Pitani ku nkhani yake

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Mumachita Mwambo wa Mgonero wa Ambuye Mosiyana ndi Zipembedzo Zina?

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Mumachita Mwambo wa Mgonero wa Ambuye Mosiyana ndi Zipembedzo Zina?

Ifeyo timayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo pochita mwambo wa “chakudya chamadzulo cha Ambuye,” womwe umadziwikanso ndi dzina lakuti “mgonero wa Ambuye,” kapena kuti Chikumbutso cha imfa ya Yesu. (1 Akorinto 11:20; Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Koma zinthu zambiri zimene zipembedzo zina zimachita komanso kukhulupirira zokhudza mwambowu sizichokera m’Baibulo.

Cholinga chake

Cholinga chochitira mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye ndi kukumbukira Yesu ndiponso kusonyeza kuti timayamikira nsembe imene anapereka chifukwa cha ife. (Mateyu 20:28; 1 Akorinto 11:24) Koma sikuti munthu amakhululukidwa machimo ake chifukwa chochita mwambowu. a Baibulo limanena kuti munthu amakhululukidwa machimo ake akamakhulupirira Yesu osati chifukwa chochita mwambo winawake wachipembedzo.—Aroma 3:25; 1 Yohane 2:1, 2.

Kodi tiyenera kuchita kangati?

Yesu anauza ophunzira ake kuti azichita mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye koma sanawauze kuti azichita kangati. (Luka 22:19) Anthu ena amaona kuti ayenera kuchita mwambowu kamodzi pa mwezi, ena kamodzi pa mlungu, ena kamodzi pa tsiku, pomwe ena amaona kuti ayenera kuchita kangapo pa tsiku. Pali enanso omwe amaona kuti angachite mwambowu mobwerezabwereza mmene angafunire. b Ngakhale zili choncho, pali mfundo zina zimene tiyenera kuziganizira.

Yesu anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye pa tsiku limene Ayuda ankachita Pasika. Iye anamwaliranso tsiku lomwelo. (Mateyu 26:1, 2) Koma sikuti zimenezi zinangochitika mwangozi. Tikutero chifukwa chakuti Baibulo limayerekezera nsembe ya Yesu ndi nkhosa imene ankagwiritsa ntchito pa tsiku la Pasika. (1 Akorinto 5:7, 8) Ayuda ankachita Pasika kamodzi pa chaka. (Ekisodo 12:1-6; Levitiko 23:5) Choncho Akhristu oyambirira ankachita mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Yesu kamodzi pa chaka. c Nawonso a Mboni za Yehova amachita zimenezi.

Tsiku komanso nthawi

Nthawi imene Yesu anayambitsa mwambowu imatithandizanso kudziwa tsiku ndiponso nthawi imene tiyenera kuchita mwambo wa Chikumbutso. Iye anachita zimenezi pa Nisani 14 dzuwa litalowa m’chaka cha 33 C.E. (Mateyu 26:18-20, 26) Tsiku limeneli ndi la m’kalendala yoyendera mwezi imene Ayuda ankagwiritsa ntchito. A Mboni amachitabe mwambo wa Chikumbutso pa tsiku limeneli chaka chilichonse ngati mmene Akhristu oyambirira ankachitira. d

Ngakhale kuti mu 33 C.E. tsiku la Nisani 14 linali Lachisanu, tsikuli silikhala Lachisanu chaka chilichonse. Ifeyo timapeza tsiku limene likugwirizana ndi tsiku la Nisani 14 potsatira njira imene Ayuda ankagwiritsa ntchito nthawi ya Yesu, m’malo motsatira njira imene Ayuda a masiku ano amagwiritsa ntchito. e

Mkate ndi vinyo

Pamene ankayambitsa mwambo watsopanowu, Yesu anagwiritsa ntchito mkate wopanda chofufumitsa ndiponso vinyo wofiira zimene zinatsala pa chakudya cha Pasika. (Mateyu 26:26-28) Nafenso timagwiritsa ntchito mkate wopanda chofufumitsa komanso wopanda zinthu zina zokometsera. Timagwiritsanso ntchito vinyo wofiira wosathira zowonjezera mphamvu kapena zokometsera.

Zipembedzo zina zimagwiritsa ntchito mkate wothira zofufumitsa kapena yisiti, komatu nthawi zambiri Baibulo limagwiritsa ntchito zofufumitsa kuimira uchimo ndiponso chinyengo. (Luka 12:1; 1 Akorinto 5:6-8; Agalatiya 5:7-9) N’chifukwa chake mkate wopanda zofufumitsa kapena wosathira zinthu zina zokometsera uli woyenera kuimira thupi la Yesu, lomwe ndi lopanda uchimo. (1 Petulo 2:22) Ena amagwiritsa ntchito juwisi wa mphesa m’malo mwa vinyo, koma izi si zogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Matchalitchi ena amachita zimenezi chifukwa cha chikhulupiriro chawo cholakwika chakuti Baibulo limaletsa kumwa mowa.—1 Timoteyo 5:23.

Mkate ndi vinyo ndi zizindikiro chabe

Mkate ndi vinyo zimene zimagwiritsidwa ntchito pa Chikumbutso ndi zizindikiro chabe za thupi ndiponso magazi a Khristu. Zizindikirozi sizisintha mozizwitsa n’kukhala thupi ndiponso magazi enieni ngati mmene ena amaganizira. Tiyeni tione chifukwa chake tikunena choncho.

  • Ngati Yesu akanauza ophunzira ake kuti amwe magazi ake enieni, akanakhala kuti akuwauza kuti aphwanye lamulo la Mulungu loletsa kumwa magazi. (Genesis 9:4; Machitidwe 15:28, 29) Koma Yesu sakanauza anthu kuti achite zinthu zotsutsana ndi lamulo la Mulungu losonyeza kuti magazi ndi opatulika.—Yohane 8:28, 29.

  • Ngati pamwambowu atumwi akanakhala kuti ankamwa magazi enieni a Yesu, iye sakananena kuti magazi anga “adzakhetsedwa,” zomwe zikusonyeza kuti anali asanapereke nsembe yake.—Mateyu 26:28.

  • Yesu anapereka nsembe yake “kamodzi kokha.” (Aheberi 9:25, 26) Koma ngati pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, mkate ndi vinyo zimasintha n’kukhala thupi ndi magazi ake enieni ndiye kuti nsembeyo imaperekedwa mobwerezabwereza ndi anthu amene amadya zizindikirozo.

  • Yesu anati: “Muzichita zimenezi pondikumbukira,” osati “pondipereka nsembe.”1 Akorinto 11:24.

Anthu ena amakhulupirira kuti mkate ndi vinyo zimasintha n’kukhala thupi ndi magazi enieni a Yesu chifukwa cha malemba ena a m’Baibulo. Mwachitsanzo, Mabaibulo ambiri amamasulira mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 26:28 kuti: “Vinyoyu ndi magazi anga.” Komabe mawu amenewa akhoza kumasuliridwanso kuti: “Vinyoyu akuimira magazi anga.” f Choncho apa Yesu anagwiritsa ntchito fanizo ngati mmene ankachitira nthawi zambiri.—Mateyu 13:34, 35.

Kodi ndi ndani amene ayenera kudya zizindikirozi?

A Mboni za Yehova akamachita mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, anthu ochepa okha ndi amene amadya mkate komanso kumwa vinyo. Kodi n’chifukwa chiyani zili choncho?

Pamene Yesu anakhetsa magazi ake, anayambitsa “pangano latsopano” lomwe linalowa m’malo mwa pangano lakale la pakati pa Yehova Mulungu ndi Aisiraeli. (Aheberi 8:10-13) Anthu amene ali m’pangano latsopanoli ndi amene amadya zizindikiro pa Chikumbutso. Anthuwa ndi okhawo “amene aitanidwa” mwapadera ndi Mulungu. (Aheberi 9:15; Luka 22:20) Akhristu amenewa adzalamulira limodzi ndi Yesu kumwamba ndipo Baibulo limanena kuti alipo okwana 144,000 okha.​—Luka 22:28-30; Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 3.

Mosiyana ndi “kagulu ka nkhosa” kameneka komwe kadzalamulire ndi Yesu kumwamba, ambirife tikuyembekezera kudzakhala m’gulu la “khamu lalikulu” lomwe lidzalandire moyo wosatha padziko lapansi. (Luka 12:32; Chivumbulutso 7:9, 10) Ngakhale kuti anthu amene tikuyembekezera kudzakhala padziko lapansi sitidya komanso kumwa zizindikiro za pa Chikumbutso, timakhala nawo pamwambowu posonyeza kuti timayamikira nsembe ya Yesu.​—1 Yohane 2:2.

a Anthu ena amanena kuti mwambo wa Mgonero wa Ambuye ndi sakaramenti. Koma buku lina lofotokoza za mawu a m’Baibulo limati: “Mawu akuti sakaramenti sapezeka mu Chipangano Chatsopano ndipo mawu achigiriki akuti μυστήριον [my·steʹri·on] sagwiritsidwa ntchito kunena za ubatizo, mgonero wa Ambuye kapena mwambo wina uliwonse.”—McClintock and Strong’s Cyclopedia, Volume IX, tsamba 212.

b Mabaibulo ambiri amamasulira lemba la 1 Akorinto 11: 25, 26 kuti, “nthawi zonse pamene” mukumwa kapena kudya mgonero. Ena amanena kuti mawuwa akusonyeza kuti tiyenera kuchita mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye nthawi zonse kapena kuti pafupipafupi. Komabe mawuwa sakusonyeza kuti tiyenera kuchita mwambowu kangati koma akungosonyeza zimene tiyenera kuchita “pamene” tikuchita mwambowu.—Baibulo la New International Version; ndi la Good News Translation.

c Onani buku lakuti, The New Schaff-Herzog Encyclopedia of Religious Knowledge, Volume IV, tsamba 43-​44, ndi la McClintock and Strong’s Cyclopedia, Volume VIII, tsamba 836.

d Onani buku lakuti, The New Cambridge History of the Bible, Volume 1, tsamba 841.

e Masiku ano, Ayuda amaona kuti mwezi wa Nisani umayamba pa nthawi imene mwezi uli kumdima. Koma m’nthawi ya Yesu iwo ankaona kuti mwezi wa Nisani unkayamba pamene mwezi wayamba kuonekera ku Yerusalemu. Izi zinkachitika patapita tsiku limodzi kapena awiri kuchokera pa nthawi imene mweziwo unali kumdima. N’chifukwa chake nthawi zina tsiku limene a Mboni amachita Chikumbutso cha imfa ya Yesu limasiyana ndi tsiku limene Ayuda a masiku ano amachita Pasika.

f Onani Baibulo la A New Translation of the Bible, lomasuliridwa ndi James Moffatt; The New Testament​—A Translation in the Language of the People, lomasuliridwa ndi Charles B. Williams; ndiponso la The Original New Testament, lomasuliridwa ndi Hugh J. Schonfield.