Onani zimene zilipo

Kodi Mzimu Woyela N’ciani?

Kodi Mzimu Woyela N’ciani?

Yankho la m’Baibo

 Mzimu woyela ni mphamvu imene Mulungu amaitumiza kuti ikagwile nchito. (Mika 3:8; Luka 1:35) Mulungu amatha kutumiza mzimu wake, kapena kuti mphamvu yake kulikonse kumene afuna kuti ikakwanilitse cifunilo cake.—Salimo 104:30; 139:7.

 Mu Baibo, liwu lakuti “mzimu” analimasulila kucokela ku liwu la Cihebeli lakuti ruʹach, komanso ku liwu la Cigiliki lakuti pneuʹma. Nthawi zambili mawu amenewa amatanthauza, mphamvu imene Mulungu amaitumiza kuti ikagwile nchito, ndiwo mzimu woyela. (Genesis 1:2) Komabe, Baibo imagwilitsilanso nchito mawu amenewa kutanthauza zinthu zina monga:

  •   Mpweya.—Habakuku 2:19; Chivumbulutso 13:15.

  •   Mphepo.—Genesis 8:1; Yohane 3:8.

  •   Mphamvu ya moyo imene ili m’thupi la zinthu zamoyo.—Yobu 34:14, 15.

  •   Maganizo a munthu kapena mtima wake.—Numeri 14:24.

  •   Anthu amzimu, kuphatikizapo Mulungu na angelo.—1 Mafumu 22:21; Yohane 4:24.

 Matanthauzo onsewa amanena za cinthu cosaoneka kwa anthu, koma nchito zake zimaoneka. Mofananamo, mzimu wa Mulungu, “uli ngati mphepo ndipo anthu sangathe kuuona kapena kuukhudza, koma ndi wamphamvu kwambili.”—An Expository Dictionary of New Testament Words, yolembedwa na W. E. Vine.

 Baibo imachulanso mzimu woyela wa Mulungu kuti “manja” kapena “zala.” (Salimo 8:3; 19:1; Luka 11:20; yelekezelani na Mateyu 12:28.) Monga mmene mmsili amaseŵenzetsela manja ake komanso zala zake pogwila nchito yake, nayenso Mulungu anagwilitsila nchito mzimu wake kuti:

  •   Pakhale cilengedwe.—Salimo 33:6; Yesaya 66:1, 2.

  •   Pakhale Baibo.—2 Petulo 1:20, 21.

  •   Atumiki ake a m’nthawi zakale acite zozizwitsa na kulalikila mokangalika.—Luka 4:18; Machitidwe 1:8; 1 Akorinto 12:4-11.

  •   Atumiki ake omumvela aonetse makhalidwe abwino.—Agalatiya 5:22, 23.

Mzimu woyela si munthu

 Baibo pochula mzimu wa Mulungu kuti “manja,” “zala,” kapenanso “mpweya,” imaonetsa kuti mzimu woyela si munthu ayi. (Ekisodo 15:8, 10) Manja a mmisili sangacoke kwa iye n’kukagwila nchito paokha popanda maganizo ake; nawonso mzimu woyela wa Mulungu sungadzigwila nchito paokha. Amacita kuutsogolela. (Luka 11:13) Baibo imafanizilanso mzimu wa Mulungu na madzi, ndipo imaugwilizanitsa na zinthu monga cikhulupililo na cidziŵitso. Zitsanzo zonsezi zimaonetsa mfundo yakuti mzimu woyela si munthu.—Yesaya 44:3; Machitidwe 6:5; 2 Akorinto 6:6.

 Baibo imachula maina a Yehova Mulungu na Mwana wake, Yesu Khristu. Koma sionetsa paliponse kuti mzimu woyela nawonso uli na dzina. (Yesaya 42:8; Luka 1:31) Pamene Mkhristu wofela cikhulupililo Sitefano anapatsidwa masomphenya oona kumwamba, anagoonako anthu aŵili cabe, osati atatu. Baibo imati: “Iye, pokhala wodzazidwa ndi mzimu woyela, anayang’anitsitsa kumwamba ndi kuona ulemelelo wa Mulungu ndi wa Yesu ataimilila kudzanja lamanja la Mulungu.” (Machitidwe 7:55) Mzimu woyela wa Mulungu ni umene unagwila nchito yothandiza Sitefano kuona masomphenyawo.

Maganizo olakwika ponena za mzimu woyela

 Maganizo olakwika: “Mzukwa Woyela,” kapena mzimu woyela, ni munthu ndipo ni mbali ya Utatu wa Mulungu, malinga na 1 Yohane 5:7, 8 mu Baibo ya King James.

 Mfundo yazoona: Pa 1 Yohane 5:7, 8 mu Baibo ya King James imaphatikizapo mawu akuti “kumwamba, Atate, Mawuyo, na Mzukwa Woyela: ndipo atatuwa ni mmodzi. Ndipo pali atatu acitila umboni padziko lapansi.” Koma ofufuza apeza kuti mawu amenewa sanalembedwe na mtumwi Yohane. Conco, safunika kukhalamo m’Baibo. Pulofesa wina, dzina lake Bruce M. Metzger, analemba kuti: “Mfundo yakuti mawu amenewa ni okaikitsa, ndipo safunika kupezeka m’Cipangano Catsopano, ni yazoona.”—A Textual Commentary on the Greek New Testament.

 Maganizo olakwika: Baibo imachula mzimu woyela monga munthu, conco izi zionetsa kuti mzimu woyela ni munthu.

 Mfundo yazoona: N’zoona kuti nthawi zina Malemba amachula mzimu woyela monga kuti ni munthu.

 Mwacitsanzo, pamene mtumwi Yohane anagwila mawu Yesu, anachula mzimu woyela monga kuti ni munthu pamene anati ni “mthandizi” amene adzapeleka umboni, kutsogolela, kulankhula, kumvela, kulengeza, kutamanda, komanso kulandila zinthu. (Yohane 16:7-15) Koma zimenezi sizitanthauza kuti mzimu woyela ni munthu. Baibo imachulanso nzelu, imfa, komanso chimo monga kuti ni munthu. (Miyambo 1:20; Aroma 5:17, 21) Mwacitsanzo, nzelu imachulidwa kukhala na “nchito” komanso “ana,” ndiponso chimo limachulidwa kukhala na makhalidwe a kunyenga, kupha, komanso kusilila mwansanje.—Mateyu 11:19; Luka 7:35; Aroma 7:8, 11.

 Maganizo olakwika: Kubatizika m’dzina la mzimu woyela kumaonetsa kuti mzimu woyela ni munthu.

 Mfundo yazoona: Nthawi zina Baibo imaseŵenzetsa liwu lakuti “dzina” potanthauza mphamvu kapena ulamulilo. (Deuteronomo 18:5, 19-22; Esitere 8:10) Conco, kubatizika “mu dzina la mzimu woyela” kumatanthauza kuti munthuyo akuvomeleza mphamvu komanso mbali imene mzimu woyela umacita pokwanilitsa cifunilo ca Mulungu.—Mateyu 28:19.

 Maganizo olakwika: Atumwi a Yesu pamodzi na ophunzila ake akale anali kukhulupilila kuti mzimu woyela unali munthu.

 Mfundo yazoona: Baibo siikamba zimenezi, ngakhalenso mbili yakale. Buku lakuti Encyclopædia Britannica limati: “Maganizo akuti Mzimu Woyela nayenso ni Mulungu . . . anayambila pa Msonkhano wa ku Constantinople mu ad 381.” Msonkhanowu unacitika patapita zaka zoposa 250 kucokela pamene mtumwi wothela anamwalila.