Onani zimene zilipo

N’cifukwa Ciani Mboni za Yehova Sizikondwelela Khrisimasi?

N’cifukwa Ciani Mboni za Yehova Sizikondwelela Khrisimasi?

Zimene Ambili Amaganiza

 Bodza limene amakamba: A Mboni za Yehova sakondwelela Khrisimasi cifukwa cakuti sakhulupilila Yesu.

 Ndife Akhristu. Ndipo timakhulupilila kuti tingapeze cipulumutso kupitila mwa Yesu Khristu cabe.—Machitidwe 4:12.

 Bodza limene amakamba: Mumagaŵanitsa mabanja mwa kuŵaphunzitsa kuti asamakondwelele Khrisimasi.

 Zoona zake: Timasamala kwambili za mabanja, ndipo timaseŵenzetsa mfundo za m’Baibo kuti mabanja akhale olimba.

 Bodza limene amakamba: Mumamanidwa zambili zabwino monga kupatsana zinthu, kukondwela na mtendele, komanso kucitila ena zabwino.

 Zoona zake: Timayesetsa kukhala opatsa komanso amtendele tsiku na tsiku. (Miyambo 11:25; Aroma 12:18) Mwacitsanzo, mmene timacitila misonkhano yathu na mmene timalalikilila, n’zogwilizana na malangizo a Yesu akuti: “Munalandila kwaulele, patsani kwaulele.” (Mateyu 10:8) Cinanso, timakhulupilila kuti ni Ufumu wa Mulungu cabe umene udzabweletsa mtendele weni-weni pa dziko lapansi.—Mateyu 10:7.

N’cifukwa Ciani Mboni za Yehova Sizikondwelela Khrisimasi?

  •   Yesu anatilamula kuti tizikumbukila imfa yake, osati kubadwa kwake.—Luka 22:19, 20.

  •   Atumwi a Yesu na ophunzila ake oyambilila, sanali kukondwelela Khrisimasi. Buku yakuti New Catholic Encyclopedia imati: “Cikondwelelo ca Khrisimasi cinayamba kucitika pambuyo pa caka ca 243 [C.E.],” ndipo pa nthawiyo panali patapita zaka zoposa 100 kucokela pamene mtumwi wothela anamwalila.

  •   Palibe umboni oonetsa kuti Yesu anabadwa pa 25 December. Ndipo m’Baibo mulibe deti yeni-yeni ya tsiku imene anabadwa.

  •   Timakhulupilila kuti Khrisimasi ni yosavomelezedwa na Mulungu cifukwa inacokela ku miyambo yacikunja.—2 Akorinto 6:17.

N’cifukwa ciani kwa Mboni za Yehova kukondwelela Khrisimasi ni nkhani yaikulu?

 Anthu ambili akali kukondwelela Khrisimasi ngakhale kuti amadziŵa kuti ciyambi cake, cinacokela ku miyambo yacikunja ndipo m’Baibo mulibe. Anthu otelo angafunse kuti: N’cifukwa ciani Mboni za Yehova zimaona kuti kukondwelela Khrisimasi ni nkhani yaikulu?

 Baibo imatilimbikitsa kuti tizifufuza zinthu patekha, mwa kuseŵenzetsa “luntha la kuganiza.” (Aroma 12:1, 2) Imatiphunzitsa kuti tifunika kuyamikila coonadi. (Yohane 4:23, 24) Conco, ngakhale kuti timasamala za mmene ena amationela, timayesetsa kutsatila mfundo za m’Baibo olo pamene ambili sayendela mfundo zimenezo.

 Ngakhale kuti sitikondwelela Khrisimasi, timalemekeza ufulu wa munthu aliyense pa zimene angasankhe pa nkhaniyi. Ndipo sitisokoneza ena pamene acita cikondwelelo ca Khrisimasi.