Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kukambilana pasadakhale ndi momasuka n’kofunika

Munthu Amene Mukonda Akadwala Matenda Osacilitsika

Munthu Amene Mukonda Akadwala Matenda Osacilitsika

DOREEN anadabwa kwambili poona kuti mwamuna wake Wesley, wa zaka 54, anamupeza na cotupa cacikulu ku ubongo. * Madokota anakamba kuti mwamuna wake adzangokhala miyezi yocepa, ndipo adzamwalila. Iye anati: “Sin’nakhulupilile zimene madokota anakamba. N’navutika maganizo kwa mawiki angapo. N’naona monga kuti zikucitikila munthu wina osati ise. Sin’nali wokonzeka.”

Anthu ambili amamvela monga mmene Doreen anamvelela. Munthu aliyense angadwale matenda osacilitsika pa nthawi iliyonse. Koma cokondweletsa n’cakuti anthu ambili amadzipeleka kuti asamalile munthu amene amakonda yemwe akudwala matenda osacilitsika. Komabe, kusamalila munthu wodwala n’kovuta. N’ciani cimene mabanja angacite kuti asamalile na kutonthoza m’bululu wawo wodwala matenda osacilitsika? Kodi odwazika angacite ciani kuti alimbane ndi nkhawa zimene zimakhalapo? Ngati wodwalayo ali pafupi kumwalila, kodi mungacite ciani? Tisanayankhe mafunso aya, coyamba tiyeni tione cifukwa cake kusamalila wodwala matenda osacilitsika n’kovuta.

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Sayansi ya zamankhwala yathandizako kuti odwala asamamwalile msanga. Zaka 100 kapena kuposapo kumbuyoku, munthu anali kukhala na moyo zaka zocepa, ngakhale m’maiko olemela. Anthu anali kumwalila msanga cifukwa ca matenda oyambukila kapena cifukwa ca ngozi. Zipatala zinali zocepa. Conco, anthu ambili odwala anali kusamalidwa kunyumba ndi acibale awo, ndipo anali kumwalilila m’nyumba.

Masiku ano, kupita patsogolo m’zamankhwala kwathandiza madokota kugwebana ndi matenda pofuna kutalikitsako moyo. Matenda amene kale anali kupha munthu mwamsanga apa lomba amatenga zaka zambili. Koma kutalikitsa moyo mwa njila imeneyi sikutanthauza kuti munthuyo wacililatu. Nthawi zambili, odwalawo amapezeka na matenda ena aakulu amene amawapangitsa kulephela kudzisamalila okha. Kusamalila anthu amenewa n’kovuta kwambili komanso n’kolemetsa.

Masiku ano, anthu ambili amafela kucipatala osati kunyumba. Ambili sadziŵa zimene zimacitika munthu akatsala pafupi kumwalila, ndipo ni ocepa cabe amene anaonapo munthu akumwalila. Poopa zam’tsogolo, munthu angalephele kapena kucita ulesi kusamalila wacibale amene akudwala. N’ciani cingathandize?

KONZEKELANI ZA KUTSOGOLO

Monga mmene zinalili kwa Doreen, anthu ambili amavutika maganizo ngati munthu amene amakonda akudwala matenda akupha. Mukakhala na nkhawa yaikulu, mantha, ndi cisoni, n’ciani cingakuthandizeni kukonzekela za kutsogolo? Mtumiki wa Mulungu wokhulupilika anapemphela kuti: “Tisonyezeni mmene tingaŵelengele masiku athu kuti tikhale ndi mtima wanzelu.” (Salimo 90:12) Inde, pemphani Yehova Mulungu mocokela pansi pa mtima kuti akuonetseni mmene ‘mungaŵelengele masiku anu’ mwanzelu, kuti nthawi yocepa imene yatsala kwa wodwalayo muiseŵenzetse m’njila yabwino koposa.

Izi zimafuna kukonzekela bwino. Ngati wodwalayo akukwanitsa kukamba ndipo angakonde kukambapo maganizo ake, cingakhale bwino kumufunsa kuti asankhe munthu amene angazim’pangila zosankha zikafika poti iye sakwanitsa kukamba. Kukambilana moona mtima ngati wodwalayo angafunike kumuika ku mashini opumila, kumucita adimiti m’cipatala, kapena kulandila mankhwala akuti-akuti, kungacepetse mikangano komanso kudziimba mlandu kumbali ya acibanja amene akupangila zosankha wodwala amene sakwanitsa kucita ciliconse. Kukambilana pasadakhale komanso momasuka kumathandiza acibanja kuika maganizo awo pa kusamalila wodwalayo. Baibo imati: “Zolingalila sizikwanilitsidwa ngati anthu sakambilana moona mtima.”—Miyambo 15:22.

MMENE MUNGATHANDIZILE

Mbali yaikulu ya osamalila wodwala ni kupeleka citonthozo. Munthu amene watsala pang’ono kumwalila afunika kum’tsimikizila kuti mumam’konda ndi kuti simudzam’siya. Mungacite bwanji zimenezi? Mungamuŵelengele nkhani zimene amakonda kapena kumuimbilako tunyimbo tumene tumam’limbikitsa na kumusangalatsa. Anthu odwala amatonthozeka ngati wam’banja lawo wawagwila dzanja na kukamba nawo mokoma mtima.

Zimakhala bwino nthawi zambili kuchula dzina la aliyense wobwela kudzaona wodwala. Buku lina linati: “Pa mphamvu 5 zimene munthu ali nazo, mphamvu ya kumvela ndiyo imatsilizila kutha. Odwala akhozabe kumvela pang’ono, olo kuti akuoneka kuti agona. Conco, musakambe ciliconse cimene simungafune kukamba iwo ali maso.”

Ngati n’kotheka, pemphelani capamodzi. Baibo imakamba kuti panthawi ina, mtumwi Paulo pamodzi ndi anzake anavutika kwambili ndipo ngakhale miyoyo yawo inali paciwopsezo. Kodi n’kuti kumene anapeza thandizo? Paulo anapempha anzake kuti: “Inunso mungathandizepo mwa kutipelekela mapembedzelo anu.” (2 Akorinto 1:8-11) Conco, pemphelo locokela pansi pamtima n’lothandiza maningi nkhawa zikatikulila kapena wina akadwala mwakaya-kaya.

MUZIONA ZINTHU MOYENELELA

Kudziŵa kuti munthu amene timakonda adzamwalila kumavutitsa maganizo. N’cifukwa cake imfa ilibe kuti n’nazoloŵela. Ife anthu sitinalengedwe kuti tizikumana ndi imfa mu umoyo wathu. (Aroma 5:12) Mau a Mulungu amachula imfa kuti “mdani.” (1 Akorinto 15:26) Conco, m’pomveka ndipo n’cibadwa kusafuna kuganizila za imfa ya munthu amene timakonda.

Ngakhale n’conco, kuganizila zimene zingacitike kungathandize acibale a wodwala kucepetsa mantha na kuika maganizo awo pa zinthu zimene zingawakhazike mtima pansi. Zizindikilo zoonetsa kuti munthu wakhala pafupi kumwalila zandandalikidwa pa bokosi lakuti “ Wodwala Akakhala Pafupi Kumwalila.” Sikuti zonse zochulidwa pamenepa zimaonekela mwa wodwala aliyense kapena mmene azindandalikila iyai. Komabe, zina mwa zizindikilozo zimaonekela mwa odwala ambili.

Wodwalayo akamwalila, zingakhale bwino kudziŵitsa mnzanu wodalilika amene anavomela kukuthandizani. Mungadziŵitsenso amene anali kusamalila wodwalayo ndi acibale kuti wamwalila, ndi kuti sakuvutikanso. Mlengi wa anthu onse amatitsimikizila kuti “akufa sadziŵa ciliconse.”—Mlaliki 9:5.

WOSAMALILA WAMKULU

Sitiyenela kukana thandizo iliyonse

Kudalila Mulungu n’kofunika kwambili, osati cabe pamene wacibale wanu wadwala mwakayakaya, koma ngakhalenso pamene muli na cisoni wodwalayo akamwalila. Iye angakuthandizeni kupitila m’mau a anthu ena ndi thandizo lawo. Doreen anati “N’naphunzila kuti siniyenela kukana thandizo iliyonse. Ndipo thandizo yocepa imene tinalandila inatitsitsimula. Ine na amuna anga tinamvela monga kuti Yehova akutiuza kuti, ‘Nili na imwe kuti nikuthandizeni pa mavuto anu.’ Sinidzaiŵala zimenezo.”

Zoona, Yehova Mulungu ndiye Wotisamalila wamkulu. Popeza ndiye Mlengi wathu, amamvetsetsa tikavutika maganizo komanso tikakhala na cisoni. Iye ni wofunitsitsa kutithandiza na kutilimbikitsa kuti tilimbane na mavuto. Cokondweletsa n’cakuti anatilonjeza kuti posacedwa adzacotsapo imfa kwamuyaya, na kuukitsa anthu mabiliyoni amene ali m’cikumbukilo cake. (Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 21:3, 4) Ndiyeno, onse adzakamba mau a mtumwi Paulo akuti: “Imfa iwe, kupambana kwako kuli kuti? Imfawe, mphamvu yako ili kuti?”—1 Akorinto 15:55.

^ par. 2 Maina tawasintha.