Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pamene Mwadwala Matenda Aakulu

Pamene Mwadwala Matenda Aakulu

Linda wa zaka 71 anati: “Nitadziŵa kuti nili na khansa m’mapapo komanso m’matumbo, n’namvela monga kuti nagamulidwa kukapika jele kwa moyo wanga wonse. Pamene n’nafika kunyumba pambuyo poonana na dokotala, n’nati, ‘Izi si zimene n’nali kuyembekezela, nifunika kupeza njila imene inganithandize kupilila.’”

Elise wa zaka 49 anati: “Nili na matenda amene amapangitsa kuti mbali ya kumanzele ya kumaso iziŵaŵa kwambili. Nthawi zina kuŵaŵa kumeneku kumanipangitsa kuvutika maganizo. Ndipo nthawi zambili n’nali kuona monga kuti palibe anganithandize, cakuti n’nafuna kudzipha cabe.”

NGATI IMWE kapena munthu amene mumam’konda anamupeza na matenda aakulu akuti angafe nawo, mungamvetse mmene zimavutitsila maganizo. Kuwonjezela pa matendawo, pamakhalanso zina zovutitsa maganizo monga izi: Mantha komanso nkhawa pokaonana na madokotala, kusapeza msanga cithandizo kapena kusoŵa ndalama zopezela cithandizo, kapenanso mavuto ena obwela cifukwa ca kumwa mankhwala. Conco, matenda aakulu amabweletsa nkhawa zambili zosautsa.

Nanga kodi tingapeze kuti thandizo? Ambili apeza citonthozo cacikulu kwambili mwa kupemphela kwa Mulungu, komanso kuŵelenga mavesi otonthoza a m’Baibo. Tingapezenso citonthozo pamene acibululu na mabwenzi ationetsa cikondi, komanso kutithandiza.

ZIMENE ZATHANDIZA ENA

Robert wa zaka 58 anati: “Khalani na cikhulupililo mwa Mulungu pamene mulimbana na matenda, ndipo adzakuthandizani kuti mupilile. Kambani na Yehova m’pemphelo. Muuzeni mmene mumvelela. M’pempheni mzimu woyela. M’pempheni kuti akuthandizeni kukhala wolimbikitsa kwa a m’banja lanu, komanso kuti mukhale woleza mtima pamene mukupilila matenda anu.”

Robert anakambanso kuti: “Zimakhala zothandiza kwambili ngati acibululu akulimbikitsa. Tsiku lililonse abululu anga aŵili kapena mmodzi amanitumila foni ndipo amanifunsa kuti, ‘Kaya mumvelako bwanji?’ Anzanga ocokela kumadela osiyana-siyana amanilimbikitsa. Iwo amanitsitsimula ndipo zimenezi zimanithandiza kuona kuti moyo ni wofunikabe.”

Ngati mwapita kukaona mnzanu wodwala, mungacite bwino kuganizila zimene Linda anakamba. Iye anati: “Mosakaikila, munthu wodwala nayenso amafuna kukhala na umoyo wabwino-bwino, ndipo sangakonde kuti nthawi zonse muzingokhalila kukambilana za matenda ake. Conco ni bwino kukambilana nkhani zimene m’makambilana nthawi zonse.”

Mwa mphamvu za Mulungu, citonthozo ca m’Malemba, komanso thandizo la acibululu ndi anzathu amene amatikonda, tingakhalebe otsimikiza kuti moyo ni wofunika ngakhale pamene tipilila matenda aakulu.