Onani zimene zilipo

Kodi a Mboni za Yehova Amapewa Anthu Amene Kale Anali M’cipembedzo Cao?

Kodi a Mboni za Yehova Amapewa Anthu Amene Kale Anali M’cipembedzo Cao?

Anthu amene kale anali a Mboni za Yehova koma tsopano analeka kulalikila ndipo anasiya kugwilizana ndi okhulupilila anzao, sitiwanyalanyaza. Koma timawafikila ndi kuwalimbikitsa kuti ayambenso kukonda zinthu za kuuzimu.

Siticotsa mwacisawawa munthu mumpingo akacita colakwa cacikulu. Komabe timacotsa Mboni yobatizika imene imaphwanya mfundo za makhalidwe abwino ndiponso ngati Mboniyo sifuna kulapa. Baibulo limakamba mosapita m’mbali kuti: “M’cotseni pakati panu munthu woipayo.”—1 Akorinto 5:13.

Nanga bwanji za munthu amene wacotsedwa mumpingo koma mkazi ndi ana ake ndi Mboni? Iye amasiya kucitila pamodzi zinthu za kuuzimu ndi banja lake. Komabe io amapitilizabe kukondana ndi kucitila zinthu zina pamodzi monga banja.

Munthu wocotsedwa amaloledwa kupezeka pa misonkhano yathu ndipo angalandilenso malangizo ndi uphungu kwa akulu mumpingo. Colinga copelekela malangizo ndi kuthandiza wocimwayo kuti ayenelelenso kukhala wa Mboni za Yehova. Wocimwa amene walapa ndi kusiya makhalidwe ake onyansa ndipo akuyesetsa kutsatila mfundo zolungama za m’Baibulo amaloledwa kukhalanso mmodzi wa Mboni za Yehova.