Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

N’cifukwa Ciani​—Pali ma Baibo Osiyana-siyana?

N’cifukwa Ciani​—Pali ma Baibo Osiyana-siyana?

N’cifukwa ciani pali zimasulilo zambili zosiyana-siyana za Baibo masiku ano? Kodi mamasulidwe atsopano a Baibo amakuthandizani kuimvetsetsa kapena ayi? Kudziŵa ciyambi cake kungakuthandizeni kuwayelekezela bwino.

Koma coyamba tifunse kuti, n’ndani analemba Baibo paciyambi? Nanga anailemba liti?

BAIBO YOYAMBILILA

Nthawi zambili, Baibo imagaŵidwa m’zigawo ziŵili. Cigawo coyamba cili na mabuku 39, ndipo muli “mawu opatulika a Mulungu.” (Aroma 3:2) Mulungu anauzila amuna okhulupilika kulemba mabuku amenewa pa nthawi yaitali. Anawalemba pafupi-fupi zaka 1,100 kuyambila mu 1513 B.C.E. mpaka ca kumapeto kwa caka ca 443 B.C.E. Ambili mwa mabuku amenewa anawalemba m’Ciheberi, ndiye cifukwa cake cigawo cimeneci timacicha Malemba a Ciheberi, cimadziŵikanso kuti Cipangano Cakale.

Cigawo caciŵili cili na mabuku 27 amenenso ni “mawu a Mulungu.” (1 Atesalonika 2:13) Mulungu anauzila ophunzila a Yesu Khristu okhulupilika kulemba mabuku amenewa pa nthawi yocepa. Anawalemba pafupi-fupi zaka 60 kuyambila mu 41 C.E. kufika mu 98 C.E. Ndipo ambili analembedwa m’Cigiriki, conco cigawo cimeneci timacicha Malemba Acigiriki Acikhiristu, cimadziŵikanso kuti Cipangano Catsopano.

Mabuku 66 ouzilidwa amenewa onse pamodzi amapanga Baibo yathunthu—Uthenga wocoka kwa Mulungu kupita kwa anthu. Nanga n’cifukwa ciani panafunika zimasulilo zina za Baibo? Onani zifukwa zitatu zotsatilazi.

  • Kuti anthu aziŵelenga Baibo m’citundu cawo.

  • Kuti acotsemo zolakwa zimene zinapangidwa pokopela, na kubwezamo mau ake a paciyambi.

  • Kuti acotsemo mau ena acikale na kuikamo ena osavuta kumva.

Onani mmene anatsatilila mfundo zimenezi pomasulila ma Baibo aŵili oyambilila.

BAIBO YA CIGIRIKI YA SEPTUAGINT

Pafupifupi zaka 300 Yesu asanabadwe, akatswili odziŵa Ciyuda anayamba kumasulila Malemba a Ciheberi m’citundu ca Cigiriki. Baibo imene anamasulila inayamba kuchedwa kuti Baibo ya Cigiriki ya Septuagint. N’cifukwa ciani anaimasulila? Kuti athandize Ayuda ambili amene panthawiyo anali kukamba Cigiriki m’malo mwa Ciheberi, kuti amve “malemba oyela.”—2 Timoteyo 3:15.

Baibo ya Septuagint inathandizanso anthu mamiliyoni ambili amene sanali Ayuda ndipo anali kukamba Cigiriki, kudziŵa zimene Baibo imaphunzitsa. Inawathandiza bwanji? Pulofesa W. F. Howard anakamba kuti: “Kuyambila capakati pa zaka 100 zoyambilila, Baibo ya Septuagint inakhala ya machechi achikhristu. Amishonale a machechiwo anali kuyenda m’masunagoge ‘kufotokoza ndi kusonyeza umboni wolembedwa wakuti Yesu ndiye Mesiya.’” (Machitidwe 17:3, 4; 20:20) Ici ndiye cifukwa cimodzi cinacititsa Ayuda “kusuliza Baibo ya Septuagint,” malinga na zimene katswili wina wa Baibo dzina lake F. F. Bruce anakamba.

Ophunzila a Yesu akalandila mabuku a Malemba Acigiriki Acikhristu, anali kuwaphatikiza pamodzi na Baibo ya Septuagint ya Malemba Aciheberi na kupanga Baibo ya thunthu imene tili nayo masiku ano.

BAIBO YA M’CILATINI YOCHEDWA VULGATE

Patapita zaka 300 Baibo itatha kulembedwa, katswili wina wa zacipembedzo dzina lake Jerome anatulutsa Baibo ya m’Cilatini, imene m’kupita kwa nthawi, inadzachedwa Latin Vulgate. Ma Baibo a m’Cilatini analiko osiyana-siyana. Nanga n’cifukwa ciani panafunika ina yatsopano? Buku ya The International Standard Bible Encyclopedia inati: “Jerome anafuna kukonzanso mau ena amene sanamasulidwe bwino, kukonza zimene zinalakwika, kucotsamo mau ena osafunika amene anawonjezelamo, na kubwezeletsa mau ena amene anacotsedwamo.”

Jerome anakonza zambili mwa zolakwika zimenezi. Koma patapita nthawi, akulu-akulu a machechi anapanga colakwa cacikulu. Iwo analengeza kuti Baibo ya Latin Vulgate ndiyo Baibo yokha yololeka, ndipo anacita zimenezi kwa zaka zambili. M’malo mothandiza anthu wamba kumvetsetsa Baibo, Baibo imeneyi inacititsa kuti anthu azilephela kuimvetsetsa, cifukwa m’kupita kwa nthawi anthu sanali kudziŵa Cilatini olo pang’ono.

ZIMASULILO ZA BAIBO ZIWONJEZELEKA

Anthu anapitiliza kutulutsa ma Baibo ena atsopano. Mwacitsanzo, ca m’ma 400 C.E. anatulutsa Baibo ina yochuka yochedwa Syriac Peshitta. Koma ca m’ma 1300 C.E., m’pamene anapanganso makonzedwe ena akuti anthu wamba aziŵelenga Baibo m’citundu cawo.

Kumapeto kwa zaka za m’ma 1300 C.E., John Wycliffe wa ku England anayamba kumasulila na kutulutsa Baibo m’Cizungu cimene ngakhale anthu wamba anali kumvela. M’kupita kwa nthawi, Johannes Gutenberg atayamba zopulinta-pulinta, akatswili ambili a Baibo anayamba kutulutsa ma Baibo osiyana-siyana m’zinenelo zambili zimene anthu anali kukamba zungulile Europe yonse.

Pamene ma Baibo a m’Cizungu anaculuka, anthu otsutsa anakamba kuti sikunali kofunikila kutulutsa ma Baibo osiyana-siyana m’citundu cimodzi. Mu 1700 C.E., mzungu wina amene anali mtsogoleli wacipembedzo, dzina lake John Lewis analemba kuti: “Citundu cimasila, conco n’kofunika kukonzanso ma Baibo ena akale kuti akhale na Citundu cimene anthu amakamba, cimene m’badwo umene ulipo ungamvetsetse.”

Masiku ano kuposa kale lonse, akatswili a Baibo ndiwo ali pa malo oyenelela opendanso ma Baibo ena akale. Iwo amamvetsetsa bwino ngako zinenelo zakale za m’Baibo, ndipo ali na mipukutu imene inapezeka posacedwa. Izi zimawathandiza kudziŵa mau enieni apaciyambi a m’Baibo.

Conco kukhala na zimasulilo zatsopano za Baibo n’kothandiza kwambili. Koma tiyenela kusamala na ma Baibo ena. * Komabe, tingapindule kwambili ngati okonzanso Baibo angacite zimenezo cifukwa cokonda kwambili Mulungu.

 

^ par. 24 Onani nkhani yakuti, “Kodi Mungadziwe Bwanji Baibulo Lomasuliridwa Bwino?” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2008.