Pitani ku nkhani yake

Kodi a Mboni za Yehova Amaiona Bwanji Nkhani ya Maphunziro?

Kodi a Mboni za Yehova Amaiona Bwanji Nkhani ya Maphunziro?

Timagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo posankha zochita pa nkhani ya maphunziro. Koma wa Mboni aliyense payekha amagwiritsa ntchito chikumbumtima chake chophunzitsidwa bwino, ndipo akafuna kusankha zochita amatsatira mfundo zotsatirazi. a

 Maphunziro ndi ofunika kwambiri

Sukulu imathandiza munthu kuti akhale ndi ‘nzeru zopindulitsa ndiponso aziganiza bwino.’ Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti makhalidwe amenewa ndi ofunika kwambiri. (Miyambo 2:10, 11; 3:21, 22) Komanso Yesu anauza otsatira ake kuti aziphunzitsa anthu zinthu zomwe anawalamula. (Mateyu 28:19, 20) N’chifukwa chake timalimbikitsana kuti tizipita kusukulu n’cholinga choti tidziwe kuwerenga bwino, kulemba komanso kukhala ndi luso lolankhula ndi anthu ena. b Maphunzirowa amatithandizanso kudziwa zimene zipembedzo zina zimakhulupirira komanso zikhalidwe za anthu.​—1 Akorinto 9:20-22; 1 Timoteyo 4:13.

Maboma amaonanso kuti maphunziro ndi ofunika kwambiri moti amalimbikitsa achinyamata kuti azipita kusukulu kaya za pulayimale kapena sekondale. Ifenso timatsatira malamulo a bomawa pomvera lamulo la m’Baibulo lakuti: “Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu.” (Aroma 13:1) Timathandiza ana athu kuti azilimbikira sukulu n’cholinga choti azikhoza bwino m’kalasi. c Paja Baibulo limanena kuti: “Chilichonse chimene mukuchita, muzichichita ndi moyo wanu wonse ngati kuti mukuchitira Yehova, osati anthu.”​—Akolose 3:23.

Kuphunzira kumatithandiza kupezera mabanja athu zinthu zofunika. Baibulo limanena kuti: “Ngati munthu sasamalira anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira, makamaka a m’banja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupirira.” (1 Timoteyo 5:8) Munthu akaphunzira savutika kupeza njira yosamalilira banja lake ndipo amakwaniritsa mfundo ya palembali. Buku lina linanena kuti cholinga chachikulu cha maphunziro ndi “kuthandiza anthu kuti adzapeze zochita zowathandiza pa moyo wawo komanso kuti adzakhale odalirika m’dera lawo.” (The World Book Encyclopedia) Munthu waluso amene anaphunzira sukulu mokwanira amakhala wodalirika ndipo savutika kwambiri kuti apeze zinthu zothandizira banja lake.​—Miyambo 22:29.

Makolo amaonanso kuti maphunziro ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri zimene zingadzathandize ana awo akadzakula. (2 Akorinto 12:14) Timalimbikitsa makolo kuti azipititsa ana awo kusukulu, ngakhale kudera kwawo kutakhala kuti kulibe sukulu zaulere, n’zovuta kuphunzira komanso ngati kuphunzirako n’kosemphana ndi chikhalidwe cha kumeneko. d Timaperekanso malangizo a mmene makolo angathandizire ana awo pa nkhani ya maphunziro. e

 Timaona maphunziro moyenera

Timafufuza mosamala tikafuna kusankha maphunziro. Baibulo limanena kuti: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” (Miyambo 14:15) Pakapezeka mwayi wa maphunziro owonjezera, timagwiritsa ntchito mfundo ya palembali poganizira kuchuluka kwa nthawi komanso ndalama zomwe tingawononge tikuchita maphunzirowo. Mwachitsanzo, munthu sangawononge nthawi yochuluka ngati atasankha kuchita maphunziro a ntchito zamanja.

Kuphunzira za Yehova n’kofunika kwambiri kuposa maphunziro a pamwamba. Nzeru zomwe timapeza tikamaphunzira Baibulo zimatithandiza kuti tidzapeze moyo wosatha pamene maphunziro a pamwamba sangatipatse moyo. (Yohane 17:3) Baibulo limatithandiza kumvetsa “zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njira yonse ya zinthu zabwino.” (Miyambo 2:9) Mtumwi Paulo anali wophunzira kwambiri moti zikanakhala kuti ndi masiku ano tikananena kuti anapita kuyunivesite. Ngakhale zinali choncho, iye ankaona kuti ‘kudziwa Khristu Yesu . . . ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri.’ (Afilipi 3:8; Machitidwe 22:3) Masiku anonso, pali a Mboni za Yehova ambiri omwe anachita maphunziro a pamwamba, koma amaona kuti kuphunzira zokhudza Yehova n’kofunika kwambiri kuposa zonsezo. f

Kuphunzira mfundo za m’Baibulo kumatithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino

 Maphunziro apamwamba angawononge makhalidwe abwino komanso munthu angasiye kukonda Yehova

Mwambi wa m’Baibulo umanena kuti: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) A Mboni za Yehova amaona kuti kutumiza ana kumayunivesite ena kapena sukulu zina zogonera komweko, kumawononga makhalidwe awo abwino komanso ubwenzi wawo ndi Yehova. N’chifukwa chake a Mboni ambiri amasankha kuti asatumize ana awo malo ngati amenewa. Amaona kuti malo oterewa ndi amene ana amalimbikitsidwa kukhala ndi maganizo olakwika otsatirawa:

  • Maganizo olakwika: Ndalama zimathandiza munthu kukhala wosangalala komanso wotetezeka

    Anthu amaona kuti maphunziro apamwamba ndi njira yokhayo yodalirika yowathandiza kudzapeza ntchito ya ndalama zambiri. Zimenezi zimachititsa kuti ana ambiri akamaliza sukulu, azipita kuyunivesite. Anthu ena amaganiza kuti ndalama zingawathandize kuti azikhala osangalala komanso otetezeka. Koma Baibulo limanena kuti maganizo amenewa ndi olakwika. (Mlaliki 5:10) Limaphunzitsanso kuti “kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse” ndipo zotsatira zake chikhulupiriro cha munthu chimachepa. (1 Timoteyo 6:10) A Mboni za Yehova amayesetsa kuti asatengeke ndi “chinyengo champhamvu cha chuma.”​—Mateyu 13:22.

  • Maganizo olakwika: Maphunziro apamwamba angapangitse munthu kukhala wotchuka

    Chitsanzo ndi a Nika Gilauri omwe poyamba anali nduna yaikulu m’dziko la Georgia. Iwo analemba zokhudza mmene anthu amaonera maphunziro apamwamba m’dzikolo. Ananena kuti: “Kuti munthu akhale wotchuka komanso azilemekezedwa, amayenera kukhala ndi digiri ya kuyunivesite. M’mbuyomo, wachinyamata akalephera kupeza digiri, anthu a m’banja lake ankamuona kuti ndi wochititsa manyazi.” g Ngakhale zili choncho, Baibulo limatichenjeza za mavuto omwe amakhalapo munthu akamafunafuna kutchuka m’dzikoli. Nthawi ina Yesu anafunsa atsogoleri achipembedzo omwe ankafuna ulemerero kuti: “Mungakhulupirire bwanji, pamene mumalandira ulemerero kuchokera kwa anthu anzanu?” (Yohane 5:44) Moyo wa kuyunivesite umalimbikitsa anthu kukhala odzikuza ndipo Mulungu sasangalala ndi khalidweli.​—Miyambo 6:16, 17; 1 Petulo 5:5.

  • Maganizo olakwika: Aliyense ali ndi ufulu wosankha yekha zochita, kaya zabwino kapena zoipa

    A Mboni za Yehova amatsatira mfundo zimene Mulungu anakhazikitsa pa nkhani yosankha zabwino ndi zoipa. (Yesaya 5:20) Magazini ina inanena kuti achinyamata ena amatengera zochita za anzawo. Komanso “amasankha zinthu molakwika ndiponso mosiyana ndi zomwe ankadziwa poyamba, pa nkhani ya zoyenera kuchita ndi zosayenera.” h Zimene magaziniyi inanena n’zogwirizana ndi mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:33) Anthu akakhala kuyunivesite, amaona kuti palibe vuto lililonse kuchita zimene Mulungu amadana nazo monga, kuledzera, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kugonana asanakwatirane. Ndipotu nthawi zina anthu amachita kulimbikitsidwa kuti azichita makhalidwe amenewa.​—1 Akorinto 6:9, 10; 2 Akorinto 7:1.

  • Maganizo olakwika: Maphunziro apamwamba angachititse kuti zinthu zisinthe padzikoli

    Ena amafunafuna maphunziro apamwamba n’cholinga choti adzasinthe zinthu padzikoli komanso pa moyo wawo. Anthu oterewa, cholinga chawo chachikulu sichikhala kulemera kapena kukhala otchuka. N’zoona kuti kukhala ndi zolinga zoterezi si kolakwika, koma a Mboni za Yehova satsatira zimenezo. Mofanana ndi Yesu, amaona kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha womwe udzakonze zinthu kuti dzikoli lidzakhale labwino. (Mateyu 6:9, 10) Komabe sikuti timangokhala n’kumadikira kuti Ufumu wa Mulungu udzathetse mavuto. M’malomwake timagwira ntchito imene Yesu ankagwira yolalikira “uthenga wabwino . . . wa ufumu” padziko lonse. Ndipo chaka chilichonse uthengawu umathandiza anthu ambiri kusintha makhalidwe awo, n’kuyamba kukhala moyo wabwino. i​—Mateyu 24:14.

a Achinyamata a Mboni amene amakhalabe ndi makolo, amatsatira zomwe makolo awo awasankhira pa nkhani ya maphunziroyi bola ngati zikugwirizana ndi malamulo a Mulungu.​—Akolose 3:20.

b Pofika pano, tafalitsa mabuku oposa 11 miliyoni padziko lonse, othandiza anthu kuwerenga ndiponso kulemba. Limodzi mwa mabukuwa ndi lakuti Dziperekeni pa Kuwerenga ndi Kulemba. M’mayiko osiyanasiyana timakhalanso ndi makalasi aulere ophunzitsa anthu kulemba ndi kuwerenga m’zilankhulo zokwana 120. M’zaka zapakati pa 2003 ndi 2017, tinaphunzitsa anthu pafupifupi 70, 000 kuti adziwe kuwerenga ndi kulemba.

c Onani nkhani yakuti “Kodi Ndisiye Sukulu?

d Mwachitsanzo, timalimbikitsa makolo kuti azipititsa ana awo aamuna ndi aakazi kusukulu. Onani nkhani yakuti, “Kodi Mwana Wanga Azipita ku Sukulu?” kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya 15 March, 2003.

f Onani nkhani za pa jw.org, pagawo lakuti “Zokhudza Mmene Moyo Unayambira.”

g Buku lakuti, Practical Economics: Economic Transformation and Government Reform in Georgia 2004​—2012, tsamba 170.

h Magazini yakuti Journal of Alcohol and Drug Education, Volume 61, Na. 1, April 2017, tsamba 72.

i Onani nkhani za pa jw.org, pagawo lakuti “Baibulo Limasintha Anthu” kuti muone zitsanzo za anthu omwe analola mphamvu ya Mulungu komanso uthenga wa Ufumu kusintha moyo wawo.