Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 3

Zimene Mungachite Pothetsa Mavuto

Zimene Mungachite Pothetsa Mavuto

“Khalani okondana kwambiri, pakuti chikondi chimakwirira machimo ochuluka.”—1 Petulo 4:8

Mukakwatirana mukhoza kukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mavutowa angabwere chifukwa chakuti mumaona zinthu ndiponso kuganiza mosiyana. Koma angabwerenso chifukwa cha anthu ena kapena zinthu zina zimene simunkaziyembekezera.

Tingafune kungonyalanyaza mavutowo koma Baibulo limatilimbikitsa kuti tiyenera kuyesetsa kuwathetsa. (Mateyu 5:23, 24) Kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo kungakuthandizeni kuchita zimenezi.

1 MUZIKAMBIRANA VUTOLO

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Pali “nthawi yolankhula.” (Mlaliki 3:1, 7) Ndi bwino kupeza nthawi yokambirana vutolo. Muzifotokozera mwamuna kapena mkazi wanu mmene mukumvera mumtima mwanu komanso maganizo anu pa nkhaniyo. Nthawi zonse ‘muzilankhula zoona.’ (Aefeso 4:25) Ngakhale mutakhumudwa kwambiri pewani kukangana. Kuyankha modekha kungathandize kuti nkhani yaing’ono isakule n’kufika pa mkangano woopsa.—Miyambo 15:4; 26:20.

Ngakhale pamene maganizo anu akusiyana ndi a mnzanuyo muyenera kukhalabe aulemu komanso achikondi. (Akolose 4:6) Muziyesetsa kuthana ndi vuto mwamsanga ndipo musasiye kulankhulana.—Aefeso 4:26.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Sankhani nthawi yabwino yoti mukambirane

  • Wina akamalankhula, musamam’dule mawu. Muzidikira kuti amalize

2 MUZIMVETSERA BWINO

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Khalani ndi chikondi chenicheni pakati panu. Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) Kumvetsera bwinobwino n’kofunika. Yesetsani kumvetsa maganizo a mnzanuyo mwachifundo ndiponso modzichepetsa. (1 Petulo 3:8; Yakobo 1:19) Musamangonamizira kuti mukumvetsera. Ngati zingatheke, siyani kaye zimene mukuchita kuti mumvetsere mwatcheru kapena m’pempheni kuti mukambirane nthawi ina. Mukamaona kuti mwamuna kapena mkazi wanu ndi mnzanu osati mdani wanu ‘simudzafulumira kukwiya.’—Mlaliki 7:9.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Pitirizani kumvetsera bwinobwino ngakhale mnzanu atanena zinthu zokukhumudwitsani

  • Yesetsani kumvetsa mmene akumvera mumtima wake. Muziyang’ana mmene nkhope yake ikuonekera ndiponso kumva mmene akulankhulira

3 MUZICHITA ZIMENE MWAGWIRIZANA

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Kugwira ntchito iliyonse kumapindulitsa, koma kungolankhula mawu chabe kumasaukitsa.” (Miyambo 14:23) Kungogwirizana zochita si kokwanira. Ndi bwino kuchita zimene mwagwirizanazo. N’zoona kuti pangafunike kuchita khama kwambiri koma n’zothandiza. (Miyambo 10:4) Mukamachita zinthu mogwirizana ‘mudzapeza mphoto yabwino’ chifukwa cha khama lanu.—Mlaliki 4:9.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Onani zimene aliyense angachite pothana ndi vutolo

  • Nthawi zina muzionanso ngati zimene munagwirizana zikutheka