Pitani ku nkhani yake

Kodi Nambala ya 666 Imatanthauza Chiyani?

Kodi Nambala ya 666 Imatanthauza Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 M’buku lomaliza la m’Baibulo, nambala ya 666, ikuimira nambala kapena kuti dzina la chilombo cha mitu 7 ndi nyanga 10, chomwe chikutuluka m’nyanja. (Chivumbulutso 13:​ 1, 17, 18) Chilombo chimenechi chikuimira maulamuliro a ndale padziko lonse lapansi amene akulamulira “anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, chinenero chilichonse ndi dziko lililonse.” (Chivumbulutso 13:7) Nambala ya 666 imasonyeza kuti Mulungu amaona kuti maulamuliro andale alephereratu kulamulira anthu. N’chifukwa chiyani tikutero?

  Dzinali lili ndi tanthauzo. Mayina amene Mulungu amapereka amakhala ndi tanthauzo. Mwachitsanzo iye anapereka dzina kwa mtumiki wake kuti akhale Abulamu lomwe limatanthauza “Tate Wokwezeka.” Kenako anam’patsa dzina lakuti Abulahamu lomwe limatanthauza “Tate wa Mitundu Yambiri.” Pa nthawi imeneyi Mulungu anamulonjeza kuti adzakhala “tate wa mitundu yambiri.” (Genesis 17:5) Mofanana ndi zimenezi, chilombochi Mulungu anachipatsa dzina kapena kuti nambala ya 666 n’cholinga choti zitithandize kumvetsa makhalidwe a chilombochi.

  Nambala ya 6 imaimira chinthu choperewera. Nthawi zambiri manambala otchulidwa m’Baibulo amaimira zinthu zina zake. Mwachitsanzo nambala ya 7 imaimira chinthu chokwanira kapena chinthu chabwino. Ndipo nambala ya 6 yomwe ndi yoperewera poyerekezera ndi nambala ya 7, ingasonyeze kuti chinthu chinachake ndi chosakwanira kapena choperewera m’maso mwa Mulungu. Nambalayi ingaimirenso anthu amene ndi adani a Mulungu.​—1 Mbiri 20:6; Danieli 3:1.

  Kubwereza katatu kumatanthauza kutsindika. Baibulo nthawi zina limatsindika nkhani inayake poitchula katatu. (Chivumbulutso 4:8; 8:​ 13) Ndiyeno tinganene kuti nambala ya 666 ikutsindika mwamphamvu mmene Mulungu amaonera kuti maulamuliro onse andale ndi operewera. Zili choncho chifukwa chakuti maulamuliro andalewa alephera kukhazikitsa bata ndi mtendere weniweni padzikoli. Ndipotu ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzakwanitse kuchita zinthu zimenezi.

Chizindikiro cha chilombo

 Baibulo limanena kuti anthu amalandira “chizindikiro cha chilombo” chifukwa chakuti amachitsatira “pochita nacho chidwi,” mpaka amafika pochilambira. (Chivumbulutso 13:​ 3,  4; 16:2) Anthu amalambira chilombochi akamalemekeza kwambiri dziko lawo, zizindikiro zoimira dziko lawo kapena asilikali a dziko lawo. Buku lina lofotokoza nkhani za chipembedzo limanena kuti: “Masiku ano anthu ambiri amakonda kwambiri dziko lawo, ndipo zimenezi zili ngati chipembedzo chawo.” aThe Encyclopedia of Religion states.

 Kodi anthu akuikidwa bwanji chizindikiro cha chilombo padzanja lamanja kapena pamphumi pawo? (Chivumbulutso 13:16) Pofotokoza zokhudza chilamulo chimene anapatsa mtundu wa Isiraeli, Mulungu ananena kuti: “Muwamange monga chizindikiro padzanja lanu, ndipo akhale ngati chomanga pamphumi panu.” (Deuteronomo 11:18) Apatu Mulungu sankatanthauza kuti Aisiraeli ankafunikadi kumamanga manja komanso zipumi zawo. Koma ankatanthauza kuti mawu ake adzawathandiza kuti zochita zawo zonse komanso maganizo awo onse azigwirizana ndi chilamulocho. Choncho nambala ya 666 sikuti imachita kuonekera pachilombocho koma imaimira anthu onse amene amalola kuti maulamuliro andale azitsogolera zochita zawo. Apa zikuonekeratu kuti anthu onse amene ali ndi chizindikiro cha chilombochi amatsutsana ndi Mulungu.​—Chivumbulutso 14:9, 10; 19:19-​21.

a Kuti mumve zambiri werengani buku lakuti, Nationalism in a Global Era, tsamba 134; ndi Nationalism and the Mind: Essays on Modern Culture, tsamba 94.