Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

THANDIZO KWA OFEDWA

Zimene Mungacite Palipano Mukafedwa

Zimene Mungacite Palipano Mukafedwa

Ngati mungafufuze malangizo a mmene mungapililile cisoni, mwacionekele mudzapeza mfundo zambili-mbili, zina zothandiza kwambili kuposa zina. Ndipo zili conco cifukwa anthu amalila malilo mosiyana-siyana, monga mmene takambila kale. Zimene zingakhale zothandiza kwa munthu wina sizingakhale zothandiza kwa wina.

Ngakhale n’conco, pali mfundo zina zimene zakhala zothandiza kwa anthu ambili. Kaŵili-kaŵili, alangizi a anthu ofedwa amalimbikitsa mfundo zimenezi, ndipo zimagwilizana na mfundo zimene sizisintha, zopezeka m’buku yakale ya nzelu, Baibo.

1: LANDILANI THANDIZO KWA ACIBULULU NA MABWENZI

  • Akatswili ena amaona kuti njila imeneyi ni yothandiza kwambili kuti munthu apilile cisoni. Koma nthawi zina, mungafune kukhala pamwekha. Mwina mungafike pokwiila amene akuyesa kukuthandizani. Izi zisakudabwitseni. Nthawi zambili ndiye mmene zimakhalila.

  • Musaganize kuti nthawi zonse mufunika kukhala pakati pa anthu, komanso musawaletse kukufikilani. Ndipo mwina mukhoza kukafuna thandizo lawo kutsogolo. Mokoma mtima, adziŵitseni zimene mufuna palipano, komanso zimene simufuna.

  • Malinga na zimene mufunikila, gaŵani bwino nthawi yokhala na anthu ena komanso yokhala pamwekha.

MFUNDO YAKE: “Aŵili amaposa mmodzi . . . Ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kum’dzutsa mnzakeyo.”—Mlaliki 4:9, 10.

2 Muzidya Zakudya Zopatsa Thanzi, Komanso Muzicita Maseŵela Olimbitsa Thupi

  • Kudya zakudya zopatsa thanzi kudzakuthandizani kugonjetsa nkhawa imene imakhalapo popilila cisoni. Muzidya zipatso zosiyana-siyana, ndiyo zamasamba, komanso zakudya zopanda mafuta kwambili.

  • Muzimwa madzi kwambili komanso zakumwa zina zopatsa thanzi.

  • Ngati mulibe cifuno cakudya mokwanila, mungamadye cakudya cocepa pafupi-fupi. Mungafunsenso adokota zakudya zina zopatsa thanzi. *

  • Kuyenda ndawala na kucita maseŵela ena olimbitsa thupi, kungakuthandizeni kucepetsa maganizo olefula. Kwa ena, maseŵela olimbitsa thupi amawathandiza kuvomeleza kusintha kwa zinthu mu umoyo wawo. Koma kwa ena amawathandiza kuti asamangoganizila za imfa ya wokondedwa wawo.

MFUNDO YAKE: “Pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.”—Aefeso 5:29.

3: MUZIGONA MOKWANILA

  • Kugona n’kofunika kwambili, maka-maka kwa ofedwa, popeza cisoni cimalefula kwambili.

  • Pewani kumwa zakumwa za caffeine monga khofi, komanso kumwa moŵa kwambili. Cifukwa izi zingakusonezeni tulo.

    MFUNDO YAKE: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwila nchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”—Mlaliki 4:6.

4: SEŴENZETSANI NJILA ZOTHANDIZA KWA IMWE

  • Kumbukilani kuti anthu amalila malilo mosiyana-siyana. Conco, mudzafunika kusankha mfundo zimene zingakhale zothandiza kwa imwe.

  • Ambili amaona kuti kufotokozela anzawo mmene amvelela, kumawathandiza kupilila imfa. Koma ena amaona kuti ni bwino kusafotokozela anzawo. Akatswili ali na maganizo osiyana-siyana pa nkhani imeneyi. Akatswili ena amakhulupilila kuti kufotokozela ena mmene umvelela n’kothandiza, pamene ena amati n’kosathandiza. Ngati mufuna kufotokozelako wina mmene mumvelela, koma musoŵa poyambila, mwina mungayambe kuuzako bwenzi lanu lapamtima zinthu zocepa.

  • Anthu ena amaona kuti kulila kumawathandiza kupilila cisoni. Koma ena amapilila ngakhale kuti salila kwambili.

MFUNDO YAKE: “Mtima umadziŵa kuŵaŵa kwa moyo wa munthu.”—Miyambo 14:10.

5: PEWANI ZIZOLOŴEZI ZOKUWONONGANI

  • Ofedwa ena pofuna kucepetsako cisoni, amamwa moŵa mopitilila malile kapena kuseŵenzetsa amkola bongo. “Kuiŵalako” mavuto mwa njila imeneyi n’kudziwononga. Ndipo kumvelako bwino kumene munthu angapeze n’kwa kanthawi. Koma zotulukapo zake zingabweletse mavuto aakulu. Conco, pofuna kucepetsako cisoni seŵenzetsani njila zimene sizingakuwonongeni.

MFUNDO YAKE: “Tiyeni tidziyeletse ndipo ticotse cinthu ciliconse coipitsa thupi.”—2 Akorinto 7:1.

6: MUZISEŴENZETSA BWINO NTHAWI YANU

  • Ambili amapeza kuti kucita zinthu zina kumawathandiza kucepetseko cisoni cawo.

  • Mungapezeko citonthozo mwa kupanga mabwenzi atsopano kapena kulimbitsa maubwenzi amene alipo kale, kuphunzila maluso atsopano, kapena kucitako zosangalatsa.

  • M’kupita kwa nthawi zinthu zingasinthe. Mudzaona kuti pang’ono-m’pang’ono mudzayamba kutenga nthawi yaitali simukuganizila za imfa ya wokondedwa wanu. Umu ni mmene munthu amafikila pocila ku cisoni.

MFUNDO YAKE: “Ciliconse cili ndi nthawi yake, . . . nthawi yolila ndi nthawi yoseka. Nthawi yolila mofuula ndi nthawi yodumphadumpha mosangalala.”—Mlaliki 3:1, 4.

7: PITILIZANI KUTSATILA PULOGILAMU YANU YA ZOCITA

  • Mwamsanga, yambaninso kucita zinthu zimene munali kucita tsiku na tsiku.

  • Ngati mutsatila pulogilamu yanu monga kugwila nchito, nthawi yogona, na zocita zina, mwacionekele zinthu zidzakhalanso m’malo mwake.

  • Kukhala wotangwanika na zinthu zabwino kudzakuthandizani kucepetsa cisoni canu.

MFUNDO YAKE: “Zoŵaŵa za pamoyo wake waufupi sazizikumbukila kaŵilikaŵili, cifukwa Mulungu woona akucititsa kuti mtima wake uzisangalala.” —Mlaliki 5:20.

8: PEWANI KUPANGA ZOSANKHA ZIKULU-ZIKULU MWAMSANGA

  • Ambili amene amapanga zosankha zikulu-zikulu mwamsanga pambuyo pakuti wokondedwa wawo wamwalila, amadziimba mlandu pambuyo pake.

  • Ngati n’kotheka, yembekezelani kwa kanthawi musanapange cosankha cokuka, kusintha nchito, kapena kutaya zinthu zina za wokondedwa wanu.

MFUNDO YAKE: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulila, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.”—Miyambo 21:5.

9: MUZIM’KUMBUKILA WOKONDEDWA WANU

  • Ofedwa ambili apeza kuti n’kothandiza kucita zinthu zimene zimapangitsa kuti azikumbukila wokondedwa wawo amene anamwalila.

  • Mungapeze citonthozo mwa kusunga masinapu, kapena zinthu zina zokukumbutsani wokondedwa wanu. Mungakhalenso na kabuku kolembamo zocitika na nkhani zina zimene mungafune kuti muzizikumbukila.

  • Sungani zinthu zimene zingakukumbutseni zocitika zosangalatsa, kuti muziziona mukafuna kutelo.

MFUNDO YAKE: “Kumbukilani masiku akale.”—Deuteronomo 32:7.

10: PEZANI NTHAWI YOCITA ZOSANGALATSA

  • Mwina mungatenge chuti.

  • Ngati n’zosatheka kutenga chuti ca nthawi yaitali, mwina mungaciteko zinthu zina zosangalatsa kwa tsiku limodzi kapena aŵili. Mwacitsanzo, mungapite kokayenda, kukaona malo osungilako zinthu zakale, kapena kuyendetsa motoka.

  • Kucita zinthu zina zosiyanako na zimene mumacita tsiku na tsiku, olo mwacidule, kungakuthandizeni kupilila cisoni.

MFUNDO YAKE: “Inuyo bwelani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.”—Maliko 6:31.

11: MUZITHANDIZA ENA

  • Kumbukilani kuti nthawi iliyonse imene mungapatule kuthandiza ena, na imwe ingakuthandizeni kuti mumveleko bwino.

  • Mungayambe mwa kuthandiza amene akhudzidwa na imfa ya wokondedwa wanu, monga mabwenzi, kapena acibululu amene angafune wolila naye

  • Kuthandiza ena na kuwatonthoza kungakupangitseni kukhalanso wacimwemwe, komanso kuona kuti moyo wanu uli na phindu.

MFUNDO YAKE: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” —Machitidwe 20:35.

12: YANG’ANANINSO ZOCITA ZANU KUTI MUONE ZOFUNIKA KWENI-KWENI

  • Nthawi yolila ingakuthandizeni kuzindikila zinthu zofunika kwambili.

  • Tengelamponi mwayi wodzifufuza kuti muone mmene museŵenzetsela umoyo wanu.

  • Sinthani zina mwa zimene mumacita ngati m’pofunika kutelo.

MFUNDO YAKE: “Ndi bwino kupita kunyumba yamalilo kusiyana ndi kupita kunyumba yamadyelelo, cifukwa amenewo ndiwo mapeto a anthu onse. Cotelo munthu amene ali moyo aziganizila zimenezi mumtima mwake.”—Mlaliki 7:2.

Kukamba zoona, palibe cimene cingatsiliziletu cisoni cobwela na imfa. Komabe, ambili amene anataikilidwa okondedwa awo, aona kuti kucita zimene tafotokoza m’nkhani ino, kwaŵathandiza kupeza citonthozo. Koma sikuti tapeleka njila zonse zocepetsela cisoni. Mukayesa kuseŵenzetsa zina mwa njila zimenezi, mudzaona kuti zidzakuthandizani kucepetsa cisoni.

^ ndime 13 Galamuka! siiuza anthu zocita pa nkhani ya zakudya