Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kodi Zamoyo Zinachita Kusintha?

Kodi Zamoyo Zinachita Kusintha?

Anthu ena amanena kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Pomwe ena amanena kuti Mulungu analenga chinthu chimodzi n’kuchisiya kuti chisinthe n’kukhala zamoyo zambirimbiri. Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi?

Kodi zimene Baibulo limanena zoti zinthu zinachita kulengedwa, zimatsutsana ndi zimene asayansi amanena?

Baibulo limangonena kuti: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Koma silifotokoza mwatsatanetsatane mmene anazilengera. Asayansi ena amakhulupirira kuti poyamba penipeni zinthu zonse za m’chilengedwechi zinali chinthu chimodzi. Ndiyeno patapita nthawi, kunayamba kutentha kwambiri ndipo chinthu chija chinaphulika n’kupanga dziko lapansili, nyenyezi ndi zinthu zina. Ngati zimenezi zitakhala zoona, sizingatsutsane ndi zimene Baibulo limanena ndipo lemba la Genesis 1:1, lingatithandize kudziwa kuti pali winawake amene anachititsa kuti chinthucho chiphulike.

Asayansi ambiri amakhulupirira kuti kuphulikako kunangochitika kokha. Koma Baibulo siligwirizana ndi zimenezi, chifukwa limanena kuti Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse. Ndiye kaya analenga zinthu zosiyanasiyana pochititsa kuti chinthu china chiphulike kapena anazilenga mwa njira inayake, mfundo ndi yoti zinthuzi sizinakhalepo zokha.

“Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”Genesis 1:1.

Kodi Baibulo limagwirizana ndi mfundo yoti zamoyo zimatha kusintha pakapita nthawi?

Baibulo limanena kuti Mulungu analenga zamoyo ‘monga mwa mitundu yake.’ (Genesis 1:11, 12, 21, 24, 25) Kodi zingatheke kuti zamoyo za m’banja limodzi zisinthe n’kuyamba kuoneka mosiyana ndi zinzake? Inde n’zotheka. Koma kodi zamoyozo zimasintha n’kukhala zamoyo zina zosiyana kotheratu ndi zoyamba zija? Ayi. Zimangosintha pang’ono chifukwa cha kusintha kwa nyengo kapena zinthu zina, koma zimakhalabe za m’banja lomwelo.

Mwachitsanzo, cha m’ma 1970 akatswiri ena ankafufuza zokhudza mbalame zotchedwa finch, pachilumba cha Galapagos. Akatswiriwa anapeza kuti nthawi ina nyengo itasintha, mbalamezi zinayamba kusintha n’kukhala ndi milomo yaikulu. Zimenezi zinkathandiza kuti mbalamezi zizipeza zakudya mosavuta. Chifukwa cha zimenezi akatswiri aja anayamba kuona kuti umenewu ndi umboni woti zamoyo zinachitadi kusintha kuchokera ku zinthu zina. Koma patadutsa zaka zingapo, akatswiri aja anapeza kuti mbalame zija zinayambanso kusintha n’kukhala ndi milomo yaing’ono. Pulofesa wina, dzina lake Jeffrey H. Schwartz, analemba kuti kusintha kumeneku kunathandiza kuti mbalamezi zisafe ndi njala, “koma sikuti kunapangitsa kuti zisinthe n’kukhala zamoyo zina.”

Kodi n’zoona kuti Mulungu analenga chamoyo chimodzi n’kuchisiya kuti chisinthe kukhala zinthu zosiyanasiyana?

Baibulo limanena kuti Mulungu ‘analenga zinthu zonse.’ (Chivumbulutso 4:11) Limanenanso kuti ‘sanapume’ mpaka atamaliza ntchito yonse yolenga. (Genesis 2:2) Anthu ena amanena zoti Mulungu analenga chinthu chimodzi kenako n’kuchisiya kuti chisinthe n’kukhala zamoyo zina. Amati chinthucho chinayamba kusintha n’kukhala mitundu yosiyanasiyana ya zinthu monga nsomba, anyani komanso anthu. Koma zimenezi si zoona chifukwa Mulungu anapuma atamaliza kulenga zinthu zonse, osati atangolenga chinthu chimodzi chokha. * Maganizo amenewa sagwirizananso ndi mfundo ya m’Baibulo yoti kuli Mlengi amene “anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi zonse zili mmenemo.”—Ekisodo 20:11; Chivumbulutso 10:6.

“Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.”Chivumbulutso 4:11.

Mfundo zina zothandiza: Baibulo limanena kuti “chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino . . . m’zinthu zimene anapanga.” (Aroma 1:20) Choncho kuphunzira za Mulungu kungatithandize kukhala ndi moyo wabwino kwambiri ndiponso Mulungu akulonjeza kuti adzapatsa moyo wosatha anthu onse omwe amamukhulupirira. (Mlaliki 12:13; Aheberi 11:6) Kuti mudziwe mfundo zina pa nkhaniyi, funsani wa Mboni za Yehova aliyense kapena pitani pa webusaiti yathu ya www.pr418.com/ny. Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO.

^ ndime 12 Komanso Baibulo siligwirizana ndi zimene asayansi ena amanena zoti Mulungu analenga dzikoli m’masiku 6 enieni a maola 24. Kuti mudziwe zambiri, onani tsamba 24 mpaka 27 m’kabuku kachingelezi kakuti, Was Life Created? Kabukuka ndi kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Mungapangenso dawunilodi kabukuka kwaulere pa webusaiti yathu ya www.pr418.com.