Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Mbalame ya Albatross Yosatopa ndi Kuuluka

Mbalame ya Albatross Yosatopa ndi Kuuluka

PALI mbalame zina zomwe zimatha kuuluka m’mwamba kwambiri komanso kwa nthawi yaitali mosavutikira, ndipo imodzi mwa mbalame zimenezi ndi mbalame yotchedwa albatross. Mbalameyi imakhala ndi mapiko aatali mamita 3.4 ndipo imatha kulemera makilogalamu 8.5. Mbalame ya albatross imatha kuuluka ulendo wautali ndipo poulukapo sifuna mphamvu zambiri. Chomwe chimathandiza mbalameyi kuchita zimenezi ndi mmene thupi lake lilili komanso luso lake pouluka.

Taganizirani izi: Mapiko a mbalame ya albatross ali ndi minofu inayake yomwe imachititsa kuti ikawongola mapiko ake pouluka isamatope msanga chifukwa chowongola mapikowo kwa nthawi yaitali. Zimenezi zimathandizanso kuti isamagwiritse ntchito mphamvu zambiri. Chinanso chomwe chimathandiza kuti mbalameyi iziuluka nthawi yaitali ndi luso lake lotha kudziwa kayendedwe ka mphepo yapanyanja.

Mbalameyi ikamauluka pamwamba pa nyanja imakwera kenako n’kutsika kwinaku ikudzitembenuza, zomwe zimathandiza kuti iziulukabe bwinobwino ngakhale kuli mphepo yamphamvu. Akatswiri asayansi angotulukira posachedwapa chimene chimathandiza kuti mbalameyi izichita zimenezi. Pogwiritsa ntchito makamera amphamvu kwambiri komanso mapulogalamu a pakompyuta, akatswiriwa apeza kuti mbalame za albatross sizitopa msanga zikamauluka chifukwa zimayamba kulowera kumene kukuchokera mphepo kenako zimakwera m’mwamba n’kuyamba kutsika, kulowera kumene kukupita mphepo. Asayansiwa ananena kuti mbalamezi zikamauluka mwa njira imeneyi zimatha kuuluka kwa nthawi yaitali sizakukupiza mapiko ake.

Potengera zimene mbalameyi imachita ikamauluka, asayansi akuona kuti akhoza kupanga ndege zosawononga mafuta ambiri mwinanso zosagwiritsa ntchito injini.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti mbalame ya albatross iziuluka chonchi?