Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yochotsa Mimba?

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yochotsa Mimba?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo siligwiritsa ntchito mawu akuti “kuchotsa mimba” ponena za kupha mwana wosabadwa. Komabe lili ndi mavesi ambiri osonyeza mmene Mulungu amaonera moyo wa munthu, kuphatikizapo wa mwana amene ali m’mimba mwa mayi ake.

 Moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. (Genesis 9:6; Salimo 36:9) Iye amaona kuti moyo wa chinthu chilichonse ndi wamtengo wapatali, kuphatikizapo moyo wa mwana yemwe adakali m’mimba mwa mayi ake. Choncho kupha mwana wosabadwa mwadala, n’chimodzimodzi ndi kupha munthu.

 Malamulo amene Mulungu anapatsa Aisiraeli ankanena kuti: “Amuna akamamenyana ndipo avulaza kwambiri mkazi wapakati moti mkaziyo n’kubereka mwana koma palibe amene wamwalira, wovulaza mkaziyo azimulipiritsa ndithu malinga ndi zimene mwiniwake wa mkaziyo angagamule. Azikapereka malipirowo kudzera mwa oweruza. Ngati wina wamwalira, pamenepo uzipereka moyo kulipira moyo.”—Ekisodo 21:22, 23. a

 Kodi moyo wa munthu umayamba liti?

 Mulungu amaona kuti moyo wa mwana umayamba mayi akangotenga pakati. M’Baibulo, Mulungu amasonyeza mobwerezabwereza kuti mwana amene sanabadwe ndi munthunso payekha. Taganizirani zitsanzo zotsatirazi, zomwe zikusonyeza kuti Mulungu amaona kuti palibe kusiyana pakati pa moyo wa mwana yemwe ali m’mimba ndi mwana yemwe wabadwa kale.

  •   Mothandizidwa ndi mzimu woyera, Mfumu Davide anauza Mulungu kuti: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza.” (Salimo 139:16) Mulungu ankadziwa kuti Davide ndi munthu ngakhale pamene anali asanabadwe.

  •   Komanso Mulungu anadziwiratu kuti mneneri Yeremiya adzakhala ndi udindo wapadera, Yeremiyayo asanabadwe. Mulungu anamuuza kuti: “Ndisanakuumbe m’mimba, ndinakudziwa, ndipo usanatuluke m’mimbamo, ndinakusankha kuti uchite ntchito yopatulika. Ndinakusankha kuti ukhale mneneri ku mitundu ya anthu.”—Yeremiya 1:5.

  •   Luka yemwe analemba nawo Baibulo komanso anali dokotala, anagwiritsa ntchito mawu a Chigiriki akuti “khanda” ponena za mwana yemwe sanabadwe komanso ponena za mwana wobadwa kumene.—Luka 1:41; 2:12, 16.

 Kodi Mulungu angakhululukire munthu amene anachotsapo mimba?

 Inde. Mulungu akhoza kukhululukira anthu amene anachotsapo mimba. Ndipo ngati anasintha n’kumaona moyo mmene Mulungu amauonera, sayenera kumadziimbabe mlandu. Paja Baibulo limanena kuti: “Yehova ndi wachifundo ndi wachisomo . . . Monga mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo, momwemonso, watiikira kutali zolakwa zathu.” b (Salimo 103:8-12) Yehova amakhululukira anthu onse omwe anachitapo tchimo, kuphatikizapo kuchotsa mimba ngati alapa kuchokera pansi pa mtima.—Salimo 86:5.

 Kodi n’kulakwa kuchotsa mimba ngati moyo wa mayi kapena wa mwana uli pangozi?

 Mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena pa nkhani ya mwana yemwe sanabadwe, kungakhale kulakwa kwakukulu ngati mayi atachotsa mimba chifukwa choti wauzidwa kuti moyo wake kapena wa mwanayo ukhala pangozi.

 Nanga bwanji ngati pa nthawi yobereka papezeka mavuto ena omwe zivute zitani mukufunika musankhe pakati pa kupulumutsa moyo wa mayi kapena wa mwana? Zikatere, aliyense ayenera kusankha yekha kuti apulumutsa moyo wake kapena wa mwanayo.

a Mabaibulo ena amamasulira lamuloli m’njira yoti zizioneka ngati chofunika kwambiri chinali moyo wa mayiyo, osati moyo wa mwana wosabadwayo. Koma m’Chiheberi, lembali limanena za kuphedwa kwa onse, mayi kapena mwana.

b Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.—Salimo 83:18.