Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ngati Mnzanu wa mu Ukwati Amaonelela Zamalisece

Ngati Mnzanu wa mu Ukwati Amaonelela Zamalisece
  • “N’namva monga mwamuna wanga wakhala akucita cigololo mobweleza-bweleza.”

  • “N’nadziona wacabe-cabe, komanso wamaonekedwe osakhumbilika, ndipo n’nali kucita manyazi.”

  • “Sin’nauzeko aliyense nkhaniyi. Conco, panalibe wonitonthoza.”

  • “N’namva monga Yehova sasamala za ine.”

Ndemanga zili pamwambazi, zionetsa cisoni cimene mkazi amakhala naco mwamuna wake akamaonelela zamalisece. Ndipo ngati wakhala akucita zimenezi mwakabisila, mwina kwa miyezi kapena zaka, mkaziyo angaone kuti n’zosatheka kum’khulupililanso. Mkazi wina anati, “N’nadzifunsa kuti: ‘Kodi mwamunayu nimam’dziŵadi? Kodi palinso zina zimene amabisa kwa ine?’”

Nkhani ino yalembedwela mkazi amene mwamuna wake amaonelela zamalisece. a Ifotokoza mfundo za m’Baibo zimene zidzam’tonthoza, na kum’tsimikizila kuti Yehova amam’konda. Zidzam’thandizanso kukhala na mtendele wa mumtima na kukhalabe pa ubwenzi na Yehova. b

KODI MKAZI ANGATANI?

Ngakhale kuti simungalamulile zilizonse zimene mwamuna wanu amacita, pali zimene mungacite kuti mucepetse nkhawa na kupeza mtendele wa mumtima. Onankoni zina mwa zinthuzo.

Pewani kudziimba mlandu. Mkazi angamaganize kuti vuto ni iyeyo kuti mwamuna wake ayambe kuonelela zamalisece. Mlongo Alice c anadziona kuti sanali ciphadzuŵa kwa mwamuna wake. Iye anadzifunsa kuti, ‘N’cifukwa ciyani mwamuna wanga amasankha kumayang’ana akazi ena m’malo mwa ine?’ Akazi ena amadziimba mlandu poganiza kuti ndiwo amasonkhezela mwamuna wawo kukhala na khalidweli. Mlongo Danielle anati, “N’nadziona ngati mkazi woipa amene anali kupasula nyumba yathu cifukwa ca mkwiyo umene n’nakhala nawo n’tadziŵa kuti mwamuna wanga amaonelela zamalisece.”

Ngati inunso mumamva conco, dziŵani kuti Yehova sakuimbani mlandu pa khalidwe loipa la mwamuna wanu. Yakobo 1:14 imati: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’cilakolako cake.” (Aroma 14:12; Afil. 2:12) M’malo mokuimbani mlandu, Yehova amayamikila kukhulupilika kwanu.—2 Mbiri 16:9.

Cingakhalenso cothandiza kudziŵa kuti ngati mwamuna wanu amaonelela zamalisece, sizitanthauza kuti mukupelewela pena pake kapena kuti sindinu wokongola ayi. Akatswili oona za nkhaniyi amanena kuti kuonelela zamalisece kumabweletsa cilakolako camphamvu ca kugonana cimene kulibe mkazi angacikhutilitse.

Pewani kuda nkhawa kwambili. Mlongo Catherine anati anali kungokhalila kuganizila zakuti mwamuna wake amaonelela zamalisece. Mlongo Frances anati: “Nimada nkhawa ngati sinidziŵa kumene mwamuna wanga ali. Nimangokhalila kuda nkhawa tsiku lonse.” Akazi ena afotokozapo kuti amacita manyazi kwambili akakhala pamodzi na Akhristu anzawo amene amadziŵa vuto ya mwamuna wawo. Ndipo ena anena kuti amamva kuti ali okha-okha cifukwa amaganiza kuti kulibe amene angamvetse zimene akupitamo.

N’cibadwa kumva conco. Koma kungoganizila zimenezi kungawonjezele nkhawa yanu. Muziika maganizo anu pa ubale wanu na Yehova. Kucita zimenezi kudzakuthandizani kukhala na mtendele wa mumtima.—Sal. 62:2; Aef. 6:10.

Mungapeze thandizo mwa kuŵelenga na kusinkhasinkha nkhani za akazi ochulidwa m’Baibo, amene pa nthawi ya mavuto anapeza citonthozo popemphela kwa Yehova. Si nthawi zonse pamene iye anali kuwacotsela mavuto awo, koma anali kuwapatsa mtendele wake. Mwacitsanzo, Hana anali “wokhumudwa kwabasi” cifukwa ca mavuto ake. Koma ‘atapemphela kwa Yehova kwa nthawi yaitali,’ anapeza mtendele wa mumtima ngakhale kuti sanadziŵe mmene zinthu zidzakhalile.—1 Sam. 1:10, 12, 18; 2 Akor. 1:3, 4.

Onse aŵili, mwamuna na mkazi wake, ayenela kupempha thandizo kwa akulu

Muzipemphanso thandizo kwa akulu mu mpingo. Iwo angakhale “malo obisalilapo mphepo ndi malo ousapo mvula yamkuntho.” (Yes. 32:2) Angakuthandizeni kupeza mlongo amene mungauzeko nkhaniyo, amenenso angakutonthozeni.—Miy. 17:17.

KODI MUNGAM’THANDIZE?

Kodi mungathe kum’thandiza mwamuna wanu kuthetsa cizolowezi cake copenyelela zamalisece? Mwina. Baibo imaonetsa kuti pothetsa vuto kapena pogonjetsa mdani wamphamvu, “aŵili amaposa mmodzi.” (Mlal. 4:9-12) Kafukufuku aonetsa kuti nthawi zambili pamakhala zotulukapo zabwino ngati okwatilana amaseŵenzela pamodzi kuti mwamuna athetse cizolowezi copenyelela zamalisece, komanso kuti mkazi ayambilenso kum’khulupilila.

Komabe, zimadalila kwambili pa kuona mtima kwa mnzanuyo na kufunitsitsa kwake kuti athetse cizolowezi coonelela zamalisece. Kodi wacondelela Yehova kuti am’patse mphamvu na kupempha thandizo kwa akulu? (2 Akor. 4:7; Yak. 5:14, 15) Kodi akucita zinthu zimene zingam’thandize kupewa mayeselo, monga kudziikila malile pa kaseŵenzetsedwe ka zipangizo zamakono, na kupewa mikhalidwe imene ingamuike pa mayeso? (Miy. 27:12) Kodi ni wofunitsitsa kulandila thandizo lanu, komanso kukhala woona mtima kwa inu? Ngati n’conco, ndiye kuti n’zotheka inu kum’thandiza.

Motani? Onani citsanzo ici. Mlongo Felicia anakwatiwa na m’bale Ethan amene anali na cizolowezi copenyelela za malisece ali wacicepele. Mlongo Felicia amacita zinthu m’njila yakuti cikhale copepuka kwa mwamuna wake kukambilana naye akakhala na cilakolako cofuna kuonelela zamalisece. M’bale Ethan anakamba kuti: “Nimakambilana na mkazi wanga moona mtima komanso momasuka. Mwacikondi, iye amanithandiza kudziikila malile. Ndipo amanifunsa pafupi-pafupi mmene zinthu zilili. Amanithandizanso kuti nisamathele nthawi yaitali pa Intaneti.” Ngakhale n’telo, mlongo Felicia cimamuŵaŵa poona kuti mwamuna wake amakhala na cikhumbo coonelela zamalisece. Komabe, iye anati, “Mkwiyo na kupwetekedwa mtima kwanga sizingam’thandize kugonjetsa vuto limeneli. Koma nimamvako bwino nikaona mwamuna wanga akugwililapo nchito pa zimene tinakambiliana za vuto lake.”

Makambilano otelo angathandize mwamuna kugonjetsa cizolowezi coonelela zamalisece. Angathandizenso mkazi kuyambilanso kukhulupilila mwamuna wake. Ndipo mwamuna akakhala womasuka kuuza mkazi wake zifooko zake, kumene akupita, komanso zimene akucita, mkazi angayambilenso kum’khulupilila poona kuti sakum’bisa kalikonse.

Kodi muona kuti mungathandize mwamuna wanu mwa njila imeneyi? Ngati n’telo, bwanji osaŵelenga nkhani ino na kukambilana mfundo zake capamodzi? Colinga ca mwamuna wanu cikhale kugonjetsa cizolowezi cake, na kukuthandizani kum’khulupililanso. Iye sayenela kukhumudwa mukafuna kukambilana naye nkhaniyi. M’malo mwake a ayenela kumvetsa mmene nkhaniyo yakukhudzilani. Colinga canu cikhale kum’thandiza pa zoyesa-yesa zake, na kum’patsa mpata kuti aonetse kuti mungam’khulupililenso. Nonse aŵili muyenela kudziŵa cifukwa cake anthu amagwela mu msampha woonelela zamalisece, na mmene mungathetsele vutolo. d

Ngati muona kuti pangabuke m’kangano pa makambilanowo, mungapemphe mkulu amene nonse aŵili mumamasuka naye kuti akhale nanu na kutsogolela makambilanowo maulendo angapo. Dziŵani kuti ngakhale kuti mnzanu wa mu ukwati wagonjetsa cikhumbo copenyelela za malisece, zingatenge nthawi kuti muyambilenso kum’khulupilila. Koma musalefuke. Muziyesa kuona masinthidwe ngakhale aang’ono. Khalani na cidalilo cakuti ngati ndinu woleza mtima banja lanu lingalimbenso m’kupita kwa nthawi.—Mlal. 7:8; 1 Akor. 13:4.

BWANJI NGATI ZIKUMUVUTA KUSIYA?

Mwamuna wanu akaonelelanso zamalisece pambuyo poyesetsa kuzipewa kwa kanthawi, kodi zitanthauza kuti ni wosalapa, kapena kuti sangathetse cizolowezico? Osati kwenikweni. Angafunike kulimbana na khalidwelo kwa moyo wake wonse, maka-maka ngati linazika mizu. Iye angaonelelenso za malisece ngakhale pambuyo pozipewa kwa zaka. Kuti asakabwelezenso, iye ayenela kudziikila citetezo cokhwima kuti asakagwelenso m’mayeselo ngakhale pamene zaoneka kuti vutolo linatha. (Miy. 28:14; Mat. 5:29; 1 Akor. 10:12) Iye ayenela kukhala watsopano mu “mphamvu yoyendetsa maganizo” ake, na kuphunzila ‘kudana naco coipa’—zamalisece komanso makhalidwe ena oipa monga kudzipukusa malisece. (Aef. 4:23; Sal. 97:10; Aroma 12:9) Kodi niwokonzeka kupanga masinthidwe amenewa? Ngati n’telo, n’zotheka kuthetselatu vutolo. e

Muziika maganizo anu pa ubale wanu na Yehova

Nanga bwanji ngati mwamuna wanu safuna kusintha? N’kutheka kuti nthawi zambili mungapwetekedwe mtima, kukhumudwa, na kuona kuti munaputsitsidwa. Pezani mtendele wa mumtima mwa kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. (1 Pet. 5:7) Pitilizani kuyandikila Yehova mwa kucita phunzilo la inu mwini, kupemphela, na kusinkhasinkha. Mukamacita zimenezi, khalani otsimikiza kuti nayenso akukuyandikilani. Monga imakambila Yesaya 57:15, Iye amakhala na anthu ‘opsinjika ndi amtima wodzicepetsa’ kuti awatsitsimule. Yesetsani kukhala Mkhristu wabwino. Muzipempha thandizo kwa akulu. Ndipo khalani na ciyembekezo cakuti pa nthawi ina mtsogolo, mwamuna wanu angasinthe.—Aroma 2:4; 2 Petulo 3:9.

a Kuti mfundoyi imveke mosavuta, m’nkhani ino tizichula mwamuna pa mbali ya woonelela zamalisece. Koma mfundo zake zingathandizenso mwamuna amene mkazi wake amaonelela zamalisece.

b Kuonelela zamalisece si cifukwa ca m’Malemba cothetsela ukwati.—Mat. 19:9.

c Maina ena asinthidwa.

d Mungapeze mfundo zothandiza pa jw.org na m’zofalitsa zathu. Mwacitsanzo, onani nkhani yakuti, “Pornography Can Shatter Your Marriage” pa jw.org; “Mungathe Kukana Mayesero!” mu Nsanja ya Mlonda ya, April 1, 2014, masa. 10-12; komanso yakuti “Kodi Zamalisece Zilibe Vuto?” mu Nsanja ya Mlonda ya, August 1, 2013, masa. 3-7.

e Cifukwa cakuti cikhumbo coonelela zamalisece cimakhala camphamvu, okwatilana ena asankha kupempha thandizo kwa akatswili pa nkhani imeneyi kuwonjezela pa thandizo lauzimu limene akulu amapeleka.