Pitani ku nkhani yake

Kodi Nkhani ya Moyo wa Yesu Imene Ili M’Baibulo Ndi Yolondola?

Kodi Nkhani ya Moyo wa Yesu Imene Ili M’Baibulo Ndi Yolondola?

Yankho la m’Baibulo

 Luka, amene analemba nawo Baibulo, ananena zokhudza moyo wa Yesu kuti: “Ndafufuza zinthu zonse mosamala kwambiri kuchokera pa chiyambi.”—Luka 1:3.

 Anthu ena amanena kuti nkhani ya moyo wa Yesu imene ili m’mabuku a Uthenga Wabwino, inasinthidwa nthawi inayake cha m’ma 300 C.E. Mabuku a Uthenga Wabwino amenewa analembedwa ndi Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane, anthu omwe anakhalapo pa nthawi yofanana ndi imene Yesu anali padziko lapansi.

 Komabe, chidutswa cha Uthenga Wabwino wa Yohane chinapezeka ku Egypt chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900. Masiku ano, chidutswa chimenechi chimadziwika ndi dzina lakuti Papyrus Rylands 457 (P52) ndipo chikusungidwa mulaibulale ina yotchedwa John Rylands Library mumzinda wa Manchester, ku England. Pachidutswapa pali mawu amene ali pa Yohane 18:31-33, 37, 38 m’Mabaibulo a masiku ano.

 Chidutswa chimenechi ndi chakale kwambiri pa zidutswa zonse za Malemba Achigiriki (Chipangano Chatsopano) zimene zikudziwika masiku ano. Akatswiri ambiri amakhulupirira kuti mpukutu wa chidutswachi unalembedwa cha mu 125 C.E., patangopita zaka pafupifupi 25 zokha kuchokera pamene Yohane analemba buku lake la Uthenga Wabwino. Mawu amene ali pachidutswachi akufanana kwambiri ndi mawu amene analembedwa m’mipukutu ina yomwe inalembedwa chaka cha 125 C.E. chitadutsa.