Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chinsinsi cha Banja Losangalala

Kodi Mungatani Ngati Mwana Wanu Wayamba Kukayikira Chipembedzo Chanu?

Kodi Mungatani Ngati Mwana Wanu Wayamba Kukayikira Chipembedzo Chanu?

Ana ambiri akamakula amatsatira chipembedzo cha makolo awo. (2 Timoteyo 3:14) Komabe si ana onse amene amachita zimenezi. Kodi mungatani ngati mwana wanu wayamba kukayikira chipembedzo chanu? Nkhaniyi ikufotokoza zimene a Mboni za Yehova amachita pa nkhani imeneyi.

“Zikumandivuta kutsatira chipembedzo cha makolo anga. Ndikuona kuti ndi bwino kungochisiya.”​—Cora, wa zaka 18. *

N’KUTHEKA kuti mumakhulupirira zoti chipembedzo chanu chimaphunzitsa zoona zokhudza Mulungu. Mumakhulupiriranso kuti zimene Baibulo limaphunzitsa zimathandiza anthu kukhala ndi moyo wosangalala. Choncho, n’zachidziwikire kuti mungayesetse kuphunzitsa mwana wanu mfundo zimenezi. (Deuteronomo 6:6, 7) Koma kodi mungatani ngati pamene mwana wanu akukula wasiya kukonda zinthu zauzimu ndipo wayamba kukayikira zinthu zimene ankazikhulupirira kwambiri ali mwana?​—Agalatiya 5:7.

Zimenezi zikachitika, sizingatanthauze kuti mwalephera udindo wanu monga Mkhristu. Monga tionere mu nkhaniyi, pali zinthu zambiri zimene zingachititse kuti mwana ayambe kukayikira chipembedzo cha makolo ake. Komabe muyenera kudziwa mfundo iyi: Zimene mungachite ngati mwana wanu wayamba kukayikira chipembedzo chanu, zingachititse kuti mwanayo ayambirenso kukonda chipembedzocho kapena asiyiretu kuchikonda. Kukakamiza mwana wanuyo kuti azitsatirabe chipembedzocho, kungangoyambitsa mkangano ndipo inuyo ndi amene mungaluze pamapeto pake.​—Akolose 3:21.

Ndi nzeru kutsatira malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu, koma ayenera kukhala wodekha kwa onse. Ayeneranso kukhala woyenerera kuphunzitsa, wougwira mtima.” (2 Timoteyo 2:24) Kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinu “woyenerera kuphunzitsa” ngati mwana wanu wayamba kukayikira chipembedzo chanu?

Chitani Zinthu Mozindikira

Choyamba muyenera kuganizira za zinthu zimene zachititsa mwanayo kuyamba kukayikira chipembedzo chanu. Mwachitsanzo, ganizirani izi:

  • Kodi amaona kuti mumpingo mulibe munthu amene angacheze naye kapena amene angakhale mnzake? “Chifukwa chakuti ndinkaona kuti mu mpingo mulibe munthu amene angakhale mnzanga, ndinayamba kugwirizana kwambiri ndi anthu a kusukulu kwathu. Panopa ndimadandaula kwambiri chifukwa anzanga amenewa anachititsa kuti kwa nthawi yaitali ndisakhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu komanso anachititsa kuti ndisiye kukonda zinthu zauzimu.”​—Lenore, wa zaka 19.

  • Kodi amadzikayikira ndipo amaona kuti sangalimbe mtima kuuza ena zimene amakhulupirira? “Ndili pa sukulu ndinkachita manyazi kuuza ena zimene ndimakhulupirira. Ndinkaopa kuti anzanga azindiseka kapena kundisala. Anthu onse amene ankachita zinthu zosiyana ndi anzawo ankasalidwa choncho sindinkafuna kuti inenso azindisala.”​—Ramón, wa zaka 23.

  • Kodi amaona kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo ndi udindo waukulu? “Ndinkaona kuti sindingakwanitse kuchita zimene zingandithandize kudzapeza moyo wosatha umene Baibulo limalonjeza. Zimenezi zinandichititsa kuona kuti ndi bwino kungosiya chipembedzo changa.”​Renee, wa zaka 16.

Kambiranani Naye

Kodi ndi zinthu zotani zimene zikuchititsa kuti mwana wanu aziganiza choncho? Njira yabwino yodziwira zimenezi ndi kumufunsa. Koma samalani kuti zimene mukambirane zisachititse kuti muyambe kukangana. M’malomwake, chitani zimene lemba la Yakobo 1:19 limanena. Lembali limati: ‘Khalani wofulumira kumva, wodekha polankhula, wosafulumira kukwiya.’ Muyenera kukhala wodekha pokambirana ndi mwana wanu. Yesetsani kuchita zimenezi ndi “luso la kuphunzitsa ndiponso moleza mtima kwambiri” ngati mmene mungachitire ndi munthu wina woti si wa m’banja mwanu.​—2 Timoteyo 4:2.

Mwachitsanzo, ngati mwana wanu sakonda kupita nanu kumisonkhano, yesetsani kufufuza ngati pali chinachake kumisonkhanoko chimene sichimusangalatsa. Koma muyenera kumufunsa modekha. Chitsanzo chotsatirachi chikusonyeza kuti kholo silingadziwe vuto limene mwanayo ali nalo ngati silingakambirane naye bwinobwino.

Mwana: Masiku ano sindikufunanso zopita kumisonkhano.

Kholo: [mokalipa] Ukutanthauza chiyani ukamati sukufuna kupita kumisonkhano?

Mwana: Kungoti masiku ano misonkhano sikumandisangalatsa.

Kholo: Ndiye kuti Mulungunso samakusangalatsa? Maganizo oipatu amenewo. Kaya ufune, kaya usafune tizipitirabe limodzi. Apo ayi, pakhomo pano uchoke.

Mulungu amafuna kuti makolo aziphunzitsa ana awo za iyeyo komanso kuti anawo azimvera makolo awo. (Aefeso 6:1) Komabe simungafune kuti mwana wanu azingotsatira m’chimbulimbuli zinthu zauzimu zomwe mumachita komanso kumangopita nanu kumisonkhano monyinyirika. N’zodziwikiratu kuti mungasangalale kuti iye azipezeka pa misonkhano chifukwa chakuti akumvetsa kufunika kwa misonkhanoyo komanso chifukwa chokonda Yehova.

Mungathandize mwana wanu kuti azikonda Mulungu komanso misonkhano ngati mutazindikira zimene zikumuchititsa kukhala ndi maganizo amenewa. Poganizira zimenezi, tiyeni tione zimene kholo lija likanachita kuti lithandize mwana wake.

Mwana: Masiku ano sindikufunanso zopita kumisonkhano.

Kholo: [modekha] N’chiyani chakupangitsa kuganiza choncho?

Mwana: Kungoti masiku ano misonkhano sikumandisangalatsa.

Kholo: N’zoonadi, kukhala pansi kwa ola lathunthu kapena maola awiri kungakhale kotopetsa. Komano n’chiyani makamaka chimene sichimakusangalatsa kumisonkhanoko?

Mwana: Kungoti ndimaona kuti palibe chomwe ndikuchitako, bola ndikanangopita kwinakwake.

Kholo: Kodi anzako amaonanso choncho?

Mwana: Pamenepo m’pamene pali vuto langa. Inetu panopa ndilibe mnzanga aliyense. Kuchokera pamene mnzanga anasamuka, ndimangoona kuti palibe amene ndingacheze naye. Ndimaona kuti aliyense akusangalala pomwe ine ndimangokhala ndekhandekha.

Kholo la mu chitsanzo chachiwirichi lachititsa mwana wakeyu kumasuka kufotokoza zakukhosi kwake. Zimenezi zathandiza kuti adziwe vuto la mwanayo, lomwe ndi kusowa wocheza naye. Zathandizanso kuti mwanayo ayambe kukhulupirira kholo lakelo moti angadzakhale womasuka kufotokoza mavuto ake ena m’tsogolo.​—Onani bokosi lakuti  “Khalani Wodekha.”

M’kupita kwa nthawi, achinyamata ambiri amazindikira kuti akagonjetsa vuto limene likuwalepheretsa kukonda zinthu zauzimu, asiya kudzikayikira komanso ayamba kukonda chipembedzo chawo. Taganizirani za Ramón, yemwe tamutchula poyamba paja. Iye poyamba ankachita manyazi kuuza anzake a kusukulu zoti ndi Mkhristu. Koma patapita nthawi Ramón anazindikira kuti kuuza anzake zimene amakhulupirira, ngakhale atamamunyoza, sikochititsa mantha ngati mmene iye ankaganizira. Iye anati:

“Tsiku lina mnyamata wa m’kalasi mwathu anayamba kundinyoza chifukwa cha chipembedzo changa. Ndinachita mantha kwambiri ndipo ndinazindikira kuti anthu onse m’kalasimo akumva zimene ankanenazo. Kenako ndinangoisintha nkhaniyo n’kumufunsa iyeyo za chipembedzo chake. Ndinadabwa kwambiri kuona kuti iyeyo anachita mantha kwambiri kuposa ineyo. Pamenepa ndinazindikira kuti achinyamata ambiri amakhulupirira zinthu zomwe sazimvetsa bwinobwino. Ndinaona kuti bola ineyo, chifukwa ndikhoza kufotokoza zimene ndimakhulupirira. Kunena zoona, pa nkhani ya kufotokoza zimene umakhulupirira, anzanga a m’kalasi ndi amene ayenera kuchita mantha, osati ineyo.”

TAYESANI IZI: Mulimbikitseni mwana wanu wachinyamata kulankhula zakukhosi kwake mwa kumufunsa mmene amamvera chifukwa chokhala Mkhristu. Kodi iyeyo amaona kuti kukhala Mkhristu n’kothandiza motani? Nanga ndi mavuto ati amene amakumana nawo chifukwa choti ndi Mkhristu? Kodi madalitso amene amapeza chifukwa chokhala Mkhristu ndi ambiri kuposa mavuto amene amakumana nawo? (Maliko 10:29, 30) Muuzeni mwana wanuyo kuti atenge pepala ndipo alembe mzere pakati pa pepalalo. Kumanzere kwa pepalalo alembe mavuto amene akukumana nawo ndipo kumanja alembeko madalitso amene wapeza. Zimene walembazo zingamuthandize kudziwa vuto lake komanso kupeza njira yolithetsera.

Muthandizeni Kugwiritsa Ntchito “Luntha la Kuganiza”

Makolo komanso akatswiri ena apeza kuti ana aang’ono amaganiza mosiyana kwambiri ndi mmene achinyamata amaganizira. (1 Akorinto 13:11) Ana aang’ono amangokhulupirira zimene auzidwa, ngakhale asanazione. Koma achinyamata akauzidwa zinthu amaziganizira kwambiri ndipo nthawi zambiri amafuna azione kaye asanazikhulupirire. Mwachitsanzo, mwana wamng’ono ataphunzitsidwa kuti Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse, angangokhulupirira. (Genesis 1:1) Koma wachinyamata ataphunzitsidwa zimenezi angayambe kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndingadziwe bwanji zoti Mulungu alikodi? N’chifukwa chiyani Mulungu yemwe ndi wachikondi amalola kuti zoipa zizichitika? Kodi zingatheke bwanji kuti Mulungu akhale wopanda chiyambi?’​—Salimo 90:2.

Mukhoza kuganiza kuti mwana wanu akamafunsa zimenezi ndiye kuti chikhulupiriro chake chayamba kuchepa. Komatu zimenezi zingasonyeze kuti iye wayamba kuchita zinthu mwanzeru. Ndipotu kufunsa mafunso n’kumene kumathandiza munthu kuti amvetse komanso ayambe kukonda zinthu zauzimu.​—Machitidwe 17:2, 3.

Komanso dziwani kuti mwana wanu akamachita zimenezi ndiye kuti akuphunzira kugwiritsa ntchito “luntha la kuganiza.” (Aroma 12:1, 2) Akamachita zimenezi amatha kudziwa bwino “m’lifupi ndi m’litali ndi kukwera ndi kuzama” kwa zimene Akhristu amakhulupirira ndipo zimenezi n’zoti sakanakwanitsa ali mwana. (Aefeso 3:18) Inoyo ndiyo nthawi yabwino yomuthandiza mwana wanuyo kumvetsa zimene amakhulupirira. Zimenezi zingathandize kuti atsimikize ndi mtima wonse kuti zimene amakhulupirirazo ndi zolondola.​—Miyambo 14:15; Machitidwe 17:11.

TAYESANI IZI: Inu ndi mwana wanuyo kambiranani mfundo za m’Baibulo zosavuta kumvetsa zimene simunaziganizirepo kuti n’zofunika kuzifufuza. Mwachitsanzo, muthandizeni kuganizira mafunso ngati awa: ‘Kodi n’chiyani chimandithandiza kukhulupirira kuti Mulungu alipodi? Kodi ndimaona umboni wotani wotsimikizira kuti Mulungu amandikondadi? N’chifukwa chiyani ndimaona kuti kutsatira malamulo a Mulungu kumandithandiza?’ Samalani kuti musakakamize mwana wanuyo kuyankha zogwirizana ndi maganizo anu. Koma mulimbikitseni kuti apeze yekha zifukwa zokhulupirira mfundo za m’Baibulo. Kuchita zimenezi kungathandize mwanayo kutsimikizira kuti zimene amakhulupirirazo n’zoona.

“Zimene Unakhulupirira Pambuyo Pokhutira Nazo”

Baibulo limanena za wachinyamata wina dzina lake Timoteyo amene anadziwa malemba oyera ‘kuyambira pamene anali wakhanda.’ Komabe mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti: “Pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo.” (2 Timoteyo 3:14, 15) Mofanana ndi Timoteyo n’kutheka kuti mwana wanu wakhala akuphunzira mfundo za m’Baibulo kuyambira ali wakhanda. Komabe panopa mukufunika kumuthandiza kuti azikhutira kuti zimene amakhulupirirazo n’zoona.

Buku lachingelezi lakuti Questions Young People Ask​—Answers That Work, Volume 1, 2011 Edition, limati: “Ngati mwana wanu akukhalabe pakhomo panu, muli ndi ufulu womuuza kuti muzichita naye limodzi zinthu zauzimu. Koma cholinga chanu n’kumuthandiza kuti azikonda Mulungu kuchokera pansi pa mtima, osati azingotsatira zinthu m’chimbulimbuli. Mukamakumbukira cholinga chanuchi, mudzathandiza mwanayo kukhala ‘wolimba m’chikhulupiriro’ ndipo adzayamba kukonda zinthu zauzimu payekha, osati chifukwa cha inuyo. *​—1 Petulo 5:9.

^ ndime 4 Mayina a mu nkhaniyi tawasintha.

^ ndime 40 Kuti mumve zambiri, onani Nsanja ya Olonda ya May 1, 2009, tsamba 10-12, ndi buku lachingelezi lakuti Questions Young People Ask​—Answers That Work, Volume 1, 2011 Edition, tsamba 315-318.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Kodi ndimatani mwana wanga akamakayikira chipembedzo chathu?

  • Kodi ndingagwiritse ntchito bwanji mfundo zimene zili m’nkhani ino kuti ndisinthe mmene ndimachitira zinthu ndi mwana wanga?