Pitani ku nkhani yake

Kodi Yesu Anafera Pamtanda?

Kodi Yesu Anafera Pamtanda?

Yankho la m’Baibulo

 Anthu ambiri amaona kuti mtanda ndi chizindikiro chachikulu cha Chikhristu. Komabe Baibulo silifotokoza kuti chinthu chimene Yesu anapachikidwapo chinkaoneka bwanji, choncho palibe amene anganene motsimikiza mmene chinkaonekera. Ngakhale izi zili choncho, Baibulo limapereka umboni wosonyeza kuti Yesu sanafere pamtanda koma anafera pamtengo wowongoka.

 Baibulo likamanena za chinthu chimene Yesu anapachikidwapo, limagwiritsa ntchito mawu achigiriki akuti stau·rosʹ. (Mateyu 27:40; Yohane 19:17) Ngakhale kuti nthawi zambiri anthu amamasulira mawuwa kuti “mtanda,” akatswiri ambiri amaphunziro amavomereza kuti tanthauzo lake lenileni ndi “mtengo wowongoka.” a Buku lina limanena kuti mawu akuti stau·rosʹ “satanthauza mitengo iwiri yopingasa.”​—Critical Lexicon and Concordance to the English and Greek New Testament.

 Baibulo limagwiritsanso ntchito mawu ena achigiriki akuti xyʹlon m’malo mwa stau·rosʹ. (Machitidwe 5:30; 1 Petulo 2:24) Mawu amenewa amatanthauza “mtengo woongoka,” kapena “thabwa.” b Ponena za nkhaniyi, Baibulo lina limanena kuti: “M’Chigiriki chimene chinagwiritsidwa ntchito polemba Chipangano Chatsopano mulibe mawu aliwonse otanthauza mtanda.”​—The Companion Bible.

Kodi Mulungu amavomereza kugwiritsa ntchito mtanda pomulambira?

Crux simplex​—mawu achilatini amene amatanthauza mtengo umodzi ankagwiritsidwa ntchito ponena za mtengo umene ankapachikapo zigawenga.

 Ngakhale kuti sitikudziwa bwinobwino mmene chinthu chimene Yesu anapachikidwapo chinkaonekera, mfundo zotsatirazi komanso mavesi a m’Baibulowo zikusonyeza kuti sitikuyenera kugwiritsa ntchito mtanda polambira.

  1.   Mulungu safuna anthu azimulambira pogwiritsa ntchito zithunzi kapena zizindikiro monga mtanda. Mulungu analamula Aisiraeli kuti asamagwiritse ntchito “chifaniziro cha chinthu chilichonse” polambira. Akhristunso amalamulidwa kuti azipewa “kupembedza mafano.”​—Deuteronomo 4:​15-19; 1 Akorinto 10:14.

  2.   Akhristu oyambirira sankagwiritsa ntchito mtanda polambira. c Zimene atumwi ankaphunzitsa komanso kuchita zimapereka chitsanzo chimene Achikhristu onse ayenera kutsatira.​—2 Atesalonika 2:15.

  3.   Anthu akunja ndi amene anayambitsa kugwiritsa ntchito mtanda polambira. d Patadutsa zaka mahandiredi ambiri Yesu atamwalira, matchalitchi anasiya kutsatira zimene Yesuyo ankaphunzitsa. Zimenezi zinapangitsa kuti anthu amene ankalowa kumene m’matchalitchi “aziloledwa kuyambiranso kugwiritsa ntchito zizindikiro komanso zifaniziro zawo zachikunja,” monga mtanda. (The Expanded Vine’s Expository Dictionary of New Testament Words) Komabe Baibulo sililola kuti Akhristu azigwiritsa ntchito zizindikiro zachikunja pofuna kukopa anthu kuti alowe Chikhristu.​—2 Akorinto 6:17.

a Onani New Bible Dictionary, Third Edition, lokonzedwanso ndi D. R. W. Wood, tsamba 245; Theological Dictionary of the New Testament, Volume VII, tsamba 572; The International Standard Bible Encyclopedia, Revised Edition, Volume 1, tsamba 825; ndi The Imperial Bible-Dictionary, Volume II, tsamba 84.

b Onani buku lakuti The Expanded Vine’s Expository Dictionary of New Testament Words, tsamba 1165; komanso A Greek-English Lexicon, lolembedwa ndi Liddell ndi Scott, Ninth Edition, tsamba 1191 ndi​1192; ndiponso Theological Dictionary of the New Testament, Volume V, tsamba 37.

c Onani Encyclopædia Britannica, 2003, pamawu akuti “Cross”; The Cross​—Its History and Symbolism tsamba 40; ndiponso The Companion Bible, Oxford University Press, appendix 162, tsamba 186.

d Onani The Encyclopedia of Religion, Volume 4, tsamba 165; The Encyclopedia Americana, Volume 8, tsamba 246; ndiponso Symbols Around Us, tsamba 205 mpaka 207.