Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Dzina la Mulungu N’ndani?

Kodi Dzina la Mulungu N’ndani?

Kuti mudziŵane na munthu wina, mosakaikila cinthu coyamba cimene mungacite ni kumufunsa kuti, “Kodi dzina lanu ndimwe ndani?” Ngati mungafunse Mulungu funso limeneli, kodi angayankhe kuti bwanji?

“Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.”Yesaya 42:8.

Kodi dzina limeneli n’lacilendo kwa imwe? Mwina zingakhale conco, cifukwa omasulila Baibo ambili samasulila dzina la Mulungu, ndipo ena saimasulila ngakhale pang’ono. M’malomwake, iwo kaŵili-kaŵili amaikamo dzina laudindo lakuti, “AMBUYE.” Koma dzina la Mulungu limapezeka maulendo pafupi-fupi 7,000 m’mipukutu yonse ya zinenelo zoyambilila za Baibo. Dzina limeneli limaimilidwa na makonsoneti anayi aciheberi a YHWH kapena JHVH. Ndipo nthawi zonse m’Cinyanja imamasulidwa kuti “Yehova.”

Dzina la Mulungu limapezeka m’malemba onse aciheberi komanso m’Mabaibo ena ambili

Mpukutu wa Dead Sea Psalms Scroll M’nthawi ya atumwi, M’CIHEBERI

Baibo ya Tyndale 1530, M’CIZUNGU

Baibo ya Reina-Valera 1602, M’CISIPANISHI

Baibo ya Union Version 1919, M’CICHAINIZI

CIFUKWA CAKE DZINA LA MULUNGU N’LOFUNIKA

Dzina la Mulungu n’lofunika kwa iye mwini. Kulibe anapatsa Mulungu dzina, iye anadzipatsa yekha. Yehova anati: “Limeneli ndilo dzina langa mpaka kalekale, ndipo ndico condikumbukilila ku mibadwomibadwo.” (Ekisodo 3:15) M’Baibo, dzina la Mulungu limapezeka kwambili kuposa maina ake onse audindo, monga Wamphamvuzonse, Atate, Ambuye, kapena Mulungu. Ndiponso kuposa maina ena monga Abulahamu, Mose komanso Yesu. Kuwonjezela apo, n’cifunilo ca Yehova kuti dzina lake lidziŵike. Baibo imati: “Kuti adziŵe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwamba-mwamba pa dziko lonse lapansi.”—Salimo 83:18, nwt-E.

Dzina la Mulungu n’lofunika kwa Yesu. M’pemphelo lodziŵika kuti pemphelo la “Atate wathu wakumwamba” kapena kuti Pemphelo la Ambuye, Yesu anaphunzitsa otsatila ake kupempha Mulungu kuti: “Dzina lanu liyeletsedwe.” (Mateyu 6:9) Yesu iye mwini anapemphela kwa Mulungu kuti: “Atate lemekezani dzina lanu.” (Yohane 12:28) Kwa Yesu, kulemekeza dzina la Mulungu kunali kofunika ngako mu umoyo wake. Pa cifukwa cimeneci, iye anati m’pemphelo: “Ine ndacititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiliza kuwadziwitsa dzinalo.”—Yohane 17:26.

Dzinali n’lofunika kwa amene amam’dziŵa bwino Mulungu. Atumiki a Mulungu akale anadziŵa kuti citetezo na cipulumutso cawo, zinatsamila pa dzina la Mulungu lapadela limenelo. “Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba. Wolungama amathawila mmenemo ndipo amatetezedwa.” (Miyambo 18:10) “Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Yoweli 2:32) Baibo imaonetsa kuti anthu otumikila Mulungu adzadziŵika na dzina lake. “Mtundu uliwonse wa anthu udzayenda m’dzina la mulungu wake. Koma ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.”—Mika 4:5; Machitidwe 15:14.

ZIMENE DZINA LIMENELI LIMATANTHAUZA

Dzina limeneli limadziŵikitsa Mulungu mwapadela. Akatswili a Baibo ambili amavomeleza kuti dzina lakuti Yehova imatanthauza kuti “Iye Amacititsa Kukhala.” Yehova Mulungu anamveketsa tanthauzo la dzina lake pamene anadzifotokoza m’mawu amene anauza Mose kuti: “NDIDZAKHALA AMENE NDIDZAFUNE KUKHALA.” (Ekisodo 3:14) Conco, dzina la Mulungu limatiuza zambili kuposa pa udindo umene ali nawo monga Mlengi, amene anacititsa zinthu zonse kukhalapo. Dzina lake ionetsa kuti Mulungu angadzicititse, kapena kucititsa zinthu zimene analenga kukhala ciliconse pokwanilitsa colinga cake. Maina aulemu amafotokoza udindo wa Mulungu, monga ulamulilo, kapena mphamvu. Koma ni dzina lake cabe lakuti Yehova limene limafotokoza zonse za iye komanso zimene angakhale.

Dzina limeneli limaonetsa kuti Mulungu amasamala za ise. Dzina la Mulungu limatanthauzanso kuti saleka kukonda zolengedwa zake, kuphatikizapo ise anthu. Cinanso, popeza Mulungu wadziŵikitsa dzina lake, zitionetsa kuti afuna tim’dziŵe. Iye ndiye anayamba kutiuza dzina lake, ise tisanayambe kufunsa za dzinalo. Mwacionekele, Mulungu afuna kuti tizimuona monga Mulungu amene tingakhale naye pa ubwenzi, osati monga mulungu wosamvetsetseka bwino-bwino komanso wopanda cikondi.—Salimo 73:28.

Kuseŵenzetsa dzina la Mulungu kumaonetsa kuti timam’konda. Mwacitsanzo, mungauze munthu amene mufuna akhale bwenzi lanu kuti azichula dzina lanu pokuitanani. Kodi mungamvele bwanji ngati nthawi zonse amakana kuseŵenzetsa dzina lanu? M’kupita kwa nthawi, mwina mungayambe kukaikila ngati munthuyo afunadi kukhala bwenzi lanu. N’cimodzi-modzi na Mulungu. Yehova watiuza dzina lake, ndipo amatilimbikitsa kuiseŵenzetsa. Pamene ticita zimenezi, timaonetsa Yehova kuti tifuna kukhala mabwenzi ake. Inde, iye amaona ngakhale ‘anthu amene amaganizila za dzina lake’!—Malaki 3:16

Kudziŵa dzina la Mulungu n’kofunika kwambili kuti tim’dziŵe bwino. Koma apa m’poyambila cabe. Kuti tifike pom’dziŵa bwino mwini wake wa dzinalo, tifunika kumvetsetsa makhalidwe ake.

KODI DZINA LA MULUNGU N’NDANI? Dzina la Mulungu ni Yehova. Dzina limeneli limadziŵikitsa Mulungu mwapadela, kuti ni Mulungu weni-weni amene angakwanilitse colinga cake