Pitani ku nkhani yake

Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo?

Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo?

Kodi mukuona kuti zinthu m’dzikoli . . .

  • zikhalabe mmene zililimu?

  • ziipa kuposa pamenepa?

  • kapena zikhala bwino?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Mulungu . . . adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4, Baibulo la Dziko Latsopano.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?

Mudzakhala ndi moyo wosangalatsa komanso ntchito yabwino.—Yesaya 65:21-23.

Simudzadwala kapena kuvutika m’njira iliyonse.—Yesaya 25:8; 33:24.

Mudzakhala wosangalala ndi banja lanu komanso mabwenzi anu mpaka kalekale.—Salimo 37:11, 29.

KODI ZIMENE BAIBULO LIKUNENAZI TINGAZIKHULUPIRIREDI?

Inde, tingazikhulupirire pa zifukwa ziwiri izi:

  • Mulungu ali ndi mphamvu zokwaniritsira lonjezo limeneli. M’Baibulo ndi Yehova Mulungu yekha amene amatchedwa “Wamphamvuyonse” chifukwa ali ndi mphamvu zopanda malire. (Chivumbulutso 15:3) Choncho adzakwaniritsa lonjezo lake losintha dzikoli kuti likhale labwino. Ndipotu Baibulo limanena kuti “zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.”—Mateyu 19:26.

  • Mulungu akufunitsitsa kukwaniritsa lonjezo lake. Mwachitsanzo, Yehova ‘akulakalaka’ kuukitsa anthu amene anamwalira. —Yobu 14:14, 15.

    Baibulo limasonyezanso kuti Mwana wa Mulungu, Yesu, ankachiritsa odwala. N’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? Chifukwa ankafunitsitsa kuwathandiza. (Maliko 1:40, 41) Yesu anatsanzira ndendende Atate wake pa nkhani yofunitsitsa kuthandiza anthu ovutika.—Yohane 14:9.

    Choncho sitingakayikire kuti Yehova ndi Yesu ndi ofunitsitsa kutithandiza kuti tidzakhale osangalala m’tsogolomu.—Salimo 72:12-14; 145:16; 2 Petulo 3:9.

GANIZIRANI MFUNDO IYI

Kodi Mulungu adzachita chiyani kuti asinthe dzikoli kukhala labwino?

Baibulo limayankha funso limeneli pa MATEYU 6:9, 10 ndi pa DANIELI 2:44.