Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO

Kodi Zamalisece Zilibe Vuto??

Kodi Zamalisece Zilibe Vuto??

M’dziko masiku ano, zamalisece zili ponse-ponse. a Zimapezeka m’zinthu monga zotsatsa malonda, mafashoni, mafilimu, nyimbo ndi mabuku. Zimapezekanso pa TV, m’maseŵela a pavidiyo, pafoni, pa Webusaiti ndi m’zithunzi-thunzi zimene anthu amatumizilana pa Intaneti. Dzikoli masiku ano, limaona kuti zamalisece zilibe vuto lililonse. Anthu ambili m’madela oculuka amakonda kupenyelela, kuŵelenga kapena kumvetsela zamalisece kuposa kale.—Onani bokosi lakuti  “Mmene Zamalisece Zafalila.”

Zamalisece zikuipila-ipila. Pulofesa wina dzina lake Gail Dines analemba kuti: “Zithunzi-thunzi zamalisece zakhala zonyansa kwambili masiku ano, cakuti zimene kale anthu anali kuona kuti ndi zithunzi-thunzi zonyansa kwambili, masiku ano amaziona kuti ndi zabwino-bwino.”

Kodi inu zimenezi mumaziona bwanji? Kodi mumaona zamalisece kuti ndi zabwino-bwino ndi zovulaza, kapena kuti zili pakati-kati? Yesu anati: “Mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo uliwonse wovunda umabala zipatso zopanda pake.” (Mateyu 7:17) Kodi zamalisece zimabala zipatso zotani? Kuti tipeze mayankho, tiyeni tikambilane mafunso angapo ofunika kwambili okhudza zamalisece.

Kodi zamalisece zimabweletsa mavuto otani kwa munthu?

ZIMENE AKATSWILI AMANENA: Cizoloŵezi cokonda zamalisece n’covuta kwambili kusiya, ndipo akatswili ena ofufuza zinthu ndi madokotala amayelekezela zamalisece ndi mankhwala osokoneza bongo.

Brian, bamene anali ndi cizoloŵezi cokonda zamalisece za pa Intaneti anati: “Zinali kundivuta kusiya. Ndinali kumva monga ndikulota. Thupi langa linali kunjenjemela, ndipo mutu nthawi zina unali kuwawa. Ndinayesa-yesa kuti ndileke, koma ngakhale pambuyo pa zaka zambili ndinali kukondabe zamalisece.”

Nthawi zambili anthu amene amakonda zamalisece amabisa khalidwe lao. Amacita zinthu mwakabisila ndi mwacinyengo. N’cifukwa cake anthu ambili amene amakonda zamalisece amavutika ndi kusungulumwa, manyazi, nkhawa, kuvutika maganizo ndi ukali. Nthawi zina amafika poganiza zodzipha. Serge, amene pafupi-fupi masiku onse anali kutenga zamalisece pa Intaneti ndi kuziika pa foni yake yam’manja anati: “Cifukwa ca khalidwe limeneli ndinakhala wodzikonda ndi wovutika maganizo. Ndinali kudziona wopanda pake, wolakwa, wosoŵa mnzake kapena wopanda kothaŵila. Ndinalephela kupempha thandizo cifukwa cakuti ndinali ndi manyazi ndi mantha.”

Ngakhale kuona zamalisece pang’ono kapena mwangozi kungakhale kovulaza. Katswili wina wofufuza za kuipa kwa zamalisece wochedwa Dr. Judith Reisman, anavomeleza mfundo imeneyi pamaso pa komiti ina ya kunyumba ya malamulo ku America. Iye anati: “Zithunzi-thunzi zamalisece zimakhazikika m’maganizo ndi kusokoneza ubongo. Zimenezi zimapangitsa munthu kukhala ndi zithunzi-thunzi m’maganizo zimene zimakhala zovuta kapena zosatheka kuziiŵala.” Mtsikana wina wa zaka 19 wochedwa Susan, amene anali kupenyelela zamalisece pa Intaneti anati: “Zithunzi-thunzi zimenezo zinakhazikika kwambili m’maganizo anga. Zimabwela m’maganizo nthawi iliyonse. Ndimaona kuti sindidzakwanitsa kuzicotselatu m’maganizo anga.”

MFUNDO YOFUNIKA KWAMBILI: Zamalisece zimapangitsa anthu amene amazikonda kukhala akapolo ndipo zimawabweletsela mavuto aakulu.—2 Petulo 2:19.

Kodi zamalisece zimabweletsa mavuto otani m’banja?

ZIMENE AKATSWILI AMANENA: “Anthu okwatilana amalekana ndipo mabanja amatha cifukwa ca zamalisece.”—The Porn Trap, lolembedwa ndi Wendy ndi Larry Maltz.

Zamalisece zimaononga zikwati ndi mabanja

  • Mwa kupangitsa anthu m’banja kukaikilana, kulephela kugwilizana ndiponso kucepetsa cikondi pakati pao.—Miyambo 2:12-17.

  • Mwa kulimbikitsa munthu kukhala ndi mzimu wodzikonda, wosaganizila ena ndi wosakhutila ndi mnzake wa m’cikwati.—Aefeso 5:28, 29.

  • Mwa kusonkhezela cilakolako conyansa ca kugonana.—2 Petulo 2:14.

  • Mwa kupangitsa munthu kukakamiza mnzake wa m’cikwati kuti azicita naye zinthu zosayenela zokhudza kugonana.—Aefeso 5:3, 4.

  • Mwa kupangitsa munthu kukhala wosakhulupilika.—Mateyu 5:28.

Baibo imauza anthu okwatilana kuti sayenela “kucita zacinyengo” kwa wina ndi mnzake. (Malaki 2:16) Kusakhulupilika ndi khalidwe lacinyengo limene lingaononge cikwati ndi kupangitsa anthu kupatukana ndi kusudzulana. Cifukwa ca zimenezo ana a m’banjalo amavulazidwa.

Zamalisece zingaonongenso ana ngati amazipenyelela. Brian, amene tam’chula poyamba paja anati: “Pamene ndinali ndi zaka pafupi-fupi 10, ndinapeza magazini a zithunzi-thunzi zamalisece a atate anga pamene ndinali kuseŵela kabisa-bisa. Ndinayamba kuziona mobisa, ndipo sindinali kudziŵa cifukwa cake ndinali kuzikonda zithunzi-thunzi zimenezo. Uku ndiye kunali kuyamba kwa cizolowezi canga coipa, ndipo cizolowezi cimeneco ndinakula naco.” Zofufuza zaonetsa kuti zamalisece zingapangitse acinyamata kukonda zaciwelewele akali pa msinkhu wocepa, ndipo angayambe uhule, kugwilila anthu, ngakhale kusokonezeka maganizo.

MFUNDO YOFUNIKA KWAMBILI: Zamalisece zimaononga ubwenzi wabwino, ndipo zimabweletsa nkhawa ndi mavuto ena.—Miyambo 6:27.

Kodi Baibo imati bwanji pankhani ya zamalisece?

ZIMENE MAU A MULUNGU AMANENA: “Conco cititsani ziwalo za thupi lanu . . . kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, cilakolako ca kugonana, cikhumbo coipa, ndi kusilila kwa nsanje, kumene ndiko kulambila mafano.”—Akolose 3:5.

Kunena mosapita m’mbali, Yehova c Mulungu amadana ndi zamalisece. Zili conco osati cifukwa cakuti iye amaona kuti kugonana ndi cinthu cocititsa manyazi. Iye analenga anthu ndi mphamvu za kugonana ndi colinga cakuti anthu okwatilana azizigwilitsila nchito kusangalatsana, kulimbitsa ubwenzi wao ndi kubeleka ana.—Yakobo 1:17.

Conco, kodi timadziŵa bwanji kuti Yehova amanyansidwa ndi zamalisece? Ganizilani zifukwa zingapo.

  • Amadziŵa kuti zamalisece zingavulaze munthu.—Aefeso 4:17-19.

  • Iye amatikonda ndipo amafuna kutiteteza kuti tisavulazidwe.—Yesaya 48:17, 18.

  • Yehova amafuna kuti maukwati ndi mabanja akhale otetezeka.—Mateyu 19:4-6.

  • Iye amafuna kuti tikhale ndi makhalidwe oyela ndi kuti tizilemekeza ufulu wa ena.—1 Atesalonika 4:3-6.

  • Iye amafuna kuti tizilemekeza mphamvu zathu zobelekela ndi kuzigwilitsila nchito m’njila yoyenela.—Aheberi 13:4.

  • Yehova amadziŵa kuti zamalisece zimaonetsa maganizo opotoka ndi odzikonda a Satana.—Genesis 6:2; Yuda 6, 7.

MFUNDO YOFUNIKA KWAMBILI: Zamalisece zimaononga ubwenzi wa munthu ndi Mulungu.—Aroma 1:24.

Koma Yehova amacitila cifundo anthu amene amafuna kusiya khalidwe lokonda zamalisece. Baibo imati: “Yehova ndi wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha. Pakuti iye akudziŵa bwino mmene anatiumbila, amakumbukila kuti ndife fumbi.” (Salimo 103:8, 14) Iye akupempha anthu odzicepetsa kupita kwa iye kuti ‘awacitile cifundo ndi kuwasonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene akufunika thandizo.’—Aheberi 4:16; onani bokosi lakuti “Zimene Mungacite kuti Muthetse Vuto Lokonda Zamalisece.”

Anthu ambili alandila thandizo limene Mulungu amapeleka. Kodi thandizo lake limagwiladi nchito? Onani zimene Baibo imanena zokhudza anthu ena amene anagonjetsa zizoloŵezi zoipa. Iyo imati: “Mwasambitsidwa kukhala oyela, mwapatulidwa, mwayesedwa olungama m’dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, komanso ndi mzimu wa Mulungu wathu.” (1 Akorinto 6:11) Anthu otelo angavomeleze mau a mtumwi Paulo akuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:13.

Susan, amene anagonjetsa cizoloŵezi cake cokonda zamalisece, anati: “Yehova yekha ndi amene angakuthandizeni kuleka khalidwe lokonda zamalisece. Ngati mupempha thandizo la Mulungu ndi citsogozo cake, mungakhale ndi ubwenzi wabwino ndi iye. Iye sadzalephela kukuthandizani.”

a Liu lakuti “zamalisece” limatanthauza zinthu zimene colinga cake ndi kupangitsa munthu kukhala ndi cilakolako ca kugonana. Zinthu zimenezi zimaphatikizapo zithunzi-thunzi, mabuku ndi zinthu zimene anthu amamvetsela.

b Maina m’nkhani ino asinthidwa.

c Yehova ndi dzina la Mulungu monga mmene Baibo imanenela.