga mmene inunso mukudziwira’ (Machitidwe 2:22).”