Pitani ku nkhani yake

Kodi Tiyenera Kulambira Mafano?

Kodi Tiyenera Kulambira Mafano?

Yankho la m’Baibulo

 Ayi. Buku lina linanena zokhudza malamulo amene Mulungu anapatsa mtundu wa Isiraeli. Bukulo linati: “Nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo zimasonyeza kuti anthu amene ankalambira Mulungu m’njira yovomerezeka sankagwiritsa ntchito mafano.” (New Catholic Encyclopedia) Taonani mavesi a m’Baibulo otsatirawa:

  •   “Usadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso cham’madzi a padziko lapansi. Usaziweramire kapena kuzitumikira, chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha.” (Ekisodo 20:​4, 5) Popeza Mulungu amafuna kuti ‘tizidzipereka kwa iye yekha,’ sasangalala tikamalambira mafano, zithunzi kapena zinthu zina.

  •   “Sindidzapereka . . . ulemerero wanga kwa zifaniziro zogoba.” (Yesaya 42:8) Mulungu amakana kumulambira pogwiritsa ntchito mafano. Aisiraeli atamulambira pogwiritsa ntchito fano la mwana wa ng’ombe, Mulungu anawauza kuti zimene anachitazo ndi “tchimo lalikulu.”​—Ekisodo 32:​7-9, Easy-to-Read Version.

  •   “Tisaganize kuti Mulunguyo ali ngati golide, siliva, mwala kapena chilichonse chosemedwa mwa luso ndi nzeru za munthu.” (Machitidwe 17:29) Mosiyana ndi anthu achikunja amene amalambira pogwiritsa ntchito mafano ‘osemedwa mwa luso ndi nzeru za munthu,’ Baibulo limanena kuti Akhristu ayenera “kuyenda mwa chikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso.”​—2 Akorinto 5:7.

  •   “Pewani mafano.” (1 Yohane 5:21) Malamulo opezeka m’Baibulo opita kwa mtundu wa Isiraeli komanso kwa Akhristu amanena mosapita m’mbali kuti zimene anthu ena amaphunzitsa zakuti Mulungu amavomereza kugwiritsa ntchito mafano pomulambira n’zabodza.