Onani zimene zilipo

Kodi Mulungu Ali na Maina Angati?

Kodi Mulungu Ali na Maina Angati?

Yankho la m’Baibo

 Mulungu ali na dzina limodzi cabe laumwini. M’Cihebeli limalembedwa conco יהוה, ndipo m’cinyanja limalembedwa kuti “Yehova.”  * Kupitila mwa mneneli wake Yesaya, Mulungu anati: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.” (Yesaya 42:8) Dzina limeneli limapezeka maulendo pafupifupi 7,000 m’mipukutu yakale ya Baibo. Komanso ndiyo ipezeka kwambili kuposa mawu ena alionse okamba za Mulungu, kapena dzina la munthu wina aliyense. *

Kodi Yehova ali na maina ena?

 Ngakhale kuti Baibo imakamba kuti Mulungu ali na dzina laumwini limodzi cabe, imaseŵenzetsanso maina ake ena audindo, kapena yofotokoza za iye. Mndandanda otsatilawu wa maina ena audindo, komanso mawu ofotokoza za iye, ukusonyeza mmene dzina lililonse limaonetsela mmene Yehova alili, komanso umunthu wake.

Dzina laudindo

Lifalensi

Tanthauzo

Allah

(Palibe)

Mawu akuti “Allah” si dzina lenileni la Mulungu, koma ni dzina laudindo la Ciarabu omwe amatanthauza kuti “Mulungu.” Ma Baibo a m’Ciarabu, komanso zinenelo zina amagwilitsa nchito mawu akuti “Allah” kutanthauza “Mulungu.”

Wamphamvuzonse

Genesis 17:1

Ali na mphamvu zimene palibe wina aliyense angalimbane nazo. Mawu a Cihebeli akuti ʼEl Shad·daiʹ amatanthauza kuti “Mulungu Wamphamvuyonse” ndipo m’Baibo amapezeka maulendo okwana 7.

Alefa ndi Omega

Chivumbulutso 1:8; 21:6; 22:13

Mawu amenewa amatanthauza kuti “woyamba ndi wotsiliza” kapena kuti “ciyambi ndi mapeto.” Kutanthauza kuti panalibe Mulungu Wamphamvuzonse Yehova asanakhaleko, ndipo sipadzakhalanso wina pambuyo pake. (Yesaya 43:10) Alefa ni cilembo coyamba, ndipo omega ndi cilembo comaliza mu alifabeti ya Cigiliki.

Wamasiku Ambili

Danieli 7:9, 13, 2

Mulungu alibe ciyambi. Iye wakhala alipo kuyambila kalekale munthu aliyense, komanso cinthu ciliconse cisanakhaleko.—Salimo 90:2.

Mlengi

Yesaya 40:28

Ndiye analenga zinthu zonse.

Atate

Mateyu 6:9

Wopatsa moyo.

Mulungu

Genesis 1:1

Woyenela kulambilidwa; wamphamvu kwambili. Mawu a Cihebeli akuti ʼElo·himʹ amanena za zinthu zambili osati cimodzi, ndipo izi zimaonetsa ukulu, ulemelelo, komanso ubwino wa Yehova.

Mulungu wa milungu

Deuteronomo 10:17

Mosiyana na “milungu yopanda phindu” imene anthu ena amailambila, Mulungu ni wapamwamba kwambili.—Yesaya 2:8.

Mlangizi Wamkulu

Yesaya 30:20, 21

Iye amatiphunzitsa na kutipatsa malangizo anzelu.—Yesaya 48:17, 18.

Wopanga Wamkulu

Salimo 149:2

Ndiye anacititsa kuti zonse zikhalepo.—Chivumbulutso 4:11.

Mulungu Wacimwemwe

1 Timoteyo 1:11

Ni Mulungu wacisangalalo komanso wa cimwemwe—Salimo 104:31.

Wakumva pemphelo

Salimo 65:2

Amamvela pemphelo lililonse lopelekedwa mwa cikhulupililo.

Ine Ndine Yemwe Ndili Ine

Ekisodo 3:14, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu

Amakhala ciliconse cimene afuna kuti akwanilitse cifunilo cake. Mawu amenewa anawamasulilanso kuti “Ndidzakhala ciliconse cimene ndikufuna” kapena kuti “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.” (The Emphasised Bible, lolembedwa na J. B. Rotherham, komanso Baibulo la Dziko Latsopano) Zimenezi zimathandiza kufotokoza tanthauzo la dzina la Mulungu lakuti, Yehova, limene lili mu vesi lotsatila.—Ekisodo 3:15.

Wansanje

Ekisodo 34:14, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu

Amafuna kuti tizilambila iye yekha. Mawu amenewa anamasulidwanso kuti “safuna kuti aliyense azipikisana naye,” kapena kuti “amene amafuna kuti anthu azidzipeleka kwa iye yekha.”—Baibulo la Mawu a Mulungu, komanso Baibulo la Dziko Latsopano.

Mfumu yamuyaya

Chivumbulutso 15:3

Ulamulilo wake ulibe ciyambi, kapena mapeto.

Ambuye

Salimo 135:5

Mwini wake kapena kuti ambuye; M’Cihebeli ni ʼA·dhohnʹ komanso ʼAdho·nimʹ.

Yehova Wamakamu, Ambuye Wamakamu

Yesaya 1:9, Aroma 9:29, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu

Ndiye mtsogoleli wa khamu lalikulu la angelo. Dzina la udindo lakuti “Ambuye Wamakamu” lingamasulidwenso kuti “Yehova Wamakamu” kapena “Mbuye wa magulu a nkhondo akumwamba.”—Aroma 9:29, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Wam’mwambamwamba

Salimo 47:2

Ndiye wamkulu m’cilengedwe conse.

Woyela Koposa

Miyambo 9:10

Iye ni woyela mu zonse kuposa munthu wina aliyense.

Woumba

Yesaya 64:8

Ali na ulamulilo pa anthu, komanso mitundu yonse monga mmene woumba mbiya alili na ulamulilo pa dongo.—Aroma 9:20, 21.

Wowombola

Yesaya 41:14

Amawombola kapena kugulanso anthu ku ucimo ndi imfa pogwilitsa nchito nsembe ya dipo ya Yesu Khristu.—Yohane 3:16.

Thanthwe

Salimo 18:2, 46

Ndiye malo acitetezo komanso cipulumutso.

Mpulumutsi

Yesaya 45:21

Amateteza anthu ku zinthu zowononga.

Mbusa

Salimo 23:1

Amasamalila alambili ake.

Ambuye Wamkulu Koposa

Genesis 15:2

Ndiye wolamulila wamkulu kuposa onse; Ndipo m’Cihebeli amati ʼAdho·naiʹ.

Wamkulukulu

Danieli 7:18, 27

Yehova ndi wolamulila wamkulu m’cilengedwe conse.

Maina a Malo M’malemba Acihebeli

 Maina ena a malo ochulidwa m’Baibo ali na dzina la Mulungu lakuti Yehova, koma sikuti maina amenewa ndiye maina ena a Mulungu.

Dzina la malo

Lifalensi

Tanthauzo

Yehova-yire

Genesis 22:13, 14

“Yehova Adzapeleka Zofunika.”

Yehova-nisi

Ekisodo 17:15

“Yehova Ndiye Mlongoti Womwe Ndi Cizindikilo Canga,” kapena “Mbendela yanga.” (Baibo la Today’s New International Version) Yehova ni Mulungu amene anthu omwe amam’tumikila angadalile kuti awateteze, komanso kuwathandiza.—Ekisodo 17:13-16.

Yehova-salomu

Oweruza 6:23, 24

“Yehova Ndi Mtendele.”

Yehova-sama

Ezekieli 48:35, American Standard Version, mawu am’munsi

“Yehova Ali Kumeneko.”

N’cifukwa ciyani tiyenela kudziŵa, komanso kugwilitsa nchito dzina la Mulungu?

  •   Mulungu amaona kuti dzina lake lakuti, Yehova, ni lofunika kwambili, ndipo n’cifukwa cake ipezeka m’Baibo maulendo ambili.—Malaki 1:11.

  •   Mobwelezabweleza, Yesu Mwana wa Mulungu, anagogomeza za kufunika kwa dzina la Mulungu. Mwacitsanzo, iye anapemphela kwa Yehova kuti: “Dzina lanu liyeletsedwe.”—Mateyu 6:9; Yohane 17:6.

  •   Anthu amene amadziŵa, komanso kuseŵenzetsa dzina la Mulungu, amakhala akucita zinthu zoyenela zomwe zingawathandize kukhala paubale na Yehova. (Salimo 9:10; Malaki 3:16) Ndipo ubale wawo umenewu na Mulungu umacititsa kuti apindule na lonjezo lake lakuti: “Popeza wasonyeza kuti amandikonda, Inenso ndidzamupulumutsa. Ndidzamuteteza cifukwa wadziŵa dzina langa.”Salimo 91:14.

  •   Baibo imati: “Ilipo yochedwa milungu, kaya kumwamba kapena padziko lapansi, ndipo n’zoona ilipodi ‘milungu’ yambili ndi ‘ambuye’ ambili.” (1 Akorinto 8:5, 6) Komabe Baibo imaonetsa Mulungu mmodzi woona mwa dzina lake lakuti, Yehova.—Salimo 83:18.

^ ndime 1 Akatswili ena a Cihebeli amaona kuti kuli bwino kuseŵenzetsa “Yahweh” monga dzina la Mulungu.

^ ndime 1 Cidule cake ca dzina la Mulungu ni, “Ya,” imene ipezeka maulendo 50 mu Baibo, kuphatikizapo mawu akuti “Aleluya,” amene atanthauza kuti “Tamandani Ya.”—Chivumbulutso 19:1; Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.