Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tizipemphera kwa Yesu?

Kodi Tizipemphera kwa Yesu?

MUNTHU wina anachita kafukufuku kuti adziwe zimene achinyamata 800 ochokera m’zipembedzo zosiyanasiyana amakhulupirira. Ankafuna kudziwa ngati achinyamatawo amakhulupirira zoti Yesu amayankha mapemphero. Achinyamata 60 pa 100 alionse ananena kuti amakhulupirira zimenezi. Koma wachinyamata mmodzi anayankha kuti, amene amayankha mapemphero si Yesu koma Mulungu.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi tizipemphera kwa Yesu kapena kwa Mulungu? * Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambirane zimene Yesu anaphunzitsa otsatira ake pa nkhani ya pemphero.

KODI YESU ANAPHUNZITSA KUTI TIZIPEMPHERA KWA NDANI?

Zimene Yesu ankaphunzitsa komanso zimene ankachita zingatithandize kudziwa kuti tizipemphera kwa ndani.

Yesu ankapemphera kwa Atate wakumwamba ndipo anatipatsa chitsanzo cha zomwe ifenso tiyenera kuchita

ZIMENE ANKAPHUNZITSA: Wophunzira wina wa Yesu atamupempha kuti: “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera,” Yesuyo anamuyankha kuti: “Mukamapemphera muzinena kuti, ‘Atate.’” (Luka 11:1, 2) Komanso pa ulaliki wake wa paphiri, analimbikitsa anthu kuti azipemphera kwa Atate wakumwamba. Kenako anawauzanso kuti: “Atate wanu amadziwa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.” (Mateyu 6:6, 8) Ndiponso usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ngati mupempha chilichonse kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani.” (Yohane 16:23) Choncho, Yesu anatiphunzitsa kuti tizipemphera kwa Yehova Mulungu yekha, yemwe ndi Atate ake komanso Atate wathu.—Yohane 20:17.

ZIMENE ANKACHITA: Yesu sankangophunzitsa anthu kuti azipemphera kwa Atate. Nayenso ankapemphera kwa Atatewo. Mwachitsanzo, pa nthawi ina anati: “Atate ndikukutamandani pamaso pa onse, inu Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi.” (Luka 10:21) Pa nthawi inanso, “Yesu anakweza maso ake kumwamba ndi kunena kuti: ‘Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva.’” (Yohane 11:41) Ndiponso atatsala pang’ono kufa, Yesu anapemphera kuti: “Atate, ndikuikiza mzimu wanga m’manja mwanu.” (Luka 23:46) Choncho, Yesu ankapemphera kwa Atate wake, yemwe ndi “Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi.” Apatu, Yesu anatipatsa chitsanzo cha zimene ifenso tiyenera kuchita tikamapemphera. (Mateyu 11:25; 26:41, 42; 1 Yohane 2:6) Nanga kodi Akhristu oyambirira ankapemphera kwa Mulungu potengera chitsanzo cha Yesuchi?

KODI AKHRISTU OYAMBIRIRA ANKAPEMPHERA KWA NDANI?

Patangodutsa milungu yochepa Yesu atabwerera kumwamba, ophunzira ake anayamba kuzunzidwa komanso kuopsezedwa ndi anthu otsutsa. (Machitidwe 4:18) Zitatere, “onse pamodzi anafuula kwa Mulungu,” popemphera kuti apitirize kuwathandiza ndipo anapemphera kudzera “m’dzina la Yesu, mtumiki [wake] woyera.” (Machitidwe 4:24, 30) Apa zikusonyezeratu kuti ophunzira a Yesu ankatsatira chitsanzo chake ndipo ankapemphera kwa Mulungu, osati kwa Yesu.

Patadutsa zaka zingapo, zimene mtumwi Paulo analembera Akhristu ena zinasonyeza mmene iyeyo ndi anzake ankapempherera. Analemba kuti: “Nthawi zonse tikamakupemphererani, timayamika Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.” (Akolose 1:3) Paulo analemberanso Akhristu anzake kuti ‘aziyamika Mulungu pa zinthu zonse m’dzina la Ambuye Yesu Khristu.’ (Aefeso 5:20) Choncho, mawu amenewa akusonyeza kuti Paulo ankalimbikitsa ena kuti “nthawi zonse” azipemphera kwa Mulungu, kudzera m’dzina la Yesu.—Akolose 3:17.

Mofanana ndi Akhristu oyambirira, ifenso tingasonyeze kuti timakonda Yesu pomvera zimene anatiphunzitsa zoti tizipemphera kwa Mulungu. (Yohane 14:15) Tikamapemphera kwa Atate wathu wakumwamba yekha, tidzamva ngati mmene anamvera munthu amene analemba mawu a pa Salimo 116:1, 2 akuti: “Mtima wanga ndi wodzaza ndi chikondi, chifukwa Yehova amamva mawu anga. . . . Ndipo ndidzaitanira pa iye masiku onse a moyo wanga.” *

^ ndime 3 Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu ndi wamkulu kuposa Yesu. Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 4 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Bukuli

^ ndime 11 Kuti Mulungu azimva mapemphero athu, tizichita zinthu zogwirizana ndi zimene amafuna. Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 17 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?