Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anadzipereka ndi Mtima Wonse Kumadzulo kwa Africa

Anadzipereka ndi Mtima Wonse Kumadzulo kwa Africa

PASCAL anakulira ku Côte d’Ivoire ndipo anali wosauka. Koma iye ankafunitsitsa kukhala ndi moyo wabwino. Popeza kuti ankachita masewera ankhonya, ankadzifunsa kuti, ‘Kodi ndingapite kudziko liti kuti ndikakhale katswiri pa masewerawa n’kukhala wolemera?’ Pamene anali ndi zaka zoposa 20 anaganiza zopita ku Ulaya. Koma popeza analibe ziphaso zoyendera, anafunika kupita kumeneko mozemba.

Mu 1998, Pascal atakwanitsa zaka 27 ananyamuka ulendowu. Iye anadutsa m’dziko la Ghana, Togo ndi Benin ndipo kenako anafika m’tauni ya Birni Nkonni m’dziko la Niger. Koma kuchokera kumeneko anafunika kuyenda ulendo woopsa kwambiri kuti akafike ku Ulaya. Iye anafunika kukwera galimoto yaikulu n’kudutsa chipululu cha Sahara kuti akafike kunyanja ya Mediterranean. Atafika kumeneko anafunika kukwera sitima yopita ku Ulaya. Koma atafika ku Niger, panachitika zinthu ziwiri zimene zinamulepheretsa ulendowu.

Choyamba, ndalama zinamuthera. Chachiwiri, anakumana ndi mpainiya wina dzina lake Noé ndipo anayamba kuphunzira Baibulo. Zimene anaphunzirazo zinamukhudza kwambiri ndipo anasintha mmene ankaonera zinthu pa moyo wake. Pascal anasintha maganizo ake ofuna kulemera aja ndipo anayamba kufuna kutumikira Mulungu. Mu December 1999, iye anabatizidwa. Pofuna kuthokoza Yehova, iye anayamba upainiya mu 2001 ku Niger komweko, ndipo ankachita upainiyawu m’tauni yomwe anaphunzirira Baibulo ija. Kodi Pascal amaona bwanji utumiki umenewu? Iye anati, “Ndikusangalala kwambiri ndi zimene ndikuchita panopa.”

AKUSANGALALA KUTUMIKIRA KU AFRICA

Anne-Rakel

Mofanana ndi Pascal, anthu ambiri aona kuti kutumikira Mulungu n’kumene kumathandiza munthu kuti azisangalala. Pofuna kukwaniritsa cholinga chimenechi, ena achoka ku Ulaya n’kupita ku Africa kuti akatumikire kumadera amene kulibe anthu okwanira olalikira za Ufumu. Ndipotu ofalitsa pafupifupi 65 ochokera ku Ulaya, azaka za pakati pa 17 ndi 70 asamukira kumayiko a kumadzulo kwa Africa monga Benin, Burkina Faso, Niger ndi Togo. * N’chiyani chinawalimbikitsa kusamukira kumayiko akutali ndipo zikuwayendera bwanji kumeneko?

Mlongo wina wochokera ku Denmark, dzina lake Anne-Rakel, anati: “Makolo anga anali amishonale ku Senegal. Iwo ankasangalala kwambiri kufotokoza za umishonale wawo moti inenso ndinkafunitsitsa kukhala mmishonale.” Pafupifupi zaka 15 zapitazo, Anne-Rakel anasamukira ku Togo ali ndi zaka zoposa 20. Panopa akutumikira mumpingo wa chinenero chamanja kumeneko. Kodi iye analimbikitsa bwanji anthu ena pamene anasamuka? Iye anati:  “Patapita nthawi, mng’ono wanga ndiponso mchimwene wanga anasamukiranso ku Togo.”

Albert-Fayette ndi Aurele

M’bale wina wa ku France dzina lake Aurele ali pa banja ndipo ali ndi zaka 70. Iye anati: “Zaka 5 zapitazo ndinapuma pa ntchito. Choncho ndinayenera kusankha pakati pokhalabe ku France n’kumadikira kuti Paradaiso afike kapena kuyamba kuchita zambiri mu utumiki.” Aurele anasankha kuchita zambiri mu utumiki. Pafupifupi zaka zitatu zapitazo, iye ndi mkazi wake, Albert-Fayette, anasamukira ku Benin. Aurele anati: “Tinasankha bwino kwambiri kudzipereka kudzatumikira Yehova kunoko.” Iye ananenanso akusekerera kuti: “Mbali zina za gawo lathu zili m’mphepete mwa nyanja ndipo zimandikumbutsa kwambiri za Paradaiso.”

Clodomir ndi mkazi wake Lysiane anasamukira ku Benin kuchokera ku France zaka 16 zapitazo. Poyamba, ankasowa kwambiri achibale ndiponso anzawo a ku France ndipo ankadera nkhawa kuti mwina sangazolowere moyo wawo watsopano ku Benin. Koma pasanapite nthawi anayamba kusangalala kwambiri. Clodomir anati: “Pa zaka 16 zimene takhala kuno tathandiza anthu 16 kuti ayambe kutumikira Yehova.”

Lysiane ndi Clodomir ali ndi ena mwa anthu omwe awathandiza kuphunzira choonadi

Johanna ndi Sébastien

Sébastien ndi mkazi wake Johanna amachokera ku France ndipo anasamukira ku Benin mu 2010. Sébastien anati: “Mumpingo muli zambiri zoti tichite moti tikuphunzira zinthu zochuluka m’nthawi yochepa.” Koma kodi anthu amamvetsera mu utumiki? Johanna anati: “Anthu amafunitsitsa kwambiri kudziwa mfundo zoona za m’Baibulo. Ngakhale pamene sitili mu utumiki, anthu amatiimitsa n’kutifunsa mafunso okhudza nkhani za m’Baibulo kapena kutipempha mabuku.” Nanga kusamuka kwakhudza bwanji banja lawo? Sébastien anati: “Kusamukira kuno kwathandiza banja lathu kuti likhale lolimba. Ndimasangalala kwambiri kukhala mu utumiki tsiku lonse limodzi ndi mkazi wanga.”

Eric ndi mkazi wake Katy akuchita upainiya kumpoto kwa Benin kumene kulibe anthu ambiri. Pafupifupi zaka 10 zapitazo pamene ankakhala ku France, anayamba kuwerenga nkhani zokhudza kutumikira kudera limene kulibe ofalitsa okwanira. Iwo anayambanso kucheza ndi anthu amene anali kuchita utumiki wa nthawi zonse. Chifukwa chochita zimenezi, anayamba kufunitsitsa kusamukira kudziko lina ndipo anasamukadi mu 2005. Iwo asangalala kwambiri kuona anthu ambiri akuyamba kutumikira Yehova. Eric anati: “Zaka ziwiri zapitazo, gulu lathu la m’tauni ya Tanguiéta linali ndi ofalitsa 9 koma panopa tilipo 30. Lamlungu lililonse, anthu pakati pa 50 ndi 80 amapezeka pa misonkhano. N’zosangalatsatu kwambiri kuona kuti gulu lathu lakula chonchi.”

Katy ndi Eric

 MUTHA KUPIRIRA MAVUTO AMENE MUNGAKUMANE NAWO

Benjamin

Anthu amene asamukira kudziko lina amakumana ndi mavuto ena. Mwachitsanzo, Anne-Rakel ali ndi mchimwene wake wazaka 33 dzina lake Benjamin. M’chaka cha 2000, Benjamin ali ku Denmark, anakumana ndi mmishonale wina yemwe ankatumikira ku Togo. Benjamin anati: “Nditamuuza kuti ndikufuna kuchita upainiya, mmishonaleyo ananena kuti: ‘N’zotheka kukachita upainiyawo ku Togo.’” Benjamin anaganizira mfundo imeneyi. Iye anati: “Pa nthawiyo ndinali ndisanakwanitse n’komwe zaka 20, koma alongo anga awiri anali kale akutumikira ku Togo. Choncho sizikanandivuta kwenikweni kupita kumeneko.” Iye anapitadi, koma panali vuto lina. Benjamin anati: “Sindinkadziwa Chifulenchi ngakhale pang’ono. Choncho ndinavutika kwambiri miyezi 6 yoyambirira chifukwa sindinkatha kulankhula ndi anthu.” Koma patapita nthawi anaphunzira Chifulenchi. Panopa Benjamin akutumikira pa Beteli ku Benin. Iye amagwira ntchito m’dipatimenti yotumiza mabuku komanso m’dipatimenti ya makompyuta.

Marie-Agnès ndi Michel

Eric ndi Katy, omwe tawatchula kale aja, ankatumikira mumpingo wa chinenero china ku France asanasamukire ku Benin. Kodi ku Benin kunali kosiyana bwanji ndi ku France? Katy anati: “Zinali zovuta kupeza nyumba yabwino. Kwa miyezi yambiri tinkakhala m’nyumba yopanda magetsi komanso madzi.” Eric anawonjezera kuti: “Kumene tinkakhala kunkamveka nyimbo zosokosa kwambiri mpaka pakati pa usiku. Izi zimafuna kuti munthu akhale woleza mtima komanso wololera.” Onse amagwirizana ndi mfundo yakuti: “Madalitso amene tapeza chifukwa chotumikira m’dera limene kulibe ofalitsa okwanira ndi ambiri kuposa mavuto amene takumana nawo.”

Michel ndi mkazi wake Marie-Agnès, omwe ndi ochokera ku France ali ndi zaka zoposa 55. Iwo anasamukira ku Benin zaka pafupifupi 5 zapitazo, koma poyamba ankada nkhawa. Michel ananena kuti anthu ena ankawauza kuti zimene akuchitazo ndi zoopsa kwambiri. Mfundo imeneyi ndi yoona ngati munthu sakudalira Yehova. Koma iwo anasamuka kuti akatumikire Yehova ndipo iye anawathandiza.

KODI MUNGAKONZEKERE BWANJI?

Anthu amene anakatumikira kudziko lina amauza anthu ena kuti kukonzekera bwino n’kofunika. Amawauzanso kuti ayenera kukhala okonzeka kuzolowera zinthu zatsopano, kukhala ndi bajeti ndiponso kudalira Yehova.—Luka 14:28-30.

Sébastien, amene tamutchula kale uja, anati: “Kwa zaka ziwiri tisanasamuke, ine ndi Johanna tinasunga ndalama. Tinkapewa kuwononga ndalamazo pa zosangalatsa kapena zinthu zina zosafunika.” Kuti apitirize kutumikira kudziko lina, amagwira ntchito ku Ulaya kwa miyezi ingapo chaka chilichonse. Izi zimawathandiza kukhala ndi ndalama zokwanira pa miyezi inayo akuchita upainiya ku Benin.

Marie-Thérèse

 Marie-Thérèse ndi mmodzi mwa alongo pafupifupi 20 osakwatiwa omwe asamukira kumadzulo kwa Africa kukatumikira kumeneko. Iye ankagwira ntchito yoyendetsa basi ku France. Koma mu 2006, anapempha tchuti kuti akachite upainiya ku Niger kwa chaka chimodzi. Pasanapite nthawi, iye anaona kuti akufuna kupitiriza kuchita upainiyawu. Marie-Thérèse anati: “Nditabwerera ku France, ndinauza bwana wanga kuti ndikufuna kuchepetsa nthawi imene ndimagwira ntchito ndipo anandivomereza. Choncho masiku ano, ndimagwira ntchito yoyendetsa basi ku France kuyambira May mpaka August. Kenako ndimachita upainiya ku Niger kuyambira September mpaka April.”

Saphira

Anthu amene ‘akufunafuna ufumu choyamba’ ayenera kukhulupirira kuti Yehova adzawathandiza kupeza ‘zinthu zina zonse zofunika.’ (Mat. 6:33) Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina wosakwatiwa wazaka zoposa 25 dzina lake Saphira. Iye amachokera ku France ndipo anapita ku Benin kukachita upainiya. Mu 2011, atatumikira ku Africa kwa zaka 5, anabwereranso ku France kuti akapeze ndalama zokwanira kuti akatumikirenso ku Benin kwa chaka china. Saphira anati: “Lachisanu, lomwe linali tsiku langa lomaliza kugwira ntchito, linafika. Koma ndinkafunikira kugwirabe ntchito masiku ena 10 kuti ndipeze ndalama zokwanira chaka chonse. Ndipo kunali kutatsala milungu iwiri yokha kuti ndibwerere ku Benin. Choncho ndinapemphera kwa Yehova n’kumufotokozera zimenezi. Pasanapite nthawi, kampani ina inandiimbira foni n’kundipempha kukagwira ntchito kwa milungu iwiri m’malo mwa munthu wina.” Lolemba, Saphira anapita kuntchitoko kuti munthu winayo akamuphunzitse zoyenera kuchita. Iye anati: “Ndinasangalala kwambiri nditamva kuti munthuyo ndi mlongo amene ankafuna kutenga tchuti cha masiku 10 kuti apite ku Sukulu ya Utumiki Waupainiya. Bwana wake anakana kumupatsa tchuticho pokhapokha patapezeka munthu wina wogwira ntchito yake. Mofanana ndi ineyo, iye anali atachonderera Yehova kuti amuthandize.”

ZIMENE ZIMACHITITSA KUTI MOYO UKHALE WOSANGALATSA

Abale ndi alongo ena akhala akutumikira kumadzulo kwa Africa kwa zaka zambiri ndipo kwangokhala ngati kwawo. Ena anatha kungokhala kumeneko kwa zaka zingapo kenako n’kubwerera kwawo. Koma panopa anthu amenewa amaonabe kuti anaphunzira zambiri pa zaka zimene anakatumikira kudziko lina. Iwo anaona kuti kutumikira Yehova n’kumene kumachititsa kuti moyo ukhale wosangalatsa.

^ ndime 6 Nthambi ya ku Benin imayang’anira ntchito yolalikira m’mayiko onse 4 amenewa ndipo anthu a kumeneko amalankhula Chifulenchi.