Onani zimene zilipo

Kodi Baibo Anaisintha Kapena Anangoisinthako Zina?

Kodi Baibo Anaisintha Kapena Anangoisinthako Zina?

 Ayi. Tikaona zimene zili m’mipukutu ya kale zikusonyeza kuti Baibo silinasinthidwe, ngakhale kuti kwa zaka masauzande ambili lakhala likukopedwa pa zinthu zimene zimawonongeka m’kupita kwa nthawi.

Kodi izi zitanthauza kuti anthu pokopolola sanali kulakwitsa zina?

 ipukutu ya Baibo masauzande inapezedwa. Ina ya mipukutu imeneyi ni yosiyana, kuonetsa kuti pokopolola anali kulakwitsa zina. Zolakwika zimenezi ni zing’ono-zing’ono ndipo sizisintha tanthauzo la malemba. Komabe, zinapezeka kuti malemba ena anasiyana kwambili, ndipo zioneka kuti anacita zimenezi mwadala n’colinga cofuna kusokoneza uthenga wa m’Baibo. Onani zitsanzo ziŵili izi:

  1.   M’mabaibo ena akale ali na mawu awa pa 1 Yohane 5:7,: “kumwamba kuli Atate, Mawu, komanso Mzukwa Woyela: onsewa ndi mmodzi.” Komabe, m’mipukutu yodalilika imaonetsa kuti mawu amenewa mulibe m’mipukutu yoyambilila. Anacita kuwaikamo pambuyo pake. * Ndiye cifukwa cake m’mabaibo odalilika atsopano anacotsamo mawu amenewa.

  2.   Dzina la Mulungu lipezeka maulendo ambili-mbili m’mipukutu yakale ya Baibo. Ngakhale n’telo, mabaibo ambili acotsa dzina limeneli n’kuikamo maina audindo monga akuti “Ambuye” kapena “Mulungu.”

Kodi tingatsimikize bwanji kuti m’Baibo mulibenso zolakwika zina zambili?

 Pofika pano, pali mipukutu yambili imene inapezeka ndipo zimenezi zathandiza kuti zikhale zosavuta kuzindikila zinthu zomwe n’zolakwika. * Kodi kufananitsa zomwe zili m’mipukutuyi kwaonetsa motani kulondola kwa Baibo?

  •   Pokamba za Malemba Acihebeli (omwe amadziwika kuti “Cipangano Cakale”), katswili wina dzina lake William H. Green anakamba kuti: “Tikhoza kukamba motsimikiza kuti palibenso zinthu zina zakale zimene zinakopololedwa molondola kwambili conco.”

  •   Pokamba za Malemba Acigiliki Acikhristu, kapena kuti “Cipangano Catsopano,” katswili wa Baibo, dzina lake, F. F. Bruce, analemba kuti: “Umboni wotsimikizila kuti zolemba zili mu Cipangano Catsopano n’zazoona ni waukulu kwambili kuposa umboni wa zolemba zina zilizonse zakale. Koma n’zodabwitsa kuti palibe amene amakayikila zolemba zakalezi zomwe zilibe umboni wokwanila.”

  •   Sir Frederic Kenyon, amene ni katswili wodziŵika bwino wa mipukutu ya Baibo, anakamba kuti munthu “akhoza kunyamula Baibo m’manja mwake n’kunena mosaopa kapena kukayikila kuti wanyamula ndi Mawu enieni a Mulungu omwe akhalapo kwa zaka zambili popanda mfundo zofunika kwambili kusokonekela.”

Kodi pali zifukwa zinanso ziti zotipangitsa kutsimikiza kuti Baibo linakopololedwa molondola?

  •   Okopolola Baibo a Ciyuda komanso a Cikhristu, sanacotse nkhani zimene zimaonetsa zophophonya zikulu-zikulu zomwe atumiki a Mulungu anacita. * (Numeri 20:12; 2 Samueli 11:2-4; Agalatiya 2:11-14) Iwo sanacotse mawu odzudzula mtundu wa Ayuda cifukwa cosamvela, komanso mawu ovumbula ziphunzitso zabodza zimene anthu anali kukhazikitsa. (Hoseya 4:2; Malaki 2:8, 9; Mateyu 23:8, 9; 1 Yohane 5:21) Anthu amene anakopolola nkhanizi, anaonetsa kuti anali okhulupilika, komanso anali kulemekeza kwambili Mawu a Mulungu cifukwa anakopolola nkhanizo molondola kwambili.

  •   Kodi si zomveka kukamba kuti Mulungu amene anauzila Baibo, angacite ciliconse kuti lipitilizebe kukhala lolondola? * (Yesaya 40:8; 1 Petulo 1:24, 25) Sikuti anali kufuna kuti Baibo lingothandiza anthu akale, koma iye anali kufuna kuti litithandizenso masiku ano. (1 Akorinto 10:11) Paja, “zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize. Malembawa amatipatsa ciyembekezo cifukwa amatithandiza kupilila ndiponso amatilimbikitsa.”—Aroma 15:4.

  •   Yesu na otsatila ake anali kugwila mawu m’Malemba Acihebeli, ndipo sanakayikile kuti nkhani zakale zimenezo zinali zolondola.—Luka 4:16-21; Machitidwe 17:1-3.

^ ndime 3 Mawu amenewa sapezeka mu mipukutu iyi ya Codex Sinaiticus, the Codex Alexandrinus, the Vatican Manuscript 1209, the original Latin Vulgate, the Philoxenian-Harclean Syriac Version, kapena the Syriac Peshitta.

^ ndime 5 Mwacitsanzo, mipukutu ya Cigiliki yoposa 5,000 imene amati Cipangano Catsopano, kapena kuti Malemba Acigiliki Acikhristu, yapezedwa.

^ ndime 9 Koma Baibo simaonetsa kuti anthu oimilako Mulungu sangalakwitse zinthu. Baibo imati: “Palibe munthu amene sacimwa.”—1 Mafumu 8:46.

^ ndime 10 Baibo imaonetsa kuti ngakhale kuti Mulungu sanali kucita kuuzila olemba Baibo liwu lililonse lolemba, iye anali kutsogolela maganizo a olemba aumunthu amenewo.—2 Timoteyo 3:16, 17; 2 Petulo 1:21.