Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumanzere: Yasser Qudaih/Anadolu via Getty Images; kumanja: RONALDO SCHEMIDT/AFP via Getty Images

KHALANI MASO

Kodi Anthu Adzasiya Liti Kumenya Nkhondo?​—Zimene Baibulo Limanena

Kodi Anthu Adzasiya Liti Kumenya Nkhondo?​—Zimene Baibulo Limanena

 Mlembi wamkulu wa Bungwe la United Nations, António Guterres, anati: “Panopa tikufunika kuchepetsa vuto limeneli. Panopa tikufunika kudziletsa kwambiri.” Iye ananena zimenezi chifukwa cha mabomba amene dziko la Iran linaphulitsa ku Israel Loweruka pa 13 April 2024.

 Nkhondo imene ikuchitika ku Middle East ndi imodzi mwa nkhondo zimene zikuchitika padziko lonse.

 “Panopa zachiwawa ndiponso mikangano zachuluka kwambiri padzikoli kuposa nthawi ya Nkhondo Yachiwiri Yapadziko Lonse ndipo anthu 2 biliyoni, kutanthauza munthu mmodzi pa anthu 4 aliwonse padzikoli, akuvutika ndi zachiwawazi.”​—United Nations Security Council, January 26, 2023.

 Mayiko omwe kukuchitika zachiwawazi ndi monga Israel, Gaza, Syria, Azerbaijan, Ukraine, Sudan, Ethiopia, Niger, Myanmar ndi Haiti. a

 Kodi kumenyana kudzatha? Kodi atsogoleri a mayiko angabweretse mtendere? Kodi Baibulo limanena zotani?

Nkhondo zimene zikuchitika m’mayiko osiyanasiyana

 Zachiwawa zimene zikuchitika padzikoli zikusonyeza kuti nkhondo zitha posachedwapa. Nkhondo zimenezi zikukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo wofotokoza za nthawi imene tikukhalamoyi. Baibulo limatchula za nthawi imeneyi kuti “mapeto a nthawi ino.”​—Mateyu 24:3.

  •   “Mudzamva phokoso la nkhondo ndi malipoti a nkhondo. . . . Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.”​—Mateyu 24:6, 7.

 Werengani nkhani yakuti “Kodi Chizindikiro cha “Masiku Otsiriza” Kapena Kuti Nthawi “ya Mapeto” N’chiyani?” kuti muone mmene nkhondo za masiku ano zikukwaniritsira ulosi wa m’Baibulo.

Nkhondo yomwe idzathetse nkhondo zonse

 Baibulo linaneneratu kuti zachiwawa ndiponso mikangano zidzatha. Kodi zidzatheka bwanji? Palibe munthu aliyense amene angathetse zimenezi koma zidzathetsedwa ndi ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse’ yomwe imatchedwa Aramagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Nkhondo imeneyi idzatsegula njira yoti Mulungu adzakwaniritse lonjezo lakuti anthu adzasangalala ndi mtendere wosatha.​—Salimo 37:10, 11, 29.

 Kuti mudziwe zambiri zokhudza nkhondo ya Mulungu yomwe idzathetse nkhondo zonse, werengani nkhani yakuti “Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzakhala Yotani?

a ACLED Conflict Index, “Ranking violent conflict levels across the world,” January 2024