Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Munthu Wokondedwa Akamwalila

Munthu Wokondedwa Akamwalila

Vanessa wa ku Australia anati: “Mkulu wanga wamwamuna atamwalila mosayembekezeleka, n’nathedwa nzelu. Kwa miyezi ingapo, cinali kuniŵaŵa nikakumbukila imfa yake. N’nali kumvela monga kuti wina akunilasa na mpeni kumtima. Nthawi zina n’nali kukhala wokhumudwa. N’nali kudzifunsa kuti, n’cifukwa ciani mlongosi wanga anamwalila? N’nadziimba mlandu cifukwa cosapeza nthawi yokwanila yoceza naye akali moyo.”

NGATI munafedwapo munthu wokondedwa, n’kutheka kuti na imwe munamvela cisoni, kuthedwa nzelu, komanso kumuyewa wokondedwa wanu. Mwina munacita mantha, kukhumudwa na kudziimba mlandu. Mwinanso munayamba kuona kuti kukhala na moyo kulibe phindu.

Dziŵani kuti kumva cisoni sikutanthauza kuti ndimwe wosalimba. Kumangoonetsa cikondi cimene munali naco pa munthuyo. Koma kodi n’zotheka kupezako citonthozo ku cisoni ca imfa?

ZIMENE ZATHANDIZA ENA

Ngakhale kuti zingaoneke monga cisoni canu sicidzatha, malangizo otsatilawa angakuthandizeni:

MUKACITA CIFUNDO, OSAYOPA KULILA

Ife anthu timalila malilo mosiyana-siyana, komanso kwa utali wosiyana-siyana. Ndipo kulila kungathandize kucepetsako cisoni. Vanessa, amene tam’gwila mawu pamwambapa anati: “N’nali kuti cifundo cikanigwila, n’nali kulila kuti nimveleko bwino pang’ono.” Nayenso Sofía amene mng’ono wake anamwalila mwadzidzidzi anati, “Nikakumbukila imfa yake, cimaniŵaŵa ngako. Cili monga kumatula cilonda cacikulu na kutsukapo. Ululu wake umamveka wosapililika, koma kumathandiza kuti cilondaco cipole.”

UZANKONI ENA MAGANIZO ANU NA MMENE MUMVELELA

N’zoona kuti nthawi zina mungafune kukhala pamwekha. Koma cisoni cili monga katundu wolema umene simungaunyamule mwekha. Jared wa zaka 17, amene atate ake anamwalila anati, “N’nali kuuzako ena mmene n’nali kumvelela. Mwina zokamba zanga sizinali kumveka bwino-bwino, n’nali kungofuna kukamba na munthu.” Janice, amene tam’gwila mawu m’nkhani yoyamba, anachulanso ubwino wina. Iye anati: “Kuuzako ena kunali kunitonthoza kwambili. N’naona kuti anthu anali kunimvetsa cakuti sin’nali kukhala wosungulumwa.”

MUSAKANE THANDIZO

Dokotala wina anati: “Ofedwa amene amalola mabwenzi ndi acibululu kuwatonthoza na kuwathandiza imfa ikacitika, amakwanitsako kupilila cisoni ca imfa.” Auzeni anzanu zimene angacite kuti akuthandizeni. Iwo angafune kuthandiza koma osadziŵa zocita.—Miyambo 17:17.

MUYANDIKILENI KWAMBILI MULUNGU

Tina anati: “Mwamuna wanga atamwalila na matenda a khansa, n’nalibenso wouzako nkhawa zanga. Conco, n’nayamba kuuza Mulungu nkhawa zanga zonse! Nikangouka tsiku lililonse, n’nali kum’pempha kuti akhale nane tsiku lonse. Mulungu ananithandiza m’njila zambili cakuti siningakwanitse kuzifotokoza.” Tarsha, amene anali na zaka 22 pamene amayi ake anamwalila anati: “Kuŵelenga Baibo tsiku lililonse kunali kunitonthoza. Kunali kunithandiza kuganizila zinthu zolimbikitsa.”

MUZIONA KUUKA KWA AKUFA M’MAGANIZO MWANU

Tina anapitiliza kuti: “Poyamba, ciyembekezo cakuti akufa adzauka sicinan’tonthoze, cifukwa n’nali kufuna mwamuna wanga. Nawonso ana anga anali kufuna atate awo. Koma lomba papita zaka zinayi, ndipo nacigwila mwamphamvu ciyembekezo cimeneci. Cimanilimbikitsa kwambili. Nimayelekezela kuti namuonanso ataukitsidwa. Kucita izi kumanibweletsela mtendele wa m’maganizo, komanso cimwemwe!”

Malilo akangocitika, sikuti cisoni cidzacepa nthawi yomweyo. Komabe, zimene Vanessa anakamba zingakulimbikitseni. Iye anati, “Poyamba zimaoneka monga cisoni sicidzatha. Koma pang’ono m’pang’ono cimayamba kucepa.”

Kumbukilani kuti, ngakhale simungamuiŵaliletu wokondedwa wanu amene anamwalila, kukhala na moyo n’kofunikabe. Na thandizo lacikondi la Mulungu, mungasangalalebe na mabwenzi abwino, komanso kukhala na umoyo waphindu. Ndipo posacedwa Mulungu adzaukitsa akufa. Iye amafuna kuti mukaonanenso na okondedwa anu. Panthawiyo, cisoni conse ca imfa cimene cili mumtima mwanu cidzathelatu!